Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 5/8 tsamba 26-27
  • Msonkhano Wapadera wa ku Moscow wa za Opaleshoni Yopanda Magazi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Msonkhano Wapadera wa ku Moscow wa za Opaleshoni Yopanda Magazi
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusonyezedwa pa Wailesi Yakanema
  • Kulembedwa m’Nyuzipepala za Zachipatala
  • Kupereka Thandizo
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kufunika Kowonjezereka kwa Chithandizo Ndiponso Opaleshoni Zopanda Magazi
    Galamukani!—2000
  • Mafunso Ophunzirira Brosha ya Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Kodi Kuika Magazi Anthu Odwala Kudzapitirirabe?
    Galamukani!—2006
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 5/8 tsamba 26-27

Msonkhano Wapadera wa ku Moscow wa za Opaleshoni Yopanda Magazi

MANKHWALA OLOŴA M’MALO MWA MAGAZI POCHITA OPALESHONI ndiwo unali mutu wa msonkhano wa zachipatala wa mayiko onse umene unachitikira ku Moscow, Russia, pa October 6, 1998. Madokotala opitirira 800 anafika ku sukulu ya zachipatala yotchedwa Vishnevskij Institute of Surgery kaamba ka msonkhanowo, umene unachitidwa mogwirizana ndi msonkhano wa Sixth All-Russian Congress of Anaesthesiologists and Intensive Care Specialists. Polofesa Andrey Ivanovich Vorobiev, amene ali dokotala wamkulu wa zamagazi pasukulu ya Russian Academy of Medical Sciences, ku Moscow, anakamba mawu amalonje ndi kulandira madokotala ku msonkhano umene anautcha kuti “msonkhano wochitidwa chifukwa chofuna kupeza mankhwala oloŵa m’malo mwa kuika munthu magazi.”

Polongosola kufunika kwa msonkhanowo, Vorobiev anakamba mwatsatanetsatane “mavuto akuluakulu amene amapezeka chifukwa choika anthu magazi.” Iye analongosola kuti chifukwa choikidwa magazi, ana ambiri odwala matenda oletsa magazi kuundana munthu akadzitema otchedwa hemophilia atenga matenda a AIDS m’mayiko monga United States, Japan, ndi Germany. Kenaka atapereka chiŵerengero choonetsa kufalikira kwa matenda a kutupa chiŵindi kudzera m’kuika anthu magazi, anadandaula motere: “Ziŵerengero zake n’zodabwitsa kwabasi. Onse amene akudwala matenda a hemophilia ali ndi matenda a kutupa chiŵindi.”

Poyamba a zachipatala ankaganiza kuti ngati munthu “wataya magazi lita imodzi, ndiye kuti iyenera kubwezeretsedwa ndi lita ina ya magazi,” Vorobiev anatero. Koma “n’kulakwitsa kwabasi!” M’mawu ake omaliza potsegulira msonkhanowo anati: “Tonse tinkavomereza kuti anthu aziikidwa magazi, koma tsopano tisiyanso maganizo akale ameneŵa limodzi.”

Madokotala ambiri amene anabwera ku msonkhanowo anali a ku Russia komweko, koma panalinso ena amene anakambapo nkhani ochokera ku France, Sweden, Belgium, ndi United States. Kuphatikiza pa kulongosolapo kusintha kwina ndi kwina kumene kwachitidwa poyesa kuchepetsa kutaya magazi mogwiritsa ntchito mankhwala ena m’malo mwa magazi, madokotalawo anatchulapo za kuopsa kwa kuika munthu magazi, kuphatikizaponso kuwonongeka kwakukulu kwa chitetezo cha thupi kumene kungachitike.

Kusonyezedwa pa Wailesi Yakanema

Wailesi yakanema yaboma ya ku Russia, imene imaoneredwa ndi anthu opitirira 235 miliyoni, inafotokoza mwatsatanetsatane zimene zinachitika kumsonkhanowo. Muulutsi, Elena Malysheva, analongosola motere: ‘Madokotala otchuka komanso ena odziŵika padziko lonse, madokotala ogonetsa tulo pochita munthu opaleshoni, ndi akatswiri a zamagazi anakumana ku Moscow kudzayankha funso ili: Kodi munthu angachitidwe opaleshoni popanda kumuika magazi?’

Elena anauza amvetseri ake pawailesi yakanemayo za matenda amene angathe kufalitsidwa ndi magazi ndiyeno analongosola motere: “N’zimene zinachititsa madokotalawa kuyesa kupeza njira ina. Ndipo inapezekadi. Anaitcha opaleshoni yopanda magazi. Munthu aliyense amene akufuna kukachitidwa opaleshoni angakambirane ndi dokotala wake za mtundu wa opaleshoni yopanda magazi imene iye akufuna.”

Ndipo pamene Andrey Vorobiev anaonekera pakanemayo, iye anati: ‘Magazi otengedwa m’thupi mwa munthu wina amakhala ndi maproteni amene amakhala achilendo m’thupi la munthu wopatsidwayo ndipo angachititse matenda osadziŵika bwino komanso amene munthu sangapeŵe. Kuwonjezera apo, ngakhale titayesetsa bwanji, wopereka magazi angathe kupatsira wodwala tizilombo toyambitsa matenda amene amakhala nawo ndi amenenso ifeyo sitingathe kuwaona’. Ndiyeno anamaliza ndi mawu akuti: ‘Tiyenera kuchepetsa kuika anthu magazi otengedwa kwa anthu ena.’

Amenenso anaonekera pa pologalamuyo anali Jean-François Baron, mkulu wa zopereka mankhwala oletsa kupweteka pochita opaleshoni komanso wa mawodi a matenda akayakaya ku chipatala cha Broussais, mu mzinda wa Paris, ku France. Analongosola kuti: “Kuchipatala chimene ndimagwirako ntchito tinatulukira mankhwala apadera amadzi amene amatha kutenga mpweya wa okosijeni. Mankhwala onseŵa ali ngati magazi koma alibe maselo ofiira alionse a m’magazi [amene angapatsire munthu matenda]. Iye ananeneratu kuti: “M’tsogolo muno njira zimenezi zidzagwiritsidwa ntchito nthaŵi zonse.”

Zimenezi zinachititsa muulutsiyo kukambapo za polofesa wina wa ku Russia, Felix F. Beloyartsev, amene zaka 20 zapitazo anatulukira mankhwala amadzi otha kutenga okosijeni, m’malo mwa magazi. Iye anatchulapo kuti panthaŵiyo, zimene Beloyartsev anatulukirazi sizinaoneke ngati kanthu ndi anthu a zachipatala ndipo kuti iye “anadzipha chifukwa cha chizunzo chopitirira chimene chinabwera chifukwa cha zimene anatulukirazi.”

Kulembedwa m’Nyuzipepala za Zachipatala

Nyuzipepala ya zachipatala yotchedwa Meditsinskaya Gazeta inakambaponso za msonkhanowo. Iyo inati: “Mfundo yaikulu imene agwirizanapo pa Msonkhanowu ndi iyi: N’kofunika kugwiritsa ntchito mankhwala ena m’malo mwa magazi paliponse pamene kuli kotheka ndipo kugwiritsa ntchito magazi kungalingaliridwe kokha ngati kuopsa kwake kutapendedwa bwinobwino mogwirizana ndi wodwala wakeyo ndiponso kokha ngati zinthu zafika poipa zedi.”

Nyuziyo inakambaponso za kuuma mtima kwa madokotala ena posamvera odwala akakana kulandira magazi. Mwachitsanzo, Mboni za Yehova sizilola kuikidwa magazi chifukwa cha langizo la m’Baibulo la ‘kusala mwazi.’ (Machitidwe 15:28, 29) Komabe, ponenapo za zimenezi, Michel de Guillenchmidt, polofesa wa zamalamulo wa ku France, akuti ananena kuti:

‘Tiyenera kuthokoza Mboni za Yehova chifukwa chakuti, mwa kuyambitsa nkhani imeneyi, zachititsa anthu kuzindikira ufulu umene zili nawo komanso zathandiza anthu onse a zachipatala kuzindikira kuopsa kwa kuika munthu magazi. Izinso zimalimbikitsa asayansi kupeza njira zina zapamwamba kwambiri zochitira opaleshoni yopanda magazi.’

Imodzi mwa nkhani zina m’nyuzipepala ya Meditsinskaya Gazeta inayamba ndi mawu oti: “Akuti kuika munthu magazi ndi kofanana ndi ukwati: Palibe munthu amadziŵa zotsatirapo zake.” Kenaka itanena kuti ‘magazi a munthu ali ngati chidindo cha chala cha munthu—palibe zala zokhala ndi chidindo chofanana,’ nyuzipepalayo inafunsa kuti: “Kodi masiku ano n’zotheka kukhala otsimikiza kotheratu kuti wodwala sapatsidwa matenda ngati aikidwa magazi?” Inayankha motere: ‘Ngakhale m’mayiko amene ali otsogola kwambiri pa zachipatala, mulibe njira zokhulupirika kotheratu zotha kupimira magazi.’

Nkhaniyo inatsiriza ndi kuti: ‘Choncho malingana ndi mmene nyumba ya msonkhanowo inadzadzira komanso chidwi choonekeratu chimene nthumwi zinasonyeza pa mavuto amene amakambidwa, tinganene kuti madokotala akusintha maganizo awo.’

Kupereka Thandizo

Panja pa holo imene amachitiramo msonkhanowo, Mboni za Yehova zinali ndi malo achionetsero pamene zinkapatsira madokotala nkhani zotengedwa m’nyuzipepala za zachipatala zonena za njira zina zochizira kutaya magazi m’thupi. Madokotala mazanamazana analandira nkhanizi.

Mwachionekere, ogwira ntchito zachipatala odziŵa zinthu akufuna kumachepetsa kugwiritsa ntchito magazi pochiza matenda.

[Zithunzi patsamba 26]

Mboni za Yehova zinapatsa madokotala mazanamazana nkhani zokhudza chidziŵitso chatsopano cha kafukufuku wokhudza magazi

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena