Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • tr mutu 10 tsamba 82-93
  • Ufumu wa Mulungu Uyamba Kulamulira Pakati pa Adani Ace

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufumu wa Mulungu Uyamba Kulamulira Pakati pa Adani Ace
  • Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUKWANIRITSIDWA KWA “CIZINDIKIRO”
  • 1914 CAKA CODZIWIKA BWINO LOMWE
  • Kodi Chiwonongeko cha Dziko Chonenedweratucho Chidzadza Liti?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • “Mapeto a Dziko” Ayandikira!
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Dongosolo Lamakonoli Lidzakhala Kwautali Wotani?
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Masiku Otsiriza
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
tr mutu 10 tsamba 82-93

Mutu 10

Ufumu wa Mulungu Uyamba Kulamulira Pakati pa Adani Ace

1. (a) Kodi anthu a cikhulupiriro akhala akumayembekezera ciani kwa nthawi yaitali? (b) Kodi Mulungu kwa nthawi yonse sanakhale Mfumu?

KWA zaka zikwi zambiri anthu a cikhulupiriro akhala akumayembekezera motenthedwa maganizo za tsiku limene ufumu wa Mulungu udzakuyamba kulamulira kwace. Iwo akuzindikira mwa mtima wonse kufunika kwace kwakuti Mulungu acitepo kanthu mwacindunji mu zocitika za apa dziko lapansi. Kodi cimeneci cimatanthauza kuti Mulungu acitepo kanthu mwacindunji mu zocitika za pa dziko lapansi. Kodi cimeneci cimatanthauza kuti Mulungu sanakhale Mfumu mkati mwa zaka mazanamazana zimene zapitazo? Ai, pakuti Yehova nthawi zonse wakhala Wolamulira Wamkuru wa mu cilengedwe caponseponse. (Yeremiya 10:10) Koma pano pa dziko lapansi ulamuliro wace watokosedwa. Ndipo, monga momwe taonera kale, pa zifukwa zabwino limodzi ndi cifuno cacikondi, Mulungu wawalola maboma aumunthu osonkhezeredwa ndi Satana kulamulira kwa nyengo ya nthawi yokhala ndi polekezera.

2. Kodi ufumu wa Mulungu nciani, ndipo kodi mphamvu ya kulamulira amaipereka kwa ndani?

2 Komabe, Yehova analonjeza kuti pakutha pa nthawi imeneyo iye adzacitapo kanthu mwacindunji motsutsana ndi opanduka onse ndi otsutsana ndi ulamuliro wace. Ndipo iye adzalilowetsa dziko lapansili limodzi ndi okhalamo ace m’kulamulira kwace kotheratu kaciwirinso. Motani? Mwa ufumuwo, boma latsopano la kumwamba limene wolamulira wace ali Mwana wace Yesu Kristu. Cotero kuyamba kulamulira kwa ufumu umenewo kumatanthauza kuti masinthidwe akuru kopambana ali pafupi. Kumatanthauza kuti Yehova Mulungu wapereka kwa mwana wace “ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse amtumikire.”—Danieli 7:13, 14.

3. Kodi ndi motani mmene ena coyamba angakuonere kukhala kwacilendo kulingalira kuti ufumu wa Mulungu wayamba kale kulamulira?

3 Cinthu cimeneco cacitika kale kumwamba. Ulamuliro wa ufumu wapatsidwa kale kwa Mwana wa Yehova. Kodi cimeneco cimamvekera kukhala cacilendo kwa inu? Cingatero, makamaka pomalingalira za mikhalidwe yobvuta kwambiri imene ikuukantha mtundu wa anthu. Koma kwenikwenidi, kuli cifukwa ca mikhalidwe imeneyiyo cakuti ife tingakhale otsimikizira kuti icico ciri coona. Kodi nchifukwa ninji kuli tero?

4. (a) Kodi ncifukwa ninji zolengedwa zonse sizimaubvomereza ufumu wa Mulungu? (b) Cotero kodi nciani cimene cinanenedweratu kuti Mulungu adzamuuza Mwana wace pakumpatsa iye mphamvu ya kulamulira monga mfumu?

4 Ici ciri tero cifukwa cakuti kuyamba kulamulira kwa ufumu wa Yehova sikukubvomerezedwa ndi zolengedwa zonse. Sikuti ndi onse amene amafuna kumalamuliridwa ndi boma limene limamamatira pa cilungamo. (Luka 19:11-14) Pacifukwa ca ici, Yehova kalekale analemba m’Mau ace kuti pamene iye ‘ayamba kulamulira monga mfumu’ pa dziko lapansi ‘mitundu idzakwiya.’ (Cibvumbulutso 11:17, 18) Iye ananeneratu kuti, pa nthawi ya kumpatsa mphamvu Mwana wace yakuti acitepo kanthu, kudzakhala koyenera kwa iyeyo kunena kuti: “Citani ufumu pakati pa adani anu.”—Salmo 110:2 [109:2, Dy].

5. Pamenepo kodi ndi ciani cimene cinayenera kucitidwa m’mwamba, limodzi ndi coturukapo cotani kaamba ka dziko lapansili?

5 Pamenepo Kristu Yesu akamgwetsa Satana kucokera kumwamba, malikuru a bomalo, kumponyera iye ku cigawo ca dziko lapansi, pokonzekera za kumpangitsa iye kukhala wosagwira nchito kotheratu. Kumwamba cilengezo cacikuruco cidzapangidwa: “Tsopano zafika cipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wace.” Koma nanga bwanji ponena za dziko lapansi? “Tsoka . . . , cifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukuru, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.” (Cibvumbulutso 12:5, 7-10, 12) Kulamulira kotheratu kwa dziko lapansi kocitidwa ndi ufumu wa Mulungu posacedwapa kuyenera kutsatirapo! Komabe, kuyambika kwa kulamulira kwa ufumu wa Mulunguko sikumatanthauza mtendere wongodza mwamsangamsanga limodzi ndi cilungamo pa dziko lapansi. Mosiyana ndi cimeneco, uko kumaiyambitsa nyengo ya bvuto lalikurukuru lopanda lina lofanana nalo pa anthu okhala pa dziko lapansi.

6. (a) Kodi ndi funso lotani limene atsatiri a Yesu anamfunsa iye ponena za kukhala pafupi kwace kwaciwiri? (b) Kodi ncifukwa ninji “cizindikiro” cooneka cinali cofunika? (c) Kodi umboni wooneka ndi maso umenewu ukakhala citsimikiziro ca ciani ponena za dongosolo loipa ili la zinthu?

6 Pomazindikira ici, tingalizindikire bwino tanthauzo la zimene Yesu anawauza atsatiri ace ponena za kudza kwace kwaciwiri. Iwo anali atamfunsa iye kuti: “Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo cizindikiro ca kufika kwanu nciani, ndi ca mathedwe a nthawi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Pamenepo Yesu analongosola, kaamba ka iwowo ndiponso ife, za zimene zidzacitika kumwamba. Mwa njira iyi, ngakhale kunali kwakuti zocitika zakumwambazo zikakhala zosaoneka ndi maso aumunthu, padzakhala citsimikiziro cooneka cakuti Kristu anali atakhala pampando wacifumu, akumalamulira monga mfumu. Ukakhala umboni wakuti dongosolo loipa la zinthu limene lautsendereza mtundu wa anthu kwa zaka mazana ambiri linali litalowa ‘m’masiku ace otsiriza.’ (2 Timoteo 3:1) Ngakhale kunali kwakuti kunanenedweratu kuti padzakhala onyoza amene adzayesa kuziluluza zenizenizo, komabe umboniwo udzakhala woonekera bwino.—2 Petro 3:3, 4.

7. (a) Kodi pali cicitika cimodzi cikha, cimene mwa cimeneco, cikakhala umboni wakuti “mathedwe” ali pafupi? (b) Kodi timadziwa bwanji dzinja likakhala pafupi? Cotero kodi ndi motani mmene tingadziwire pamene Ufumuwo wayamba kulamulira?

