Kusokonezeka kwa Nyengo
M’NJIRA zosiyanasiyana, ambiri mwa ife timadalira mafuta ndi nkhuni zokhala ndi carbon. Timayendetsa magalimoto omwe amayendera petulo kapena dizilo. Timagwiritsira ntchito magetsi omwe amapangidwa ndi mainjini oyendera malasha, gasi, kapena mafuta. Timayatsa nkhuni, makala, gasi, ndi malasha kuti tiphikire kapena kuti tiothe. Zonsezi zimawonjezera mpweya wotchedwa carbon dioxide m’mlengalenga. Mpweya umenewu umagwira ndi kusunga kutentha kwa dzuŵa.
Timawonjezeranso mipweya ina m’mlengalenga yomwe imatenthetsa dziko. Mpweya wotchedwa nitrous oxide umachokera m’ feteleza wa nitrogen amene amamgwiritsira ntchito paulimi. Mpweya wa methane umachokera m’minda ya mpunga ndiponso malo odyetsera ng’ombe. Mipweya ya chlorofluorocarbon (CFCs) imapangika popanga zinthu zapulasitiki m’mafakitale ndi pochita ntchito zina za m’maindasitale. Mipweya ya CFC sikuti imangotenthetsa dziko chabe komanso imawononga muyalo wophimba dziko wotchedwa ozone.
Kuchotsapo mipweya ya CFC, imene tsopano ikutulutsidwa mosamala kwambiri, mipweya yotenthetsa dziko imatulutsidwa kupita m’mlengalenga mowonjezereka kwambiri. China chochititsa zimenezi ndi kuchuluka kwa anthu padziko, kuphatikizaponso kugwiritsira ntchito mafuta kowonjezereka, maindasitale ndiponso uchikumbe. Malinga ndi bungwe la Environmental Protection Agency la ku Washington, pali pano anthu amatulutsa matani mamiliyoni zikwi zisanu ndi chimodzi a mpweya wa carbon dioxide ndi mipweya ina yotenthetsa dziko kupita m’mlengalenga chaka chilichonse. Mipweya yotenthetsa dziko imeneyi siitherapo; ikhoza kukhala m’mlengalenga kwa zaka makumi ambiri.
Asayansi amatsimikiza kwambiri zinthu ziŵiri. Choyamba, m’zaka makumi kapena mazana aposachedwa, carbon dioxide ndi mipweya ina yotenthetsa dziko yachuluka kwambiri m’mlengalenga. Chachiŵiri, mkati mwa zaka zana lapitali, pa avareji kutentha kwapadziko kwawonjezeka ndi 0.3 kufika 0.6 digiri Celsius.
Pali funso lakuti, Kodi pali kugwirizana kulikonse pakati pa kutentha kwa dziko ndi mpweya womwe anthu amaupangitsa kupita m’mlengalenga? Asayansi ena amakana, akumati kutentha kumangochitika panyengo yake ndipo limachititsa ndi dzuŵa. Koma ambiri mwa odziŵa za nyengo amagwirizana ndi lipoti la bungwe la Intergovernmental Panel on Climate Change. Linanena kuti kutentha kwa dzikoku “nzokayikitsa kuti kumangochitika mwachilengedwe” ndi kuti “maumboni amasonyeza kuti anthu amachitapo kanthu kena komwe kamakhudza nyengo padziko lonse.” Komabe zakuti kaya anthu ndiwo akupangitsa kuti dziko litenthe sizinatsimikizike—makamaka kuti dziko lidzatentha mwamsanga chotani m’zaka za zana la 21 ndipo zotsatirapo zake zidzakhala zotani.
Mkangano Chifukwa cha Kukayikira Zamtsogolo
Odziŵa za nyengo akamanena za zomwe zidzachitika mtsogolo chifukwa cha kutulutsira mpweya wotenthetsa dziko m’mlengalenga, amadalira makompyuta opima za nyengo amakono ochita zinthu mofulumira ndipo amphamvu. Koma, nyengo padzikoli imachitika chifukwa cha zinthu zosiyanasiyana monga kuzungulira kwa dziko, mlengalenga, nyanja za mchere, ayezi, zinthu zosiyanasiyana zapadziko, ndi dzuŵa. Popeza pali zinthu zosiyanasiyana ndiponso dziko nlalikulu kwambiri, nzosatheka kuti kompyuta ipime bwino molondola zomwe zidzachitika zaka 50 kapena 100 kutsogolo. Posachedwa magazini a Science anati: “Odziŵa za nyengo amati sitidziŵa bwino ngati zochita za anthu zayamba kutenthetsa dziko—kapenanso kuti kutentha kochititsidwa ndi mipweya yotenthetsa dziko kudzakhala kotani kukadzayamba.”
Kukayikira zamtsogolo kumapangitsa kukhala kosavuta kunena kuti kulibe chovuta kutsogolo. Asayansi omwe amakayikira za kutentha kwa dziko pamodzi ndi a maindasitale omwe maso awo ali pa zachuma basi omwe amafuna kuti apitirize kukhala monga mmene alili leromu, amati zomwe anthu amadziŵa pali pano si zokwanira kupangitsa kuti pachitike ntchito yodya ndalama zambiri yowongolera zinthu. Iwo amati mwina mtsogolo simudzachitika zoipa monga mmene ena amaganizira.
Oona zachilengedwe amayankha mwa kunena kuti kusadziŵa zinthu motsimikizira kwa asayansi sikuyenera kupangitsa okhazikitsa malamulo kulephera kuchitapo kanthu. Pamene zili zoona kuti mwina mtsogolo nyengo siidzaipa monga mmene ena amaopera, nzothekanso kuti mwina zinthu zikhoza kudzaipa kuposa pamenepo! Kuwonjezera apo, amatinso pokhala zomwe zidzachitike mtsogolo sizidziwika sindiye kuti sipayenera kuchitika kanthu kuchepetsa tsoka lomwe likhoza kudzaoneka. Mwachitsanzo, anthu omwe amaleka kusuta fodya sayamba akapimitsa kwa dokotala kuti adziŵe ngati zaka 30 kapena 40 kutsogolo adzadwale kansa yam’mapapo. Amaleka chifukwa amazindikira za ngoziyo ndiye amafuna kuchepetsa kapena kuthetseratu mpata wodzadwala.
Kodi Pakuchitika Zotani?
Popeza pali mkangano waukulu chotero ponena za ukulu wa vuto la kutentha kwa dziko—ndiponso ngakhale zakuti kaya vutolo lilipo nkomwe—nzosadabwitsa kuti pali malingaliro osiyana ponena za zoyenera kuchita. Kwa zaka zambiri oona za chilengedwe akhala akulimbikitsa kuti anthu azigwiritsira ntchito zinthu zomwe siziwononga zachilengedwe. Nzotheka kugwiritsira ntchito mphamvu ya dzuŵa, mphepo, mitsinje, ndiponso mpweya ndi madzi otentha a pansi pa nthaka.
Oona zachilengedwe akhala akulimbikitsanso maboma kuti akhazikitse malamulo kuti anthu achepetse kutulutsa mpweya wotenthetsa dziko. Motero maboma akhala akusainirana mapangano. Mwachitsanzo, mu 1992, pamsonkhano wa Earth Summit ku Rio de Janeiro ku Brazil, nthumwi za maiko pafupifupi 150 zinasaina pangano kutsimikizira kuti achitapo kanthu kuchepetsa kutulutsa mpweya wotenthetsa dziko, makamaka carbon dioxide. Cholinga chinali chakuti m’chaka cha 2000, maiko okhala ndi maindasitale ochuluka azidzatulutsa mpweya wotenthetsa dziko monga mmene ankachitira m’chaka cha 1990. Ngakhale kuti oŵerengeka achitapo kanthu pa zimenezi, maiko ambiri olemera sanabwezeko nkomwe kuti afikitse pa mlingo umene anagwirizana. M’malo mochepetsako, maiko ambiri akuwonjezera kupanga mpweya wotenthetsa dziko wochuluka kuposa kale! Mwachitsanzo, mu United States kukuoneka kuti podzafika m’chaka cha 2000, kutulutsa mpweya wa carbon dioxide kudzakwera ndi 11 peresenti kuposa mmene zinalili m’chaka cha 1990.
Chaposachedwapa, analingalira zochitapo kanthu pa mapangano a maiko osiyanasiyanawa. M’malo monena zochepetsa monga mmene anagwirizanirana m’pangano la 1992, tsopano akupempha kuti agwirizane mlingo umene azitulutsa wa mpweya wotenthetsa dziko woti wina asapambanitse.
Mtengo wa Kusintha
Atsogoleri a ndale amafunafuna kumaonedwa monga mabwenzi a zachilengedwe. Komabe, amaonanso zomwe zingatsatirepo pa zachuma ngati patakhala kusintha. Malinga ndi magazini otchedwa The Economist, popeza 90 peresenti ya dziko imadalira mafuta okhala ndi carbon, kuti pakhale kusintha kuleka kuwagwiritsira ntchito kukhoza kupangitsa kuti zinthu zisinthe kwambiri; ndipo akadakambirana za mtengo wa kusinthako.
Kodi mtengo ukhoza kukhala wotani ngati atachepetsa kutulutsa mpweya wotenthetsa dziko ndi 10 peresenti poyerekezera ndi mmene zinaliri mu 1990 podzafika m’chaka cha 2010? Yankho la funso limenelo likhoza kudalira amene mwamfunsa. Lingalirani za mmene amaonera nkhaniyi ku United States, dziko limene limatulutsira mu mlengalenga mpweya wotenthetsa dziko wambiri kuposa ena onse. Mabungwe ofufuza zochitika m’maindasitale amachenjeza kuti kuchepetsa kumeneko kukhoza kuwonongetsa dziko la United States madola mabiliyoni ambiri chaka chilichonse ndi kupangitsa anthu okwana 600,000 kusoŵa ntchito. Motsutsana ndi zimenezo, oona zachilengedwe amati kusintha kumeneko kukhoza kupangitsa kuti ndalama madola mabiliyoni zisungike chaka ndi chaka ndiponso kupangitsa anthu ena okwana 773,000 kupeza ntchito.
Ngakhale kuti magulu oona zachilengedwe akhala akulankhulapo zakuti payenera kuchitika kanthu, pali maindasitale akuluakulu—okonza magalimoto, makampani a mafuta, ndi a migodi ya malasha, kungotchulapo oŵerengeka chabe—amene amagwiritsira ntchito ndalama zawo zambiri ndi mphamvu kupondereza nkhani yakuti dziko likutentha ndiponso kukokomeza zakuti ngati atasintha kuleka kugwiritsira ntchito mafuta a carbon ndiye kuti pakhoza kukhala mavuto a zachuma aakulu.
Makambitsirano adakali mkati. Komabe ngati anthu akupangitsa kuti nyengo isinthe ndiye osamachitapo kanthu koma kumangolankhula, mawu akuti aliyense amangolankhula za nyengo koma palibe aliyense amachitapo kanthu adzakhala ndi tanthauzo loopsa kwambiri.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 23]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Chitsanzo cha Mmene Dziko Limatenthera
Kutentha kwa Dziko: Mlengalenga wa dzikoli, mofanana ndi magalasi a nyumba yobzalamo mbewu mumasunga kuthentha kwa dzuŵa. Kuwala kwa dzuŵa kumatenthetsa dziko, koma kutentha kumene kumachitikako—komwe kumayenda monga infrared radiation—sikuchoka mwamsanga m’mlengalenga. M’malo mwake mpweya wotenthetsa dziko umatsekereza kutenthako ndipo ukumabwezera mbali ina padziko pompano, motero zikuwonjezera kutentha kwa dziko.
1. Dzuŵa
2. Infrared Radiation yotsekerezedwa
3. Mipweya yotenthetsa dziko
4. Radiation ikuchoka
[Bokosi pamasamba 24, 25]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Zinthu Zimene zimalamulira Nyengo
Kuti timvetsetse za makambitsirano amene aliko onena za kutentha kwa padziko lonse, tiyenera kumvetsetsa magwero amene amapangitsa kuti nyengo ikhale mmene ilili. Tiyeni tingoonapo zofunika kwambiri zokha.
1. Dzuŵa—Magwero a Kutentha ndi Kuwala
Moyo padziko umadalira ng’anjo ya nyukiliya yomwe timaitcha dzuŵa. Pokhala dzuŵa nlalikulu kuposa dziko lathuli kuŵirikiza nthaŵi miliyoni, nlodalirika monga magwero a kutentha ndi kuwala. Ngati dzuŵa litangochepetsako pang’ono kutentha kwake dziko lathuli likhoza kukutidwa ndi ayezi; litangowonjezera pang’ono dziko likhoza kupsa. Popeza dziko limazungulira dzuŵa pa mtunda wa makilomita 150,000,000 miliyoni, limalandira chabe theka la kachigawo kamodzi mwa zigawo biliyoni za mphamvu imene limatulutsa. Komabe, imeneyo ndiyo mphamvu yoyenera yeniyeni kuti pano pakhale nyengo kwakuti pakhoza kukhala zamoyo.
2. Mlengalenga—Bulangeti Lofunditsa Dziko Mwakuliphimba
Si kuti ndi dzuŵa lokha limene limapangitsa padziko kutentha kapena kuzizira; mlengalenga wathu nawonso uli ndi ntchito. Dziko ndi mwezi zili pamtunda umodzimodzi kuchokera ku dzuŵa, motero zonsezo zimalandira kutentha kofanana kuchokera ku dzuŵa. Komabe, ngakhale kuti pa avareji temperecha pano padziko ndi 15 digiri Celsius, pamwezi mpozizira kwambiri mwakuti avareji yake ndi -18 digiri Celsuis. Nchifukwa ninji pali kusiyana? Dziko lili ndi mlengalenga; koma mwezi ayi.
Mlengalenga wathuwu—chovala cha dziko lathuli chopangidwa ndi oxygen, nitrogen, ndi mipweya ina—mumasunga kutentha kwina kwa dzuŵa ndipo mumalola kotsalako kupita. Zimenezi amaziyerekezera ndi zochitika mu greenhouse. Monga mmene mumadziŵira greenhouse, ndi nyumba yokhala ndi zipupa ndi denga za magalasi kapena pulasitiki. Kuwala kwa dzuŵa kumaloŵa mosavuta ndi kutenthetsa mkatimo. Komabe panthaŵi yomweyo denga ndi zipupa zakezo zimapangitsa kuti kutentha kuzichoka pang’onopang’ono.
Momwemonso, mlengalenga wathu umalola dzuŵa kutenthetsa dziko. Dziko limabwezera kutenthako m’mlengalenga monga infrared radiation. Mbali yaikulu ya kutentha kumeneko sikupita kutali kunja kwa dziko chifukwa mipweya ina imagwira kutenthako ndi kukubwezera padziko, zikumapangitsa dziko kuwonjezereka kutentha. Kutentha kumeneku kumatchedwa kuti (greenhouse effect). Kudakakhala kuti mlengalenga wathuwu siugwira kutentha mwanjira imeneyi, dziko likadakhala lopanda zamoyo monga mmene palili pamwezi.
3. Nthunzi ya Madzi—Mpweya Wofunika Potenthetsa Dziko
Maperesenti okwana 99 a mlengalenga wathu ndi opangidwa ndi mipweya ya mitundu paŵiri: nitrogen ndi oxygen. Ngakhale kuti mipweya imeneyi imathandiza kwambiri pantchito zochirikiza moyo padziko, siikhudza mwachindunji kusinthasintha kwa nyengo. Ntchito yosintha nyengo imatsalira mbali yomwe ndi peresenti imodzi yokha ya mlengalenga yomwe ndiyo mipweya yotenthetsa dziko monga nthunzi ya madzi, carbon dioxide, nitrous oxide, methane, chlorofluorocarbons, ndi ozone.
Mpweya womwe uli patsogolo kwambiri kutenthetsa dziko ndi—nthunzi ya madzi—siilingaliridwa monga mpweya nkomwe, popeza timalingalira za madzi monga mmene amakhalira asanaume. Koma molekyu ya nthunzi ya madzi iliyonse ikakhala m’mlengalenga imakhala yotentha. Mwachitsanzo, nthunzi ya madzi m’mitambo imazizira ndi kugwirana kusanduka madzi, kutenthako kumachoka, zikumapangitsa kuyenda kwa mphepo kwa mphamvu. Kuyenda kwa nthunzi ya madzi m’mlengalenga kumachititsa kusintha kwakukulu ponena za mmene kuchere ndi mmene nyengo ikhalire.
4. Carbon Dioxide—Wofunika pa Moyo
Mpweya umene umatchulidwa kwambiri pa nkhani ya kutenthetsa dziko ndi carbon dioxide. Nkulakwa kunena kuti carbon dioxide amangoipitsa chilengedwe. Carbon dioxide ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kuti pachitike photosynthesis, njira imene zomera zobiriŵira zimapangira chakudya chawo. Anthu ndi zinyama amapuma oxygen ndi kutulutsa carbon dioxide. Mbewu zimapuma carbon dioxide ndi kutulutsa oxygen. Kunena zoona ndi chimodzi cha zinthu zimene Mlengi anazipereka zimene zimapangitsa kuti moyo ukhalepo padziko lapansi.a Komabe, carbon dioxide akachulukitsa m’mlengalenga zingafanane ndi kufunda mabulangeti ambiri. Akhoza kupangitsa kutentha kwambiri.
Zinthu Zosiyanasiyana Zopangitsa Nyengo
Si kuti dzuŵa ndi mlengalenga ndizo zokha zimapangitsa nyengo. Zinanso ndi nyanja za mchere ndi ayezi woundana m’malo ena, miyala ya m’migodi yopezeka pamtunda ndi zomera, zamoyo ndi malo awo okhala, mmene makemikolo amakhudzira zomera ndi nyama, mmene dziko limazungulirira dzuŵa. Kupenda zanyengo kumakhudza mitundu yonse ya sayansi yapadziko.
Dzuŵa
Mlengalenga
Nthunzi ya madzi (H20)
carbon dioxide (CO2)
[Mawu a M’munsi]
a Pafupifupi zamoyo zonse padziko zimapeza mphamvu zake pa zinthu zokhala ndi carbon, motero zimadalira pa kuwala kwa dzuŵa mwachindunji kapena mosakhala mwachindunji. Komabe pali zinthu zina zimene zimakula mumdima pansi pa nyanja za mchere zikumapeza chakudya kuchokera ku makemikolo opanda carbon. M’malo mochita photosynthesis, zinthu zimenezi zimagwiritsira ntchito njira yotchedwa chemosynthesis.