Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 5/8 tsamba 5-8
  • Zimene Tifunikira Kudziŵa Ponena za Magulu Aupandu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Tifunikira Kudziŵa Ponena za Magulu Aupandu
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chimene Amaloŵera m’Magulu Aupandu
  • Nkovuta Kutulukamo
  • Nkotheka Kukhala ndi Moyo Wabwino
  • Kodi Ndiyenera Kuphatikana ndi Gulu?
    Galamukani!—1991
  • Kodi Ndingadzichinjirize Motani ku Kuukiridwa ndi Gulu?
    Galamukani!—1991
  • Kutetezera Ana Athu ku Magulu Aupandu
    Galamukani!—1998
  • Mliriwo Ufalikira
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 5/8 tsamba 5-8

Zimene Tifunikira Kudziŵa Ponena za Magulu Aupandu

Wade, amene anali m’gulu laupandu ku California, anati: “Tinali chabe anyamata amene tinali kukhala dera limodzi. Tinayambiranso sukulu limodzi. Kokha kuti zomwe tinkasankha kuchita sizinali zabwino.”

KAŴIRIKAŴIRI magulu aupandu amayamba ngati chabe timagulu ta anthu a m’dera limodzi. Anthu amene anali kutha msinkhu kumene kapenanso ocheperapo ankakonda kumacheza pamphambano pa njira. Ankachita zinthu pamodzi ndipo kenaka anagwirizana kuti adzitetezere ku gulu lina limene linali litapangidwa kale chapafupi nawo. Koma mosakhalitsa gulu lawo linayamba kukhala ndi mamembala achiwawa kwambiri, ndipo linayamba kuchita zaupandu zoopsa kwambiri.

Gulu lina laupandu la mumsewu wina linaona gulu latsopanoli ngati mdani wawo. Mkwiyo unayambitsa chiwawa. Ozembetsa mankhwala osokoneza bongo analigwiritsira ntchito gululi kugulitsa mankhwala oletsedwawo. Kenaka linayamba kuchitanso zinthu zina zaupandu.

Luis anali ndi zaka 11 pamene anzake anapanga gulu laupandu. Ali ndi zaka 12 zakubadwa anayamba kumwa mankhwala osokoneza bongo. Ali ndi zaka 13 anamangidwa kwa nthaŵi yoyamba. Ankaba nawo magalimoto, kuthyola nyumba za anthu, ndiponso kuba moopseza ndi mfuti. Anali kabwerebwere kundende chifukwa chopezeka m’ndewu za magulu aupandu ndi m’zipolowe.

Nthaŵi zina tingadabwe ndi anthu amene ali m’magulu aupandu. Martha, mtsikana wooneka bwino, wophunzira wa kusekondale wochita bwino, anali kupeza malikisi abwino ndipo anali ndi khalidwe labwino pasukulu. Komatu, anali mtsogoleri wa gulu lina limene linali kugulitsa chamba, heroin, ndi cocaine. Anadzasintha moyo wakewo atachita mantha poona kuti mnzake wina anawomberedwa nthaŵi zingapo ndi kuphedwa.

Chimene Amaloŵera m’Magulu Aupandu

Nzachisoni kuti anthu ena amati adaloŵa gulu laupandu potsata chikondi. Anali kufuna utsamwali, unansi wathithithi umene sanaupeze panyumba pawo. Nyuzipepala ya Die Zeit ya ku Hamburg, Germany, inati m’magulu ochita zaupandu m’misewu achinyamata amafuna kupezamo chisungiko chimene sangachipeze kulikonse. Eric, yemwe anali m’gulu laupandu, anati ngati sakukonda panyumba panu, “umakafuna kwina oti nkukukonda.”

Mwamuna wina yemwe anali m’gulu laupandu analemba zimene ankachita pamene anali mnyamata: “Ndinali kupitapita kundende chifukwa cha khalidwe losayenera, ndewu za magulu aupandu, zipolowe ndipo potsirizira pake kufuna kupha munthu pomuwombera tikudutsa m’galimoto.” Kenaka, pamene anadzakhala ndi mwana wake wa mwamuna Ramiro, sanali kucheza naye kwenikweni. Pamene Ramiro anakula, nayenso analoŵa gulu laupandu, ndipo anamangidwa ndi apolisi atachita nawo ndewu ya magulu aupandu. Pamene atate ake anamkakamiza kuti achokemo m’gululo, anakalipa kuti: “Tsopano amenewo ndiwo apabanja langa.”