7 Pamene tiulingalirira umboniwo limodzi, kuli kofunika kuzindikira kuti Yesu sananene kuti cocitika cimodzi cokha, monga ngati mbiri ya nkhondo kapena cibvomezi cacikuru, ndico cimene cidzakhala umboni wakuti “citsiriziro” cinali pafupi. (Mateyu 24:6) M’malo mwace, iye anati: “Onani mkuyu, ndi mitengo yonse: pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo. Inde cotero inunso, pakuona zinthu izi zirikucitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.” (Luka 21:29-31) Ngati tiuona mtengo umodzi ukumayoyoka masamba mkati mwa cirimwe cifukwa cakuti kunja kwatentha kwa masiku angapo, ife sitimalingalira kuti dzinja lafika, kodi timatero? Koma ngati tiiona mitengo yonse ikuphukira ndipo usana ukumakhala wautali ife timadziwa kuti dzinja liri pafupi. Kuli cimodzimodzinso, pamene zinthu zonse zimene Yesu anazilongosola zicitika, ife tingadziwe motsimikizirikadi kuti Kristu ali pa mpando wace wakumwamba ndi kuti ufumu wace, ndithudi, wayamba kulamulira mokangalika. Pamene cimeneco cicitika, cilanditso ciri pafupi!

KUKWANIRITSIDWA KWA “CIZINDIKIRO”

8. (a) Monga momwe kwalembedwera pa Mateyu 24:7, kodi nciani cimene Yesu ananena kuti cidzasonyeza kukhala kwace pafupi kwaciwiri? (b) Kodi ndi motani mmene nkhondo imene inabuka mu 1914 inagwirizanira kwambiri ndi kalongosoledwe kaceko? (c) Cotero kodi ndi caka citi cimene cinakusonyeza kuyambika kwa ‘masiku otsiriza’ ndi nthawi imene ufumu wa Mulungu unakuyamba kulamulira kwace kokangalika?

8 Kwenikwenidi kodi nciani cimene Yesu anacisonyeza kukhala comakusonyeza kukhala pafupi kwace kwaciwiri ndi “mathedwe a nthawi ya pansi pano”? Iye anati: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi m’malo akuti akuti.” (Mateyu 24:7) Panopo Yesu akutiuza ife kufunafuna nkhondo ya mtundu watsopano-nkhondo ya ponseponse! Nkhondo imene inaulika mu 1914 ikugwirizana ndi kalongosoledwe kaceko. Sikokha kuti magulu a khondo anamenyana pa mabwalo a nkhondo; koma anthu wambanso analinganizidwa kuti acipereke cicirikozo cokwanira mu nkhondoyo. Monga momwe Yesu ananeneratu, mitundu yonse yathunthu ndi maufumu inali kumenyana. Kwa nthawi yoyamba mu mbiri ya dziko, dziko lonse lapansi linali pa nkhondo. Ndico cifukwa cace iyo ikuchedwa “Nkhondo Yoyamba ya Dziko.” Ponena za iyo bukhu lakuti World War I linati:

“Mu ukulu wace, mu ciwawa cace, ndipo koposa zonse, m’kufalikira kwace ponseponse, panalibe yina yolingana nayo. Nkhondo Yoyamba ya Dziko inazipangitsa zaka za zana ili kukhala za Nkhondo Yokalikira Ponseponse,—M’kakwaniritsidwe kenikeni ka liulo—nkhondo ya dziko lonse.

“Ndi kale lonse 1914-1918 isanakwane palibe nkhondo imene inazigwiritsira nchito mphamvu zocuruka zoterozo za omenyana ndi kufalikira pa mbali yaikuru yoteroyo ya dziko lapansi. Palibe mitundu yocuruka kwambiri monga imeneyo imene inali italowamo. Ndi kale lonse panalibe kuphana kwacisawawa koteroko ndi kosasankha.”a

The World Book Encyclopedia inanena kuti ciwerengero ca asilikari amene anaphedwa ndi kubvulazidwa cinapitirira 37,000,000, ndipo inaonjezapo kuti:

“Ciwerengero ca anthu wamba osakhala asilikari amene anafa m’madera amene nkhondoyo inamenyedweramo kwenikweni cinakwanira 5,000,000. njala, nthenda ndi kusowa pokhala zinawapha anthu 80 mwa akufa 100 alionse mwa anthu wamba amenewa. Folowenza, imene anthu ena ananena kuti inacititsidwa ndi nkhondoyo, inawapha mamiliyoni makumi ambirimbiri oonjezereka.”b

Izi zinali monga momwe Yesu anli ataneneratu. Zitaikidwa pamodzi, zenizeni izi zimaidziwikitsa 1914 monga kukhala ciyambi ca “masiku otsiriza” ndi caka cimene ufumu wakumwamba wa Mulungu unakuyamba kulamulira kwace kokangalika.—Onaninso Luka 21:10, 11.

9. Kodi ndi cocitika cina citi comawasonyeza “masiku otsiriza” cimene cakhala cikumacitika mowirikizawirikiza ciyambire 1914?

9 Ndiponso, 1914 itapita zibvomezi zotsatizanatsatizana zaligwedeza dziko lapansi, kumakucititsa kuononga kwakukuru. Mu 1915, mu Italy, cifupifupi anthu 30,000 anaphedwa. Mu 1920, mu China, okwanira 180,000 anafa. Mu 1923, okwanira 143,000 anafa mu Japan. Ndipo zibvomezi zazikuru zapitirizabe kumacitika mowirikiza mozizwitsa ciyambire pa nthawi imeneyo. Monga momwe Yesu ananeneratu kuti, izo ziri cizindikiro cina ca ‘masiku otsiriza.’

10. Kodi nciani cimene cikusonyeza kuti zocitika zimene zinacidziwikitsa caka ca 1914 zinangokhala kokha “zowawa zoyamba”?

10 Komabe, Yesu ananena kuti zocitika zimene zinasonyeza ciyambi ca ‘masiku otsiriza’ mu 1914 zinali kokha “zowawa zoyamba.” (Mateyu 24:8) Bvuto lokulira linalinkudza. Moukwaniritsa ulosi wacewo, zinaterodi. The World Book Encyclopedia imati: “Nkhondo Yoyamba ya Dziko ndi zotsatirapo zace inacititsa bvuto lalikuru kopambana la kucepa kwa ndarama mu mbiri ya dziko kuciyambiyambi kwa zaka zoyambira 1930. Zotsatirapo za nkhonoyo limodzi ndi zothetsa nzeru za kusintha kuti pakhale mtendere zinatsogolera ku kupanda mpumulo cifupifupi mu mtundu uliwonse.” Ici cinatsogolera ku Nkhondo Yaciwiri ya Dziko. Ndipo ponena za nkhondo imeneyo bukhu lokhalokhalo limati:

“Nkhondo Yaciwiri ya Dziko inapha anthu ambiri, inaononga ndarama zambiri, inaononga Cuma cambiri, inayambukira anthu ambiri . . . koposa nkhondo yina iriyonse mu mbiri yakale. . . . Kwayerekezedwa kuti ciwerengero ca akufa mu nkhondoyo, anthu wamba limodzi ndi asilikari omwe, anakwanira kupitirira 22,000,000. Ciwerengero ca obvulala cayerekezedwa kukhala kupitiira 34,000,000.”c

Zoonadi, “zowawa” zimene Yesu anali atazineratu zafikira kukhala zokulira pamene ‘masiku otsirizawa’ akumasendezera kuti afike pacimace.

11. (a) Kodi ndi pa mlingo wotani kuperewera kwa zakudya kwaonjezera zowawazo, monga momwe Yesu ananeneratu? (b) Kodi nciani cimene bukhu la mutu wakuti “Famine-1975!” (“Njala-1975!”) limanena ponena za mtsogolo?

11 Mkati mwa Nkhondo Yaciwiri ya Dziko ndiponso pambuyo pace kuperewera kwa zakudya kofala kunaonjezera zowawazo. Pasanapite nthawi yaitali itangotha nkhondoyo magazini ochedwa Look anati:

“Mbali imodzi mwa mbali zinai za anthu okhala pa dziko akusauka ndi njala lerolino. Mawa zidzaipitsitsa. Njala m’mbali zambiri za dziko lapansi lerolino yabvuta kwambiri koposa mmene ambiri a ife tingaganizire. . . .  Pali anthu ambiri tsopano amene akupwairapwaira cakudya mosaphula kanthu lerolino koposa nthawi yina iriyonse mu mbiri yakale.”d

Posacedwa pomwepo, bukhu lolembedwa mutu wakuti “Famine—1975!” (“Njala—1975!”) linalongosola ponena za kuperewera kwa cakudya kwa lerolino kuti:

“Njala ikufalikira dziko ndi dziko, kontinenti ndi kontinenti m’mbali yosatsungula ya maiko otentha ndi othentha pang’ono.—Bvuto la masiku anoli likupita mbali imodzi—ku ngozi. Lero pali mitundu yodya mosakhuta; mawa padzakhala mitundu yomasauka ndi njala.

“Pokwana 1975 kusalongosoka kwa maboma, zipolowe, kulamulira kwaudikitetara kocitidwa ndi ankhondo, ziwawa, kuonongedwa kwa njira za kayendedwa ndi kupanda mpumulo kwaciwawa ndizo zimene zidzatenga malo mu nthawiyo m’mitundu yambiri ya njalayo.”e

12. (a) Kodi ndi mikhalidwe ina iti, imene inanenedweratu m’Baibulo, imene yabuka pa mlingo waukurukuru ciyambire 1914? (b) Cotero kodi ndi maripoti a mtundu wanji amene amadza kucokera ku mtundu ndi mtundu?

12 Yesu ananeneratunso za “kucuruka kwa kusayeruzika” kukhala monga cizindikiro ca ‘masiku otsiriza.’ (Mateyu 24:12) Ndipo Mulungu anamuuzira mtumwi Paulo kuonjezerapo kuti: “Masiku otsiriza . . .  anthu adzakhala odzikonda okha, . . .  osamvera akuwabala, . . .  osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda Mulungu, . . .  anthu oipa ndi onyenga, adzaipa ciipire.” (2 Timoteo 3:1-5, 13) Iyi ndiyo mikhalidwe imene yabuka pa mlingo waukurukuru ciyambire 1914! Inuyo mwaiona iyo ndi maso anu, kodi simunaione? Pa dziko lonse lapansi kusayeruzika kukukulakula. Loya wina anati: “cifupifupi kulikonse, kuphatikizapo Soviet Russia, kukuonekera kuti pali kuonjezereka kwa upandu, ndipo ha, makamaka maupandu ocitidwa ndi anyamata opulupudza.”f Kucokera ku mtundu ndi mtundu kukudza maripoti onga ngati awa:

“Pfunde la upandu ndi ciwawa likumsesa United States yense . . .  M’mizinda yambiri, akazi amacita mantha kuyenda kutada. Ndipo iwo ali ndi cifukwa cabwino. Cigololo cogwirira, ziukiro, kubuka kwa zipolowe zamisala zikuonjezerekaonjezereka. Kukuonekera kuti maupandu akumacitidwa cifukwa ca nkharwe cabe . . .  Kumvera lamulo ndi cilongosoko zikunyonyotsoka.”g

13. (a) Pa Luka 21:25, 26, kodi ndi mbali yina iti ya “masiku otsiriza” imene Yesu anaineneratu? (b) Kodi ndi motani mmene kakwaniritsidwe ka ulosi uwu kakhalira koonekera bwino mu mbiri za m’nthawi yathu?

13 Monga mbali yina ya ‘masiku otsiriza,’ Yesu analankhula za cisokonezeko cacikuru ndi mantha pakati pa mitundu limodzi ndi atsogoleri ao. Iye ananeneratu kuti: “Pa dziko lapansi cisauko ca mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru . . .  anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi.” (Luka 21:25, 26) Kukwaniritsidwa kwa ulosi uwu kuli koonekera bwino mu mbiri za mu nthawi yathu. U.S. News & World Report inati:

“Kodi dziko liri mu cipolowe cacikuru koposa mmene kunakhalira Nkhondo Yaciwiri ya Dziko isanacitike? Mosakaikira.

“Pa avereji, kuomberana kumabuka kamodzi pa mwezi. Pomazipatula nkhondo zenizeni monga ngati ya ku Korea ndi ku Vietnam, ripotilo limasonyeza zipanduko, kuukira boma, zipolowe, kupandukira boma ndi kuukirana pa dziko lonse kopitirira 300 kuyambira pamene Nkhondo Yaciwiri ya Dziko inathera.”h

Cimene caonjezeredwa ku zinthu zimenezi ndico mantha a kuopa kuonongedwa ndi zida zocurukazo za nyuklea zimene mitundu ina iri nazo. Mlembi wina wa nyuzi ananena kuti: “Coona ndico cakuti lerolino lingaliro lalikurukuru limodzi limene latenga malo akuru m’moyo wathu ndilo mantha.”i Kuli monga momwe Yesu ananeneratu: mtundu wa anthu ukuopa ndipo mitundu ikucita mantha.

14. Kodi maumboni onse amasonyezanji ponena za caka ca 1914?

14 Zizindikiro zonse zonenedweratuzo za ‘masiku otsiriza’ ziripo. Izo zikutsimikizira mosakaikira kuti ife takhala ‘m’masiku otsiriza’ ciyambire 1914. Cifukwa ca cimeneco munali m’caka cimeneco pamene ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira!—Cibvumbulutso 11:17, 18.

15. Ncifukwa ninji mbadwo wathu suli wofanana ndi yina yonse?

15 Kuli koona kuti m’mibadwo yapitayo munali nyengo zina zimene zinali ndi ciwawa cacikuru limodzi ndi cisembwere cocuruka. Kunyonyotsoka kwa Cifumu Caciroma kuli citsanzo ca ici. Koma ndi kale lonse palibe nthawi iriyonse mu mbiri yakale yaumunthu pamene mikhalidwe yonse imene inanenedwa ndi Yesu inaonekera mu m’badwo umodzi. Ndipo ndi kale lonse izo sizinacitikire pamodzi mu mtundu uliwonse wa dziko lapansi. Lerolino ife tikukhala, osangoti kokha m’masiku otsiriza a ufumu umodzi wokha wa ndale za dziko, koma ‘m’masiku otsiriza’ a dongosolo lonse loipa la zinthu lolamulidwa ndi Satana.

1914 CAKA CODZIWIKA BWINO LOMWE

16. Kodi ophunzira Baibulo anadziwiratu kuti padzakhala masinthidwe akuru mu 1914?

16 Zaka zambiri nthawiyi isanakwane ophunzira Baibulo anazindikira kuti 1914 cidzakhala caka cofunika kwambiri. Kawerengedwe ka zaka ka Baibulo kamasonya motsimikizirika ku caka cimeneco,j ndipo ophunzira mosamalitsa Mau a Mulungu anadziwa cimeneco. Iwo anayembekezera kusintha kwakukuru kuti kudzacitika, ndipo zenizeni zimatsimikizira kuti 1914, ndithudi, cinali caka cosaiwalika.

17. Kodi olemba mbiri amati ciani ponena za caka ca 1914?

17 Ena amene amazidziwa bwino zocitika za dziko amabvomereza mokwanira kuti caka ca 1914 cinali cosaiwalika. Nyuzipepala yochedwa Evening Star ya ku London inasimba kuti nkhondo Yoyamba ya Dziko “inaling’amba dongosolo lonse la ndale za dziko la dziko lonse lapansi. Cinthu ciriconse cinasintha. . . .  olemba mbiri yakale ena mu zaka za zana limene likudzalo angadzanene bwinolomwe kuti tsiku limene dziko linapenga linali August 4, 1914.”k Ponena za kusintha kwakukuru kumene 1914 inakupanga, wolemba mbiri yakale H. R. Trevor-Roper anati:

“Kuli kophunzitsa zinthu zambiri kuiyerekeza Nkhondo Yoyamba ya Dziko ndi yaciwiriyo . . .  nkhondo yoyambayo inakupereka kusintha kwakukurukuru mu mbiri yakale. Inaithetsa nyengo yaitali ya mtendere ndi kuiyamba nyengo yatsopano ya ciwawa mu imene nkhondo yaciwiriyo yangokhala ngati mbali yina yongoonjezerapo. Ciyambire 1914 dziko lakhala ndi khalidwe latsopano: khalidwe la kulimbana kwa mitundu yonse. . . .  Motero Nkhondo ya Dziko yoyamba imasonyeza nthawi ya kusintha kwa zinthu mu mbiri yamakonoyi.”l

18. Kodi nciani cimene ena acinena ponena za 1914?

18 Atsogoleri a dziko anenanso kanthu za kufunika kwace kwa caka ca 1914. Mkuru wa boma wapapitapo wa ku West Germany Konrad Adenauer analankhula za nthawi yapitayo “1914 isanakwane pamene panali mtendere weniweni, bata ndi cisungiko pa dziko ili lapansi—nthawi imene ife sitinawadziwe mantha.” Pamenepo iye anaonjezerapo kuti: “Cisungiko ndi bata zacoka m’miyoyo ya anthu ciyambire 1914. Nanga bwanji ponena za mtendere? Ciyambire 1914, Ajeremani sanauone mtendere weniweni mofanananso ndi mbali yaikuru ya mtundu wa anthu.a Ndiponso, tawaonani malongosoledwe a m’bukhu la mutu wakuti “1914.” Muyambitsiyo amati: “Mu caka ca 1914 dziko lapansi, monga momwe linadziwidwira pa nthawiyo, linatha. Koposa caka cina ciriconse pambuyo pace kapena patsogolo pace iyiyo inali nthawi yosaiwalika mu zaka za zana la makumi awiri . . .  kuyambira nthawi imeneyo kunkabe mtsogolo cinthu ciriconse cinasintha.”b

19. Ncifukwa ninji dongosolo loipa ili la zinthu lacita mopenga cotero ciyambire 1914?

19 Satana Mdierekezi limodzi ndi ziwanda zace amadziwa kuti ali ndi “kanthawi” cabe kamene kawatsalira asanaonongedwe. (Cibvumbulutso 12:12) Ngakhale pamene Yesu anali pa dziko lapansi, ziwanda zinadziwa kuti tsiku lina izo zidzaonongedwa. Izo zinasonyeza khalidwe lacidani nthawi imeneyo, ndipo tsopano podziwa kuti zimadziwa kuti nthawi yao yafupika izo ziri zacidani kwambiri ndi zaciwawa koposa kale lonse. (Luka 8:27-33) Izo zimawayambitsa mabvuto ocuruka monga momwe zingathere, m’malo mwakuti ziwapatutse maganizo a mtundu wa anthu kucoka ku ufumu wa Mulungu. Cimeneco ndico cifukwa cace cimene dongosolo loipa ili la zinthu lakhala likumacita mwamisala cotero ciyambire 1914. Ilo likucita monga ngati nguli, cidole ca mwana, cimene cimayenda dzandidzandi mopenga ico cisanagwe ndi kuima kotheratu.

20. (a) Ncifukwa ninji sitinayenera kulefulidwa mtima cifukwa ca mkhalidwe wadzikoli? (b) Kodi nciani cimene Yesu anacineneratu kuti atsatiri ace adzakhala akumacilalikira pa nthawi iyi? Kodi cikucitika?

20 Kodi ife tikutaya mtima cifukwa ca mkhalidwe uwu? Yesu Kristu ananena kuti akuphunzira ace adzakhala naco cifukwa ca kutukulira mitu yao. Cifukwa ninji? Cifukwa cakuti amalidziwa tanthauzo lace. Mu zocitika izi iwo amauona umboni wakuti cilanditso ciri pafupi! (Luka 21:28) Ndipo iwo samangoibindkiritsa mbiri yosangalatsa imeneyi kwa iwo eni, m’dziko lonse lapansi iwo akuilalikira mbiri yodzutsa mtimayo yakuti ufumu wa Mulungu tsopano ukulamulira. Monga momwe Yesu ananeneratu: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwe-po mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Iyinso, iri mbali ya “cizindikiro” cimeneco. Mu North ndi South America, Europe, Africa, Asia limodzi ndi m’zisumbu za m’nyanja mboni za Yehova mokangalika zimapitirizabe kumaubukitsa uthenga wofunika kwambiri uwu. Ponse pawiri m’mizinda yaikuru ndi m’midzi yaing’ono inu mudzazipeza, m’mbali zonse za dziko lapansi. Inde, mbali iyi ya “cizindikiro” ikumakwaniritsidwanso.

21. (a) Tacilongosolani cimene cinacitika mu 1914. (b) Kodi yankho la pemphero lakuti ufumu wa Mulungu “udze” lidzatanthauzanji?

21 Mosakaikira konse, umboniwo umasonya ku 1914 kukhala caka cimene ufumu wa Mulungu unayamba kukhala caka cimene ufumu wa Mulungu unayamba kugwira nchito, ndipo cimeneco cikuzicititsa zinthu kumacitika pano pa dziko lapansi. Mu caka cokhacokhaco “nyengo ya pansi pano yino yoipa” inalowa ‘m’masiku ace otsiriza.’ (Agalatiya 1:4) Posacedwapa tsopano, pemphero lakuti ufumu wa Mulungu “udze” lidzayankhidwa, pamene uwo udzaisonyeza mphamvu yace yaikuru mwa kumaliononga dongsolo lonse loipa la Satana. Pamenepo ufumu wa Mulungu wokha udzagwira nchito monga boma limodzi la kulilamulira dziko lapansi kwamuyaya. (Danieli 2:44) Pomacitenga citsogozo conse ca zocitika za pa dziko lapansi, uwo udzawapereka pa mtundu wa anthu womvera madalitso a mtendere, cimwemwe ndi moyo. Pemphero lakuti ‘cifuniro ca Mulungu cicitike, monga kumwamba, comweconso pa dziko lapansi,’ lidzakwaniritsidwa mwaulemerero, pakuti pa nthawi imeneyo ufumu wa Mulungu udzakhala utadza kudzalamulira kosatha. Ndipo tangolingalirani za cimeneco! Inuyo mungasangalale nawo moyo wamuyaya m’kulamulira kwacikondi kwa ufumu umenewo.—Mateyu 6:9, 10.

[Mawu a M’munsi]

a Bukhu lakuti World War I, lolembedwa ndi H. W. Baldwin, 1962, tsamba 1, 2.

b The World Book Encyclopedia, 1966, Voliyamu 20, tsamba 377.

c The World Book Encyclopedia, 1966, Voliyamu 20, tsamba 379, 380, 410.

d Nyuzipepa yakuti Look, ya pa June 11, 1946.

e Famine-1975, lolembedwa ndi W. & P. Paddock, 1967, tsamba 52, 55, 61.

f U.S. News & World Report, Nov. 1, 1965, tsamba 80.

g momwemo, Aug. 1, 1966, tsamba 46, 47.

h U.S. News & World Report, Nov. 27, 1967, tsamba 62.

i momwemo, Oct. 11, 1965, tsamba 144.

j Kaamba ka kalongosoledwe katsatanetsatane ponena za ici, onani bukhu lakuti “Babylon the Great Has Fallen!” God’s Kingdom Rules!, tsamba 174-181; ndiponso kucokera ku Paradaiso Wotayika Kunka ku Paradaiso Woopezedwanso, tsamba 173.

k Nyuzipepa ya ku London yochedwa Evening Star, imene inagwidwa mau mu New Orleans Times Picayune, Aug. 5, 1960.

l The New York Times Magazine, Aug. 1, 1954, tsamba 9.

a Cleveland West Parker, Jan. 20, 1966, tsamba 1.

b Bukhu lakuti 1914, lolembedwa ndi J. Cameron, 1959, tsamba v, vi.

[Chithunzi patsamba 85]

Yesu anawauza ophunzira ace za cimene cidzakhala umboni wooneka ndi maso wa kukhala pafupi kwace kosaonekako mu mphamvu ya ufumu

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena