Chikondwerero Pakati pa Anthu a Mulungu
MAU a Mfumu Davide, olembedwa pa Salmo 68, maversi 2-4, amaphatikizamo mau oitana onse okonda ufulu weni weni: “Yimbani kwa Mulungu, liyimbireni nyimbo dzina lake; undirani mseu lye woberekekayo kuchidikha monga Yehova limene liri dzina lache; ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pache.” Ndi mwai wokulira wotani umene ungakhalepo koposa kutumpha ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu wathu? (Yesaya 12:2, 3) Mkati monse mwa chaka cha 1986, Yehova wadyetsa mboni zake mochititsa chidwi pamene izo zinapitirizabe kulalikira ufulu kwa anthu a padziko lapansi.
Masamba otsatirawa akupereka chidule cha ntchito za Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse lapansi mkati mwa 1986. Chiri chifukwa chabwino chotani nanga chakukondwerera! Monga momwe ziwerengero ziri kusonyezera, chiwerengero chapamwamba cha Mboni zokangalika m’maiko 208 ochita ripoti chinaonjezeka kufika ku 3, 229, 022, kuonjezeka ndi 6.8-peresenti mkati mwa chaka. Chiwerengero cha obatizidwa chinali 225, 868.
Kukumbukira Imfa ya Yesu
Chiwerengero cha opezekapo pa kukumana kofunika kwambiri kwa chaka, Chikumbutso cha imfa ya Yesu, chinakwera kufika ku chifupifupi 8, 160, 597, angakhale kuti maripoti ena sanalandiridwe chifukwa cha kuipa kwa mikhalidwe ya m’dziko. Chiwerengero chaogawanako ku ziphiphiritso za Chikumbutso chinachepa kufika ku 8, 927 popeza odzozedwa achikulire anamaliza utumiki wao pa dziko lapansi.—Chivumbulutso 2:10.
Ambiri a awo amene anasonkhana m’kumvera ku lamulo la Yesu anasonyeza kulimba mtima kwa chitsanzo. (1 Akorinto 11:23-26; Yohane 16:33) M’dziko lina la mu Africa kumene ntchito ya Yehova iri yotsekedwa, mpingo unasonkhana pa nyumba ya mlongo wina kukumbukira Chikumbutso. Patangopita mphindi zisanu ndi zitatu mkati mwa nkhani, olamulira akumaloko anaturukira kudzagwira abalewo. Iwo analamula abalewo kuimitsa msonkhano. Abalewo mwa chifundo koma molimbika anaumilira kuti iwo akanayenera kupereka ulemu ku Chikumbutso cha imfa yopereka nsembe ya Yesu. Pambuyo pa kulingalira ndi kuchonderera ndi apolisi, iwo analoledwa kupitiriza m’kumvetsera kwa maofisala. Msonkhano unamalizidwa mwamtendere, ndipo kenaka onse anagwidwa. Pambuyo pa nyengo ya kufunsidwa, asanu anasungidwa. Iwo anakhala m’ndende kwa kanthawi koma kenaka anamasulidwa, achimwemwe kotero kuti anakhoza kukumbukira Mgonero wa Ambuye!—1 Yohane 5:3, 4.
Mu Nigeria, komwe chiwerengero cha Mboni chaonjezeka kufika ku 128, 461, anali ndi chiwerengero cha opezekapo pa Chikumbutso cha 394, 370—chiwerengero chapamwamba koposa kuyambira ndi kale lonse. Msonkhano wa Chikumbutso wina unapangidwa pa malo pamene akumanga nyumba ya Betele yatsopano pa Igieduma, ndipo oposa 700—chifupifupi mudzi wonse wa kumeneko—anapezekapo.
Kuchokera ku Mexico kwabwera ripoti: “Kuli konse komwe tingapite m’dziko ofalitsa akungopezeka pali ponse ndi chimwemwe, ndipo dziko lonse liri kuoneka liri pa moto ndi chowonadi. Chowonadi chawakuta abale, ndipo miyoyo yawo imazungulira pa chowonadi. Mabanja onse akubwera ku chowonadi. Peresenti yabwino ya anthu omwe amaphunzira amayamba kufika ku misonkhano pa nthawi imodzimodziyo. Ichi chimathandiza iwo kupanga kupita patsogolo kofulumira.” Mexico inachitira ripoti chiwerengero chaopezeka pa Chikumbutso cha 838, 467. Mu August ofalitsa a Ufumu 198, 003 m’dziko limenelo anali kutsogoza maphunziro a Baibulo okwanira 327, 664 m’nyumba za anthu. Ha ndi chiyembekezo chotani chomwe anali nacho kaamba ka kuonjezeka kopitirizabe!
Kufutukuka Koonjezeka kwa Dziko Lonse
Kuchokera pa mtima pa Chipembedzo cha dziko kwafika maripoti ofananawo akufutukuka. Italy anachifikira chiwerengero chatsopano chapamwamba cha ofalitsa cha 139, 570 mu August. Ndipo 301, 009 anapezekapo kaamba ka Chikumbukiro cha Mgonero wa Ambuye. Mboni za Yehova kwenikwenidi ‘zikulola kuwala kwao kuwala pamaso pa anthu.’ (Mateyu 5:16) Mwachitsanzo: “Mlongo anali kuika ndalama mu makina ogulira matiketi a basi pamene mnzake anamuuza iye kuti panalibe chifukwa cha kulipilira kaamba ka tiketi popeza anayenera kukwera basi kwa kanthawi kochepa. Mlongoyo analongosola kuti chinali choyenera kulipira kaamba ka tiketi, angakhale kaamba ka ulendo wa malo oima amodzi. Pambuyo pachimenechi, mnzakeyo anatsika m’basi. Pa nsongayi, woyendetsa basi anatembenukira kwa iye ndi kunena: ‘Kodi uli m’modzi wa Mboni za Yehova?’ ‘Inde,’ anayankha motero mlongoyo, ‘ndi chiyani chakupanga kufunsa tero?’ ‘Ndinamva kukambitsirana kwanu ponena za kulipira tiketi ya basi, ndipo ndinadziwa kuti Mboni za Yehova ziri pakati pa anthu ochepa kwambiri omwe amachita choncho ndipo ali oona mtima m’zinthu zonse.’ Miyezi yochepera pambuyo pake, mwamuna wina anamufikira mlongoyo pa msonkhano ndi kuti: ‘Kodi undidziwa ine? Ndiri woyendetsa basi yemwe analankhula kwa iwe ponena za kulipira kaamba ka tiketi. Nditayang’anitsitsa mikhalidwe yanu, ndinalingalira za kuyamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.’”
Britain anali ndi chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa a Ufumu cha 107, 767, kuphatikizapo mbale wobatizidwa posachedwa uyu: “George tsopano ali ndi zaka 84 zakubadwa. Pambuyo pa zaka 50 monga wolalikira m’matchalitchi a kumaloko, iye anafika ku chidziwitso cha chowonadi. Poyambilira, pamene iye amaliza phunziro lake la Baibulo, anayenera kuthamangira ku chipinda china ndi kukasuta ndudu. Iye wakhala wosuta ndudu wokhazikika kwa zaka 70. Koma pambuyo pakuphunzira mutu 26 wa bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, iye sanasutenso kachiwiri. George tsopano wakhala wobatizidwa koposa chaka chimodzi ndipo ali wachangu kwambiri mu utumiki wa m’munda, kuwauza ena ponena za madalitso amene Yehova adzabweretsa m’dongosolo Lake lazinthu latsopano.”