Nesi wina wa pachipatala china chake ku Texas, atalankhula kwa nthaŵi yoposa pang’ono chaka chimodzi ndi achichepere 114 omwe anali atawomberedwapo mfuti, anati: “Nzodabwitsa. Sindikumbukira ngati ndinamvapo wina wa iwo akufuna amayi ake kapena mbale wake wina aliyense.”

Komatu, si ana okha a m’madera osauka a tauni amene amaloŵa m’magulu aupandu. Zaka zingapo zapitazo, magazini ya ku Canada yotchedwa Maclean’s inati apolisi anati apeza achichepere okhala m’dera la anthu opeza bwino kwambiri ndiponso okhala m’dera la anthu osauka kwambiri la mzinda wina ali m’gulu laupandu limodzi. Achinyamata ochokera m’mabanja osiyanasiyana amenewa amapanga kagulu kawo ncholinga chimodzi—amafunafuna kugwirizana kwa pabanja kumene sanakupeze kunyumba kwawo.

M’madera ena achinyamata amakula ndi malingaliro akuti nkoyenera kuloŵa m’gulu laupandu. Fernando wazaka 16 anati: “Amaganiza kuti kuloŵa m’gulu laupandu kudzawathandiza kuthetsa mavuto awo. Amati: ‘Ndidzapeza mabwenzi. Iwo ndi akuluakulu ndiponso amakhala ndi mfuti. Adzanditeteza, ndipo palibe amene azindivuta.’” Koma mamembala atsopano a gulu laupandu mosakhalitsa amazindikira kuti iwo ndi amene adani a gululo tsopano akufuna kuthana nawo.

Kaŵirikaŵiri magulu aupandu amapezeka m’madera omwe muli ndalama zochepa koma mfuti zambiri. Malipoti akuti m’mizinda ina ikuluikulu m’kalasi mumapezeka kuti ophunzira aŵiri mwa atatu alionse amakhala m’banja la kholo limodzi. Mwina kholo la wophunzirayo ndi womwerekera ndi zoledzeretsa amene angagonerere kwina, ndipo wophunzirayo amafunika kukasiya mwana wake amene alibenso atate ake kumalo olerera ana iye asanapite kusukulu mmaŵa.

Kazembe wa ku California Pete Wilson, anati: “Tili ndi vuto lalikulu chifukwa ana ambiri akukula opanda atate awo, opanda munthu wamwamuna woti aziwasonyeza chikondi, kuwatsogolera, kuwalanga ndi kuwauza makhalidwe abwino—osazindikira chifukwa chake ayenera kudzilemekeza kapenanso kulemekeza anthu ena.” Iye anati achinyamata ena “amaoneka kuti angaphulitse munthu [kumupha ndi mfuti] popanda chisoni mpang’ono pomwe” chifukwa cha kukhala kwawo osamvera ena chifundo.

Ngakhale kuti kusoŵeka kwa kugwirizana m’banja, kuphunzitsidwa, ndi chitsanzo chabwino cha khalidwe labwino ndi zochititsa zazikulu za kukula kwa magulu aupandu, palinso zinthu zina. Zimenezi ndi monga maprogramu a pa TV ndi mavidiyo amene amaonetsa chiwawa ngati njira yapafupi yothetsera mavuto, anthu amene kaŵirikaŵiri amati osauka ngolephera nkumawakumbutsa nthaŵi ndi nthaŵi kuti sangathe kuchita zimene ena amachita, ndi kuwonjezereka kwa mabanja a kholo limodzi m’mene mayi wachisungwana wogwira ntchito mopanikizikayo amayenera kulimbapo kuti asamalire mwana kapena ana ake amene sayang’aniridwa. Zochititsa zingapo zimenezi kapena zonsezi, mwina ndi zinanso, zapangitsa kufalikira kwa mliri wapadziko lonse wa magulu ochita zaupandu m’misewu.

Nkovuta Kutulukamo

Nzoona kuti anthu ena atakhala m’gulu laupandu kwa kanthaŵi amachoka nkukagwira ntchito zina. Ena angakakhale ndi achibale ena kudera lina nasiyana nawo moyo waupandu. Koma kaŵirikaŵiri nkovuta kutuluka m’gulu laupandu.

