PHUNZIRO 24
Kodi Angelo Ndi Ndani, Nanga Amachita Zotani?
Yehova amafuna kuti tidziwe zokhudza banja lake lakumwamba. M’banja limeneli mulinso angelo, omwe amatchedwa “ana . . . a Mulungu.” (Yobu 38:7) Kodi Baibulo limanena zotani zokhudza angelo? Kodi zimene angelo amachita zimakhudza bwanji anthu? Kodi angelo onse ali m’banja la Mulungu?
1. Kodi angelo ndi ndani?
Asanalenge dziko lapansi, Yehova analenga angelo. Mofanana ndi Mulungu, angelo saoneka ndipo amakhala kumwamba. (Aheberi 1:14) Angelo alipo mamiliyoni ambirimbiri ndipo mngelo wina aliyense ndi wosiyana ndi mnzake. (Chivumbulutso 5:11) Iwo “amamvera mawu ake [a Yehova] komanso kuchita zimene wanena.” (Salimo 103:20) Kale, nthawi zina Yehova ankatumiza angelo padziko lapansi kuti adzapereke mauthenga, adzathandize anthu ake komanso kuwapulumutsa. Masiku ano angelo amatsogolera Akhristu kuti akalalikire kwa anthu amene akufuna kudziwa za Mulungu.
2. Kodi Satana komanso ziwanda zake ndi ndani?
Angelo ena anasankha kusiya kumvera Yehova. Mngelo amene anayambirira kuchita zimenezi ndi amene amatchedwa kuti “Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Satana ankafuna kuti azilamulira ena, choncho anapusitsa Adamu ndi Hava ndipo kenako anadzapusitsanso angelo ena kuti asiye kumvera Mulungu. Angelo amene anasankha kupandukira Mulunguwa amatchedwa ziwanda. Popeza kuti angelowa anali kumwamba, Yehova anawathamangitsira padziko lapansi ndipo posachedwapa awonongedwa.—Werengani Chivumbulutso 12:9, 12.
3. Kodi Satana ndi ziwanda zake amapusitsa bwanji anthu?
Satana ndi ziwanda zake amapusitsa anthu ambiri kuti azikhulupirira zamizimu. Anthu amene amakhulupirira zamizimu amalankhulana ndi ziwanda ndipo kuchita zimenezi ndi koopsa kwambiri. Mwachitsanzo, anthu ena akakhala ndi vuto amapita kukakumana ndi okhulupirira nyenyezi, olosera zam’tsogolo, anthu amene amatha kudziwa zimene ena akuganiza komanso asing’anga. Anthu ena akadwala amakatenga mankhwala omwe amafuna kuti achitenso zinthu zina zokhudzana ndi kukhulupirira zamizimu. Satana ndi ziwanda zake amapusitsanso anthu kuti azikhulupirira zoti akhoza kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. Koma Yehova amatichenjeza kuti: “Musamapemphe anthu olankhula ndi mizimu kuti akuthandizeni ndipo musamafunse malangizo kwa anthu olosera zam’tsogolo.” (Levitiko 19:31) Iye amatiuza zimenezi chifukwa amafuna kutiteteza kwa Satana komanso ziwanda zake, omwe ndi adani a Mulungu ndipo amafuna kutipweteka.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti muone zinthu zabwino zimene angelo amachita, kuopsa kokhulupirira mizimu komanso zimene tingachite kuti tidziteteze kwa Satana ndi ziwanda zake.
4. Angelo amathandiza anthu kuphunzira zokhudza Yehova
Angelo a Mulungu salalikira mwachindunji kwa anthu. M’malomwake amatsogolera atumiki a Mulungu kwa anthu amene akufuna kuphunzira. Werengani Chivumbulutso 14:6, 7, kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani timafunikira kuthandizidwa ndi angelo tikamalalikira?
Kodi mukumva bwanji mukaganizira kuti angelo angakutsogolereni kwa anthu amene akufuna kuphunzira Baibulo? N’chifukwa chiyani mukumva choncho?
5. Muzipewa zamizimu
Satana ndi ziwanda ndi adani a Yehova komanso a anthufe. Werengani Luka 9:38-42, kenako mukambirane funso ili:
Kodi ziwanda zimawachitira zotani anthu?
Sitiku kumachita zinthu zomwe zingapangitse kuti ziwanda zizitivutitsa. Werengani Deuteronomo 18:10-12, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ziwanda zimafuna kumalankhula nafe komanso kutipusitsa pogwiritsa ntchito njira ziti? Kodi kumene mumakhala anthu amakonda kuchita zinthu ziti?
Kodi mukuona kuti ndi zomveka Yehova akamatiletsa kuchita zamizimu? N’chifukwa chiyani mukutero?
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi mukuganiza kuti khoza limene Palesa anamveka mwana wake linali loopsa? N’chifukwa chiyani mukutero?
Kodi Palesa anafunika kuchita chiyani kuti asamavutitsidwe ndi ziwanda?
Akhristu enieni salola kuti ziwanda ziziwavutitsa. Werengani Machitidwe 19:19 ndi 1 Akorinto 10:21, kenako mukambirane funso ili:
Ngati muli ndi zinthu zokhudzana ndi zamizimu, n’chifukwa chiyani muyenera kuziwotcha kapena kuziwononga?
6. N’zotheka kugonjetsa Satana ndi ziwanda zake
Satana ndi amene amalamulira ziwanda. Koma angelo okhulupirika amatsogoleredwa ndi Mikayeli, mkulu wa angelo. Mikayeli ndi dzina lina la Yesu. Kodi Mikayeli ali ndi mphamvu zochuluka bwanji? Werengani Chivumbulutso 12:7-9, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi wamphamvu kwambiri ndi ndani, pakati pa Mikayeli ndi angelo ake komanso Satana komanso ziwanda zake?
Kodi mukuganiza kuti otsatira a Yesu ayenera kumaopa Satana ndi ziwanda zake?
Mungathe kugonjetsa Satana ndi ziwanda zake. Werengani Yakobo 4:7, kenako mukambirane funso ili:
Mungatani kuti musamavutitsidwe ndi Satana ndi ziwanda zake?
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Palibe vuto lililonse kumasewera magemu ndi kuwonera mafilimu okhudzana ndi zamizimu. Ndi zosangalatsa basi.”
N’chifukwa chiyani maganizo amenewa ndi oopsa?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Angelo okhulupirika amatithandiza. Satana ndi ziwanda zake ndi adani a Yehova ndipo amagwiritsa ntchito zamizimu pofuna kusocheretsa anthu.
Kubwereza
Kodi angelo okhulupirika amathandiza bwanji anthu kuphunzira zokhudza Yehova?
Kodi Satana ndi ziwanda zake ndi ndani?
N’chifukwa chiyani inuyo simukufuna kuchita chilichonse chokhudzana ndi zamizimu?
ONANI ZINANSO
Onani umboni wosonyeza kuti Yesu ndi Mikayeli mkulu wa angelo.
“Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani umboni wotsimikizira kuti Mdyerekezi ndi weniweni.
Onani zimene zinathandiza mayi wina kusiya kukhulupirira zamizimu.
Onani mmene Satana amapusitsira anthu powachititsa kuti azikhulupirira mizimu.
“Zoona Zake za Matsenga ndi Ufiti” (Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza? chigawo 5)