Federal Republic ya Germany ikuchitira ripoti chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa 118, 645. Kulinso makumi zikwi za mboni zokhulupirika ‘kulola kuwala kwawo kuwala’ m’dziko loyandikana nawo la Germany Democratic Republic. Mu Germany okhulupirika akale salola kuika pansi “lupanga lawo la mzimu.” (Aefeso 6:16, 17) Mpingo ukupangira ripoti kuti: “Tiri ndi mlongo yemwe ali ndi zaka 103 zakubadwa ndipo amakhalabe yekha. Akulu anakonza kaamba ka gulu la alongo asanu ndi awiri kufika ku asanu ndi atatu kutenga mbali m’kumusamalira iye mlungu ulionse. Iwo akhala akuchita chimenechi kwa zaka zapita zitatu kufika zinayi. Antchito osamalira anthu, omwe amalipiridwa ndi boma, amabwera kudzasamalira kaamba ka kusambitsa ndi kusintha zovala. Koma pamene iwo akudwala kapena ali patchuthi, alongo athu amatenga ntchitoyo. Chizindikiritso cha chikondi cha Chikristu chimenechi ndi kudzipereka kwa kutumikira kwatumikira monga umboni wabwino kwa anthu akunja. Mlongo wathu wa zaka 103 zakubadwa ali wogalamuka m’maganizo ndipo amawalingalira antchito osamalira anthu kukhala ‘gawo lake.’ Iye amalalikira kwa iwo mwachangu pamene ali kumusambitsa iye ndi kuwapatsa iwo mabuku.” Moonadi, “imvi ndiyo korona waulemu pamene ipeza njira ya chilungamo.”—Miyambo 16:31.
Komabe, chiitano cha kulemekeza Yehova chikupita kwa anthu a zaka zosiyanasiyana—“anyamata ndiponso anamwali, okalamba pamodzi ndi ana.” Anthu achichepere ambiri ‘akukumbukira Mlengi wawo m’masiku aunyamata wawo.’ (Salmo 148:12; Mlaliki 12:1) Mu Brazil, kumene kunali chiwerengero chapamwamba chosangalatsa kwambiri cha ofalitsa 196, 948, Watch Tower Society inalandira kalata yochokera ku tauni yakutali kumene abale awiri achichepere akhala akuchitira umboni kwa miyezi ingapo. Iyo inatero ku mbali ina: “Ndingakonde kukuyamikirani kaamba ka achichepere abwino amene muli nawo mu chipembedzo chanu. Ine ndiri mphunzitsi wa pa sukulu ndipo mochulukira ndimachita ndi achichepere, ndipo ndimadziwa kuti iwo sali monga momwe analiri poyamba. Achichepere anu ali kwenikwenidi chitsanzo. Iwo amalemekeza akulu awo, ali aulemu ndipo amavala moyenerera. Ndipo m’mene amadziwira ma Baibulo awo! Chimenecho moonadi chiri chipembedzo! Chiri chomvetsa chisoni kuti iwo akayenera kuchoka.” Mabanja a abale athu akupita tsopano kukakhazikika kotheratu ku ena amalo okhala kutali oterewa kukatenga chikondwerero.
Kodi ndi kupita patsogolo kwa mtundu wanji kumene chowonadi chikupanga ku maiko opanda Chikristu? The Wall Street Journal ya July 9, 1986, inalemba nkhani yaitali pansi pa mutu waukulu wakuti “Dziko Losabala—Amishonare Achikristu Anadzala Mbeu mu Japani Koma Anapeza Zochepa Zikumera.” M’mishonare wa United Church of Christ anachitira ripoti akunena kuti, “Palibe njira ina iri yonse yonena kuti Chikristu kwenikweni chidzazika mizu mu Japani,” ndipo wansembe wa chiFranciscana ananena kuti, “Tsiku la m’mishonare wa kunja mu Japani latha.” Onse awiri anagwira ntchito kopanda phindu kwa zaka zoposa 30. Nkhaniyo inanena kuti: “Yochepa ndi 1 peresenti ya anthu onse m’dzikomo ali Akristu, ndipo mosasamala kathu za ntchito yonse ya umishonare, peresentiyo yakhala iri kutsika.” Zochuluka kwambiri kaamba ka zipembedzo za Chikristu cha Dziko! Koma bwanji ponena za Mboni za Yehova, zimene zimaphunzitsa Chikristu changwiro m’dziko limenelo? Kwa miyezi 92 yapita yotsatizana, iwo aonjezera chiwerengero cha maminisitala awo okangalika kufika ku chiwerengero chapamwamba cha 113, 062 (kuphatikizapo avereji ya apainiya 46, 390 mwezi uli onse). Mu Japani maphunziro a Baibulo apanyumba 146, 316 akutsogozedwa kwa anthu okondwerera chatsopano. Ichi moonadi chiri chitsogozo cha kuonjezeka kokulira. Pano, tikuona kukwaniritsidwa kwenikweni kwa Yesaya 65:13, 14.
Munda wa Upainiya
Bwanji ponena za pakati penipeni pa ntchito yonka mtsogolo imeneyi—United States of America? Kumeneko, ofalitsa a Ufumu 744, 919 anali m’munda monga chiwerengero chapamwamba. Koma kodi ‘amishonare apanyumba amenewa’ ali ofunikiradi? Moonadi iwo ali, popeza upandu, mankhwala oledzeletsa, kuipa, matenda, ndi chivundi zakwera kufika ku mlingo woipitsitsa kwenikweni kusiyana ndi m’maiko ena otchedwa osapembedza. Anthu akufuna zinthu zabwinopo kaamba ka chitonthozo ndi chiyembekezo, ndipo Mboni za Yehova ziri ndi uthenga woterowo. (Yesaya 61: 1, 2; Mateyu 24:14) Mu United States, mkati mwa 1986, aminisitala amenewa anapereka maora okwanira 146, 673, 490 kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu. Icho chinafika kuchiwerengero cha peresenti yoonjezereka ya 12. 6, kapena maora okwanira 16, 449, 229 kuposa chaka chapita. Nthawi imeneyo inaonongedwa mopindulitsa, popeza mabuku okwanira 6, 138, 938 anagawiridwa, komwe kuli kuongokera kwa 23. 2 peresenti kuposa chaka chapita. Mu April mokha, chionkhetsocho chinali choposa mabuku 1, 000, 000 olongosola za chiyembekezo chenicheni kaamba ka mtendere ndi chisungiko.
Mbali imodzi yosangalatsa kwambiri ponena za ripoti la United States ndiyo kupita patsogolo kwa utumiki wa upainiya. Mu April panali chiwerengero chapamwamba cha apainiya okhazikika 45, 786, kuonjezeka ndi 23 peresenti kuposa chaka chapita. Pamene muphatikiza chiwerengero chimenecho ndi avereji ya apainiya othandizira ya 43, 369 ndi avereji ya apainiya apadera 279, chimatanthauza kuti mwezi uli wonse chifupifupi 90, 000 ali kubukitsa Ufumu wa Mulungu m’mathayo antchito ya upainiya. Amenewa ali achichepere ndipo achikulire, nawonso, omwe mwa nzeru akugwiritsira nthawi yawo mkulemekeza Yehova.
Kupereka Umboni Wokwanira
Mukuphunzitsa m’mabwalo ndi m’nyumba ndi nyumba, Mtumwi Paulo “anachitira umboni” ku mbiri yabwino. (Machitidwe 20:20, 21) Umboni wofananawo ukuperekedwa mu magawo ochuluka lerolino. Mwachitsanzo ripoti iri lachokera ku Guadeloupe: “Pofika kumapeto kwa chaka chautumiki, tinali ndi ofalitsa m’modzi kaamba ka anthu 72. Sichikufunika kunenedwa kuti, tiri anthu odziwika koposa kuzungulira m’dziko lonse! M’chenicheni, m’malo ambiri, timapita ku gawo limodzimodzilo mlungu uli wonse. Ena anganene kuti kwenikwenidi anthu atopetsedwa ndi kutiona, kapena kuti ali magwero akufooketsa kukhala m’gawo limodzimodzilo mlungu ndi mlungu. Koma mosiyana, pamene mochulukira timagwirira ntchito m’gawolo, chikondwerero chochulukira chimadzutsidwa. Ndipo choturukapo? Chabwino, chiri chiwerengero chapamwamba mu April wapita cha maphunziro a Baibulo a panyumba 7, 136 otsogozedwa ndi ofalitsa athu 4, 558! Posachedwapa magazini inatuluka yokhala ndi mutu wakuti: ‘Mboni za Yehova—Mafumu Ku Khomo ndi Khomo’! Tikuchilingalira icho kukhala ulemu. Mkati mwa chaka cha utumiki, abale ndi alongo atsopano 458 anabatizidwa.” Kukhazikika ndi chisangalalo zinasonyezedwa m’kugwira ntchito mu magawo athu mobwerezabwereza, kudziwa ndi kukhala mabwenzi a anthu, mwachikondi kuphwanya kunyaen kwawo—ichi chingatsogoze ku kupeza ambiri onga nkhosa.
Yehova molemera akudalitsa atumiki ache m’dziko la mu Afirika kumene ntchito iri yoletsedwa ndi ukali wa nkhondo. M’dziko limenelo ambiri a abale athu akuvutika m’ndende, ndipo Mboni zina zachichepere zakhala zikumaphedwa. Komabe, April inawona ripoti lapamwamba kwambiri, lokhala ndi chiwerengero chapamwamba cha khumi cha nthawi zonse. Chiwerengero chatsopano cha ofalitsa chiri choonjezereka ndi 29 peresenti kuposa chaka chapita. Ndi changu cha mtundu wotani nanga chomwe abale okondedwa amenewa ali kuchisonyeza! Avereji ya maora mu April inali yoposa 18 pa wofalitsa aliyense, ndipo maphunziro a Baibulo a panyumba anali 2. 6 pa wofalitsa aliyense.
Uthenga wachinsinsi wolandiridwa ndi ofesi ya nthambi imene ikusamalira gawo limeneli uli wokwanira kupereka malingaliro ponena za mikhalidwe ya kumaloko. Iyo ikunena motere: “Kutentha kukupitirizabe kumenya pa ife. Kuyesayesa kofunikira kuyenda mozungulira ndi kuona wina wake chiri chitsimikiziro chakuti tikukhala ndi mafunde otentha. Koma tikudziwa kuti tinapangidwa mwa mtundu wotero kotero kuti tingathe kuzolowerana ndi mtundu uli wonse wa kutentha ndi mtundu uli wonse wa mikhalidwe. Mosasamala kathu za chiri chonse, timapirira ndi kukhulupirira kuti tidzapulumuka.” Umphumphu wotero!
Osunga umphumphu a umwini amapanga gulu losunga umphumphu. Gulu la dziko lonse la Mboni za Yehova zokwanira 3, 229, 022 liri limenelo! Iwo amayang’ana kutsogolo ku kupulumuka “chisautso chachikulu” chikudzacho ndi kugawana pansi pa Ufumu wa Kristu, mu ntchito yaikulu yakulisintha dziko kukhala paradaiso. (Chivumbulutso 7:14; 21:3, 4; Yesaya 65:17, 21-23, 25) Iwo amakondwera ndi njira m’mene Yehova angakhale tsopano akudalitsira ntchito yawo ya changu, mosasamala kathu kuti kaya akulalikira mau “mnyengo yabwino” kapena “mnyengo yobvuta.” (2 Timoteo 4:2) Masamba otsatirawa akusonyeza m’mene iwo avomerezera ku mutu wa lemba la chaka la 1986: “Pita . . . , nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.”—Luka 9:60.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]
Mbali Zina za Ripoti la Dziko Lonse la Mboni za Yehova
Kuonjezeka:
Chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa: 3. 229, 022 6. 8%
Avereji ya Mwezi ndi mwezi ya apainiya: 391, 294 21. 2%
Chionkhetsocha maora aulaliki: 680, 837, 042 15. 3%
Avereji ya mwezi ndi mwezi ya maphunziro a Baibulo apanyumba: 2, 726, 252 14. 6%
Chionkhetso chonse chaobatizidwa mu 1986: 225, 868 19%
[Tchati on page 10-13]
RIPOTI LAUTUMIKI LA CHAKA CHA 1986 LA MBONI ZA YEHOVA DZIKO LONSE
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
[Chithunzi patsamba 8, 9]
KUCHITIRA UMBONI “KUBWALO NDI KU NYUMBA NDI NYUMBA”
Davao Philippines
Venice Italy
Castle Combe England
Gålå Norway
Kowloon Hong Kong
Taipei Taiwan
Queenstown New Zealand
Bolgatanga Ghana
Paris France
Quetzaltenango Guatemala
Kerala India
Banff Canada