Kaŵirikaŵiri anthu aupandu amamenyedwa mwa nkhanza ndi mamembala anzawo angapo kuti awalole kuchoka ali amoyo. Ndipotu, anthu ena amene anafuna kutuluka m’magulu ena aupandu anali kuwomberedwa. Anali kuloledwa kuchoka ngati sanafe! Kodi kutuluka m’gulu laupandu kumayenerera kuzunzidwa konseko?

Munthu wina amene anali m’gulu laupandu anapereka chifukwa chake anafuna kutulukamo: “Anzanga asanu anafa kale.” Zoonadi, moyo wa munthu amene ali m’gulu laupandu ungakhaledi pachiswe. Magazini a Time anasimba za membala wa gulu lina laupandu ku Chicago kuti: “Mu ntchito yake ya zaka zisanu ndi ziŵiri, wakhala atawomberedwapo pamimba, kumenyedwapo m’mutu ndi zomangira njanji, anathyokapo dzanja pandewu ndi kumangidwa kaŵiri chifukwa choba galimoto . . . Koma tsopano popeza kuti anatuluka m’gululo, ngakhale amene anali anzakewo akufuna kuthana naye.”

Nkotheka Kukhala ndi Moyo Wabwino

Eleno, wa ku Brazil, anali m’gulu la Headbangers, gulu laupandu limene linali kuchita ndewu ya mipeni ndipo nthaŵi zinanso ya mfuti. Anali kudzimva kukhala womanidwa, choncho ankakhutiritsidwa nkuswa zinthu ndi kuukira anthu. Mnzake wa kuntchito anakamba naye za Baibulo. Kenako Eleno anakapezeka pamsonkhano wa Mboni za Yehova kumene anakumanako ndi anzake ena amene anachoka m’gulu lakelo ndi wina yemwe anali m’gulu lodana nalo. Anapatsana moni ngati pachibale—zosiyana kwambiri ndi mmene zikanakhalira nthaŵi za m’mbuyomo.

Kodi zimenezi zimachitikadi? Inde zimachitikadi! Posachedwapa woimira magazini ya Galamukani! anacheza ndi omwe anali mamembala a magulu akuluakulu aupandu ku Los Angeles amene tsopano akutumikira ndi mipingo ya Mboni za Yehova. Atacheza kwa maola ochuluka, mmodzi wa iwo anasiya kaye kulankhula, naŵeramuka, ndipo anati: “Taonani! Omwe anali a Bloods ndi a Crips ali pano okondana ngati pachibale!” Iwo anavomereza kuti kusintha kwawo kuchoka pa anthu ankhanza m’gulu laupandu ndi kukhala anthu achifundo ndi achikondi kunachitika chifukwa chakuti anaphunzira mapulinsipulo aumulungu mwa kuphunzira Baibulo mosamalitsa.

Kodi izi zingachitikedi mu ma 1990? Kodi anthu aupandu angasinthedi motero tsopano? Angathe ngati ali ofunitsitsa kupeza chilimbikitso champhamvu choperekedwa ndi Mawu a Mulungu ndipo kenaka nkugwirizanitsa miyoyo yawo ndi mapulinsipulo a Baibulo. Ngati ndinu membala wa gulu laupandu, bwanji osalingalira zosintha?

Baibulo limatilimbikitsa kuti “muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale” ndi kuti “nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.” (Aefeso 4:22-24) Kodi umunthu watsopano umenewo umabwera bwanji? Baibulo limati, “mwa chidziŵitso cholongosoka,” (NW), munthu ‘angakonzedwe watsopano . . . monga mwa chifaniziro cha [Mulungu] amene anamlenga.’—Akolose 3:9-11.

Kodi nkoyenerera kuyesa kusintha? Ee, nkoyeneradi! Ngati ndinu membala wa gulu laupandu, mwinamwake mudzafunika chithandizo kuti mukhoze kusintha. Alipo anthu m’dera lanu amene adzakhala okondwa kukuthandizani. Komatu, makolo ndi amene angakhoze bwino kupangitsa ana awo kukhala ndi maganizo abwino kwambiri. Choncho tsopano tidzalingalira zimene makolo angachite kuti atetezere ana awo kuti asakhale m’magulu aupandu.

[Chithunzi patsamba 7]

Mamembala akale a magulu aupandu odana tsopano ngoyanjanitsidwa ndi choonadi cha Baibulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena