Mutu 15
“Turukani Pakati Pao”
1. Ngati timakonda coonadi ndi cilungamo, kodi tiyeneranso kudana ndi kupewa ciani?
YEHOVA Mulungu amawayembekezera onse amene amamkonda ndi kumtumikira iye kusagwirizana konse ndi kulambira konyenga. Ponena za Mwana wa Mulungu, Baibulo limanena kuti: “Mwakonda cilungamo, ndi kudana naco coipa.” Cifukwa ca ici Atate wace anamdalitsa iye, akumamkuza iye monga mfumu yosankhidwa ya ufumu wa Mulungu. (Ahebri 1:9) Ngati mumakonda coonadi ndi cilungamo, pamenepo inunso mudzadana naco ndi kucipewa cimene ciri conyenga ndi cosakondweretsa Mulungu. Mu njira iyi inu mungapeze cinjirizo ponse pawiri tsopano ndiponso mkati mwa nthawi ikudzayo ya kupereka ciweruzo ca Mulungu pa awo amene samalabadira cifuniro cace.
2. Ngati tikuona kusiyana kwa pakati pa awo amene amamtumikira Mulungu ndi awo amene samamtumikira, kodi ndi kacitidwe kotani kamene tiyenera kukatsatira, ndipo ncifukwa ninji?
2 Kalekale Mulungu ananeneratu kuti iye adzakhala ndi anthu amene adzakhala ‘cuma cace capadera,’ ndi kuti anthu ongopenyerera adzakuonadi “kusiyana kwa pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa womtumikira Mulungu ndi uyo amene sanamtumikire iye.” (Malaki 3:17, 18, NW) Ngati mukuona kusiyana kumeneku, pamenepo muyenera kucitapo kanthu mogwirizana nako. Kulephera kutero kudzaciika paupandu ciyembekezo canu ca kuupeza moyo wamuyaya. Kodi ndi kacitidwe kotani kamene muyenera kukatsatira? Mau a Mulungu amanena motsimikizira kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti cilungamo cigawana bwanji ndi cosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? . . . Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?” Cifukwa cakuti sipangakhale unansi woyenera pakati pa awo amene akucita cilungamo ndi awo amene akucita kusayeruzika, Mulungu amalamulira kuti: “Turukani pakati pao ndipo patukani.”—2 Akorinto 6:14-17.
KUTURUKA MU “BABULO WAMKURU”
3. Kodi ndi mau amodzimodziwo otani amene Mulungu anawalankhula kwa anthu ace a mu ndende mu Babulo wakale, ndipo kodi uku kunali kuwamana iwo cinthu ciriconse cabwino?
3 Kwa awo amene pa nthawi yina anali anthu ace osankhika ndi amene anali mu ndende mu Babulo wakale, Yehova Mulungu analankhula mau amodzimodziwo: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga! Mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi cilungamo cako monga mafunde a nyanja; . . . dzina lace silikadacotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga. Turukani inu m’Babulo.” (Yesaya 48:17-20) Zimene Yehova anazicita kumeneko zinali zowapindulitsa awo amene anamkonda iye, osawamana iwo cinthu ciriconse cabwino. Mwa kumgonjetsa Babulo mu 539 B.C.E. iye anakupangitsa kukhala kothekera kwa iwo kucoka m’Babulo monga anthu omasuka.
4. (a) Ngakhale kuli kwakuti Babulo wakale kulibe, kodi Mulungu amanenanji ponena za Babulo wina? (b) Mu Cibvumbulutso mutu 17, kodi ndi motani mmene Babulo wamkuru ameneyu akuphiphiritsidwira?
4 Babulo wakale kulibe. Komabe Mulungu akulankhula za Babulo wina wochedwa “Babulo Wamkuru.” Ndipo kaciwirinso iye amapereka lamulo lakuti: “Turukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi macimo ace, ndi kuti mungalandireko ya miliri yace.” (Cibvumbulutso 18:4) M’mutu wapambuyopo wa Cibvumbulutso, Babulo wamkuru akulongosoledwa mophiphiritsira monga mkazi wacigololo amene amalamulira kapena kuwakwera pa msana “anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe,” ndi amene ali ndi “ufumu pa mafumu a dziko” ndipo ‘amacita cigololo’ ndi mafumu amenewa.—Cibvumbulutso 17:1, 2, 15, 18.
5. (a) Kodi Babulo Wamkuru ali ulamuliro wa ndale za dziko? (b) Kodi ncifukwa ninji Babulo Wamkuru sangakhale ulamuliro wa malonda? (c) M’Baibulo, ncifukwa ninji ulamuliro wacipembedzo unaphiphiritsiridwa ndi mkazi wacigololo?
5 Ici cimatanthauza kuti Babulo Wamkuru ali ulamuliro. Ulamuliro wotani? Popeza kuti “mafumu a dziko,” magulu a ndale za dziko, akunenedwa kuti ‘akucita cigololo’ ndi mkaziyo, Babulo Wamkuruyo Sali ulamuliro wa ndale za dziko. Bukhu la Cibvumbulutso limasonyeza kuti pamene Babulo Wamkuru waonongedwa “amalonda” a dziko lapansi adzaima patali nalira; cotero iyenso sali ulamuliro wa malonda. (Cibvumbulutso 18:15) Kodi nanga, iye angakhale ulamuliro wacipembedzo? Eya, cipembedzo cakhala nacodi cisonkhezero cacikuru pa maufumu a ndale za dziko, ndipo ulamuliro wace ukufalikira kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana a pa dziko lapansi. Koma kodi ncifukwa ninji ulamuliro wacipembedzo umenewu ukuphiphiritsidwa ndi mkazi wauhule wokhala ndi cimo la cigololo? Cifukwa cakuti uwo umasanganiza cipembedzo ndi ndale za dziko. Ponena za Cikristu ca Dziko, Baibulo limasonyeza kuti awo amene amanena kuti amamtumikira Mulungu koma ali osakhulupirika ndipo alowa m’kugwirizana ndi maulamuliro a ndale za dziko akuonedwa ndi Mulungu kukhala mahule auzimu kapena akazi acigololo.—Ezekieli 16:1, 2, 28-30; Yakobo 4:4.
6. Kodi ndi kuti kumene cipembedzo conyenga cinayambirako citapita Cigumula, ndipo kodi ndi motani mmene ziphunzitso zace ndi macitacita zinafikira kukhala zowanda?
6 Kunali pasanapite nthawi yaitali kucokera pa cigumula ca m’tsiku la Nowa pamene cipembedzo conyenga cinayambika mu Babulo, kumene Nimrode anadzikuza ‘motsutsana ndi Yehova.’ Komabe, Yehova anacisokoneza cinenero ca anthuwo ndipo “anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi.” Pamene iwo anapita, iwo anazitenganso ziphunzitso zao Zacibabulo limodzi ndi macitacita. (Genesis 10:8-10; 11:4-9) Mogwirizana ndi ici, bukhu lakuti The Religion of Babylonia and Assyria (lolembedwa ndi Mphunzitsi Morris Jastrow, tsamba 701) limanena za “lingaliro lofala limene linasonyezedwa mwa anthu akale mwa masonyezedwe akuru kopambana a malingaliro acipembedzo mu Babulo ndi mwa nchito yacipembedzo imene inali m’dera limenelo.”
7. Kodi ziphunzitso ndi macitacita ambiri amene akupezeka m’zipembedzo lerolino zinayambira kuti?
7 Motero, ngakhale kuli kwakuti anthu ambiri samacizindikira ici, pali ziphunzitso ndi macitacita ambiri zimene zikupezeka mu zipembedzo za pa dziko lonse lapansi lerolino zimene ciyambi cace ndico cipembedzo conyenga ca mu Babulo. Kodi zina za ico ndi ciani?
8. (a) Tazichulani zina za ziphunzitso zacipembedzo zimene zinali zodziwika kwambiri mu Babulo wakale. (b) Kodi izo zikuphunzitsidwa m’Mau a Mulungu?
8 Pakati pa ziphunzitso zimene zinali zochuka mu Babulo wakale panali: kulambira kwa utatu kapena milungu itatu, cikhulupiriro cakuti moyo waumunthu sumafa, ndi ciphunzitso cakuti anthu anali kumazunzika iwo atamwalira m’dziko lobisika kapena “dziko losabwerako.” Kugwiritsiranso nchito kwa zifanizo kunali ndi mbali yaikuru mu kulambira kwa Acibabulo. Monga momwe kwasonyezedwera kale m’mitu imene yapitayo ya bukhu ili, palibe ciriconse ca ziphunzitso izi cimene cimaphunzitsidwa m’Mau a Mulungu, Baibulo. Komabe, kodi timaziona ziphunzitso zimodzimodzizo ndi macitacita amodzimodziwo m’magulu a cipembedzo amene atizinga ife lerolino?
9. (a) Kodi nciani cimene cimacipatsa cipembedzo cikwangwani cakuti ico ciri mbali ya Babulo Wamkuru? (b) Popeza Mulungu ananeneratu kuti iye adzadzetsa cionongeko ca dzidzidzi pa Babulo Wamkuru, kodi cinthu cofunika kucicita mwamsanga nciani?
9 Limodzi ndi ziphunzitso za “Utatu,” kusafa kwa moyo waumunthu ndiponso moto wa helo wozunzira, ciphunzitso cina ciriconse kapena macitacita amene ali osiyana ndi mau ouziridwa a Mulungu amacidziwikitsa cipembedzoco kukhala conyenga ndipo amacibveka ico cikwangwani cakuti ico ciri mbali ya Babulo Wamkuru. Cipembedzo cingamadzinenere kukhala comakucirikiza kulambira kwa Mulungu woona wa Baibulo ndipo cingamagwiritsire nchito dzina la Mwana wace, Yesu Kristu, koma kodi cingakhale copindulitsa motani ngati caipitsidwa ndi ziphunzitso Zacibabulo limodzi ndi macitacita? (Agalatiya 5:7-9; Mateyu 7:22, 23) Mulungu waneneratu kuti mwadzidzidzi, “m’tsiku limodzi,” miliri ya “imfa, ndi maliro, ndi njala” zidzadza pa Babulo Wamkuru. Cotero kuli kofunika kwambiri ndiponso kaamba ka ubwino wathu kuti tidzipatule kotheratu m’mbali iriyonse ya ulamuliro wa cipembedzo conyenga cimeneco.—Cibvumbulutso 18:8.
10. (a) Kodi munthu angakhale ‘ataturuka pakati pao’ ngati iye apitirizabe kumagwirizana mwa njira iriyonse ndi cipembedzo cimene cimaphunzitsa ziphunzitso zonyenga? (b) Kodi ndi cidziwitso cotani cimene munthu ayenera kucipereka pa gulu lacipembedzo limene iye anali atagwirizana nalo poyambirirapo?
10 Kodi nciani cimene cimatanthauza ‘kuturuka pakati pao’? Kodi kuli kokwanira kwa munthu kungokuzindikira kokha m’maganizo mwace kunama kwace kwa ziphunzitso Zacibabulo, pamene iye akumapitirizabe kugwirizana ndi gulu lacipembedzo limene limamamatira ku ziphunzitso zimenezo? Ndithudi, kodi kameneka sikangakhale kacitidwe ka cinyengo? Kodi kuteroko sikungakhale kupereka cicirikizo cotsimikizirika pa cinthu cimene Mulungu amacitsutsa? Kodi ndi motani mmene munthu woteroyo angadzilingalirire iye mwini moonadi kukhala womvera lamulo la Mulungu lakuti “turukani pakati pao, ndipo patukani, . . . ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka? (2 Akorinto 6:17) Ngati sitikufuna kukhala ofanana ndi anthu aja amene anasonkhana pa kacisi wa Baala mu nthawi ya Yehu naonongedwa mwa kulamulira kwa Mulungu, pamenepo tifunikira kucokeratu mu lirilonse la magulu a Babulo Wamkuru. Tifunikira kusiya kumakhala ndi phande m’macitacita ao. (2 Mafumu 10:20-27)a Tifunikira kuwapatsa iwo cenjezo lakuti ife tikuturuka m’magulu ao. Mwa kumacita ici ife sitidzakhala ‘okaika-kaika,’ tikumayesa “kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziwanda,” mwa kumatero ndi ‘kuputa nsanje ya Yehova.’—1 Mafumu 18:21;b 1 Akorinto 10:21, 22.
11. Kodi kanenedwe ka Baibulo ndi kotani ponena za magulu a kugwirizana mipingo?
11 Koma kodi kugwirizana pamodzi kwa zipembedzo mu kugwirizana mipingo kapena mwa bungwe la cigwirizano sikuli cinthu cabwino? Eya, kodi ndi motani mmene Yehova mulungu amakulingalirira uko? Colembedwa ca Baibulo cimasonyeza kuti iye sanakulole kugwirizana mipingo ndi Akanani kaamba ka mtundu wa Israyeli. (Deuteronomo 7:3, 4) Ndipo kodi ndi motani mmene Mwana wa Mulungu anakulingalirira kugwirizana mipingo? Iye sanalowe mu nchito ya kugwirizana mipingo limodzi ndi magulu a cipembedzo osiyanasiyana a Ciyuda pamene iye anali pa dziko lapansi. Mosiyana ndi cimeneco, iye anacitsutsa kotheratu cipembedzo conyenga ca m’tsiku lace, nalongosola motsimikizira kuti: “Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.”—Yohane 14:6; onaninso Mateyu 23:13, 38.
KUIMIRA COONADI KOTSIMIKIZIRA KUMADZETSA MADALITSO
12. (a) Pamene munthu acisiya kotheratu cipembedzo conyenga, kodi nciani cimene cingacitike kwa anansi ace? (b) Kodi icico cimapereka ciyeso pa cikondi ca mtundu wotani?
12 Kuturuka mu kulambira konyenga kungadzetse zothetsa nzeru. Yesu anasonyeza kuti anansi ace a munthu angakatsutse kacitidwe kameneko. Komabe, ngakhale kukhale kwakuti awo amene akutsutsawo akhale okondedwa ace a munthuyo kwenikweni monga apabanja lace la munthuyo Yesu ananena kuti ici siciyenera kukupanga kusintha kulikonse mu cosankha cathu. (Mateyu 10:32-37) Sikuti kumatanthauza kuwakonda amenewo mocepera koposa kale, koma cofunika ndico ukulu wa cikondi cathu pa Yehova ndi Mau ace a coonadi.
13. (a) Kodi ndi ciyambukiro cotani cimene kupirira kwanu m’coonadi cingakhale naco pa anthu amene inu mumakhalira nawo limodzi? (b) Kodi ndi citsimikiziro cotani cimene Mulungu amacipereka?
13 Kwenikweni, kuli mwa kumakatenga kaimidwe kolimba ka coonadi cakuti munthu angacitepo kanthu kaamba ka ubwino wosatha wa acibale amene poyamba angatsutsane ndi kacitidwe koyenera. Kugonjera ku citsutso kungangowalimbikitsa awawo m’kutsutsana kwao ndi coonadi. Ku mbali yina, khalidwe lanu lokhulupirika m’kumamamatira ku coonadi ca Mau a Mulungu ndi kumakhala mogwirizana naco lidzakupatsani inu madalitso ndi cimwemwe; lidzakupangitsani inu kukhala munthu wabwino. Motero m’kupita kwa nthawi, awo amene ali ogwwirizana ndi inu angafikire pa kuizindikira nzeru ya kacitidwe kanu ndi kuthandizidwa kucionanso coonadi. Ici ndico ciyembekezo cimene Baibulo limatilimbikitsa ife kucigwiritsa ndi kucifunafuna. (1 Akorinto 7:12-16; 1 Petro 3:1, 2) Zoonadi, kudzafunikira kupirira, kukhulupirira kuti njira ya Mulungu ndiyo imene iri yabwino kopambana, ndipo, koposa zonse, cikondi. Koma Mulungu mwiniyo mwacikondi amakutsimikizirani inu kuti iye adzakucirikizani ndi kukupatsani nyonga ngati mumtsogoza iye m’moyo wanu.—Aroma 8:38, 39.
14. (a) Kodi Mulungu amawayembekezera anthu okalamba kupatuka mu cipembedzo conyenga ndi kukutsatira kulambira koona? (b) Kodi ndi ciyembekezo cotani cimene cimeneci cidzacipereka kwa anthu oterowo?
14 Kaciwirinso, ena angalingalire kuti iwo tsopano akalamba, ndi kuti sikungathekenso kusintha kacitidwe kao. Komabe, Yehova Mulungu, amene iye mwiniyo amachedwa “Nkhalamba ya kale lomwe,” amawaitananso anthu okalamba, kuti akhale ndi phande m’kumtamanda iye. (Danieli 7:9; Salmo 148:12, 13) Mau ace amasonyeza kuti ukalamba sudzampangitsa munthu kukhala wopanda liwongo ngati iye alephera kudzipatula pa zimene Mulungu amazitsutsa, koma kuti “imvi ndiyo korona wa ulemu, idzapezedwa m’njira ya cilungamo.” (Miyambo 16:31; onaninso Ezekieli 9:4-6.) Nthawi siimatha m’moyo wa munthu kuti aimire cimene iyeyo akudziwa kukhala coonadi, motero kumaima molimba pa njira ya ku moyo wamuyaya.—Miyambo 10:22.
15. (a) Kodi ndi dalitso lotani limene tingasangalale nalo ngati tituruka pakati pa awo amene amacicita cipembedzo conyenga? (b) Cotero, kodi ife tiyenera kusonkhana ndi yani?
15 Ngati tsopano tikatsatira kacitidwe kotsimikizirika ka kuturuka pakati pa awo amene amacicita cipembedzo conyenga, ife tingasangalale nawo unansi wodalitsika, wacimwemwe ndi Mulungu wathu, Yehova. (2 Akorinito 6:17, 18) Pakuti nkhaniyo simathera pa kungoturuka pakati pa awo amene amaphunzitsa ndi kucita zinthu zimene ziri zosiyana ndi Mau a Mulungu. Mulungu amaperekanso lamulo lakuti ife sitinayenera ‘kuleka kusonkhana kwathu pamodzi,’ monga momwe Ahebri 10:24, 25 amatiuzira ife. Pamenepo, kodi ife tinayenera kusonkhana limodzi ndi yani? Limodzi ndi awo amene amalambira Mulungu mu mzimu ndi m’coonadi. Ponena za amenewo Mulungu amati: “Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.”—2 Akorinto 6:16.
16. Mwa kumafika pa misonkhano ya mboni za Yehova, kodi nciani cimene mudzaciona ponena za (a) zopereka za ndarama? (b) misonkhanoyo? (c) Khalidwe la anthu osonkhanawo?
16 Awo amene amalipanga gulu Lacikristu la mboni za Yehova ndiwo anthu amene adzipatula okha kucokera ku zipembedzo zambiri zacikunja ndi za Cikristu ca Dziko. Motero iwo amthawa Babulo Wamkuru. Mwa kumafika pa misonkhano pa imodzi ya Making’idomu Holo ao, inu mungadzionere nokha za kusiyana kumene icico cakupanga. Sikuli tero kokha cifukwa ca malo osonkhanirawo limodzinso ndi ceniceni cakuti zopereka za ndarama sizimaitanitsidwa, koma kwakurukuru iri misonkhanoyo limodzi ndi mkhalidwe wa anthu osonkhanawo zimene zimazidziwikitsa mboni za yehova kukhala zosiyana ndi zipembedzo zina. Misonkhano imeneyi iridi maphunziro a Baibulo, ikumagogomezera za mmene maprinsipulo a Baibulo amagwirira nchito m’kakhalidwe kathu ka tsiku ndi tsiku ndiponso za mmene tingaphunzitsire Mau a Mulungu kwa ena. Kumeneko inu mudzawaona anthu amene ‘amafunafuna coyamba moona mtima ufumuwo ndi cilungamo ca Mulungu,’ ndi amene mwacangu amayesayesa kuziturutsa zipatso za mzimu wa Mulungu.—Mateyu 6:33; Agalatiya 5:22, 23.
17. Ncifukwa ninji kuli kofunika kukhala ndi phande m’misonkhano imeneyi mokhazikika?
17 Kufikapo kamodzi kapena kawiri kungacikhutiritse cidwi canu ca kufuna kudziwa kuti zimatani, koma kuti inu mukupange kupita patsogolo kotsimikizirika mu utumiki wa Mulungu inu mufunikira kukhala monga Akristu oyambirira. Iwo anaciona coonadi kukhala ca mtengo wapatali, cotero iwo “anali cikhalire m’ciphunzitso ca atumwi . . . Ndipo tsiku ndi tsiku anali cikhalire ndi mtima umodzi m’kacisi.” (Macitidwe 2:42, 46) Kokha mwa kumakhala ndi phande mokhazikika m’misonkhano ya mpingo imeneyi inuyo mungacipititse patsogolo cikhulupiriro, ciyamikiro ndi citsimikiziro zimene inu mufunikira kuti mupeze cibvomerezo ca Mulungu.
18. Kodi ndi lonjezo lotani la Yesu limene lidzakwaniritsidwa ngati mudzipatula ku Babulo Wamkuru ndi kumasonkhana ndi anthu a Yehova mokhazikika?
18 Ngakhale kuli kwakuti kucoka mu Babulo Wamkuru wamakono kungakupangitseni inu kutaya mabwenzi anu akale, inu mudzwapeza ambirimbiri mwa kumafika kwanu pa misonkhano ya anthu a Yehova mokhazikika. Mofanana ndi ophunzira oyambirira a Yesu, amenenso anasiya zambiri m’malo mwakuti amtsatire iye, inu mudzaona likumakwaniritsidwa mwa inu lonjezo lakuti ‘mudzapeza mazana owirikiza tsopano ndi mu nthawi irinkudza’ ponena za abale ndi alongo ndi nyumba kumene inu mudzalandiridwa mwacisangalalo. Inu mudzapeza kuti inu mwafikira kukhala mbali ya banja lalikuru la abale Acikristu, amene cikondi cao ndi utsamwali wao ziri zamphamvu kwenikweni ndi zoona mtima. Inu mudzapeza zonsezi limodzi ndi ciyembekezo ca moyo wosatha “mu dongosolo limene likudzalo la zinthu.”—Marko 10:28-30; Salmo 27:10 [26:10, Dy].
19. (a) Kodi ndi motani mmene Mulungu akugwiritsirira nchito gulu lace looneka ndi maso kaamba ka dalitso lathu? (b) Cotero nciani cimene ciri canzeru kwa ife kucicita tsopano?
19 Yehova Mulungu ali nalo gulu looneka ndi maso limene akuligwiritsira nchito lerolino kutiphunzitsira ndi kutikonzekeretsa ife kaamba ka moyo mu dongosolo lace latsopano lolungama. Dongosolo lamakonoli loipa litacoka, njira ya Mulungu idzapezeka kulikonse. Boma limene lidzatsala lidzakhala lace lokha. (Dan. 2:44) Anthu ace obvomerezeka ndiwo okha amene adzatsala pa dziko lapansi amene munthu angaceze nawo. Miyezo yokha ya Mulungu yopimira coyenera ndi colakwa ndiyo imene idzaloledwa. Padzakhala cipembedzo cimodzi cokha. Cotero cinthu canzeru kucicita ndico kudzigwirizanitsa ife eni tsopanolino ndi njira ya Mulungu yocitira zinthu, tikumagwiritsira nchito mokwanira kaphunzitsidwe kamene Mulungu wakapereka kupyolera m’Mau ace olembedwa Baibulo Loyera. Mu Njira iyi ife timatsimikizira kuti ife timanenadi mwa mtima wonse pamene timati ife tikufuna moyo wamuyaya mu dongosolo lolungama latsopano la Mulungu.—Salmo 86:10, 11 [85:10, 11, Dy]; Miyambo 4:10-13.
[Mawu a M’munsi]
a 4 Mafumu 10:20-27, Dy.
b 3 Mafumu 18:21, Dy.