Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 1/8 tsamba 23-25
  • Kodi Madansi a Rave ndi Zosangulutsa Zabwino?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Madansi a Rave ndi Zosangulutsa Zabwino?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupenda Madansi a Rave
  • Kuipa kwa Madansi a Rave
  • Kodi Muyeneradi Kuvina Dansi ya Rave?
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amagwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Galamukani!—2001
  • Kodi N’kulakwa Kupita ku Malo Ovinira a Achinyamata?
    Galamukani!—2004
  • Achinyamata—Kanani Mzimu wa Dziko
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Mumasankha Nyimbo Mwanzeru?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 1/8 tsamba 23-25

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Madansi a Rave ndi Zosangulutsa Zabwino?

“Ndikamavina manja anga ali m’mwamba ndipo nyimbo ikungoloŵerera m’thupi mwanga, ndimalimbikitsidwa ndi ena omwe akuvina m’bwalo. Zimangokhala ngati ukulota.”—Gena.

MOTERO Gena akulongosola momwe kupita ku dansi ya rave kumasangalatsira. Madansiŵa, omwe nthaŵi zonse amachezera, anatchuka choyamba ku Britain m’ma 1980. Tsopano akuchitika kumbali zonse za dziko, kuphatikizapo ku Belgium, Canada, Germany, India, New Zealand, South Africa, ndi ku United States.

Madansi a rave amachitikira m’manaiti kalabu, nyumba zosungira katundu zomwe analeka kuzigwiritsira ntchito, pa mabwalo opanda kanthu—paliponse pomwe anthu angasonkhanepo, kumavina mosalamulirika osalekeza usiku wonse. “Pang’onopang’ono achinyamata akukonda kusanguluka ndi madansi a rave kuposa manaiti kalabu,” analemba motero Adam Levin mu Sunday Times Magazine ya ku Johannesburg, South Africa. “Ngati mwana wanu wachinyamata sananenepo zimenezi,” iye akuwonjezera motero, “ndiye kuti simukambitsirana naye bwino.”

Kupenda Madansi a Rave

Nthaŵi zina madansi a rave amakhala achinsinsi, malo ake sawanena kufikira tsiku lomwe achitikelo. Komabe, kukangoyamba kuwala magetsi ndi nyimbo zamaliridwe oguguda zotchedwa techno zikamaimba, kumabwera achinyamata ambiri kuyambira pa makumi oŵerengeka kufika mwina mpaka zikwizikwi atavala mosayenera. “Zimakhala ngati gulu limodzi la anthu likuvina likumasonyeza mphamvu zawo malinga ndi momwe nyimbo ikuimbira,” akutero Katy, wophunzira m’kalasi lachiŵiri pakoleji.

Komabe, rave si dansi chabe. Ndi chikhalidwe, kapena monga mmene ovina rave amanenera, ndi “scene.” Mfundo zazikulu zimene amakhulupirira ku rave ndizo mtendere, chikondi, umodzi, ndi ulemu—mosasankha mtundu, dziko, kapena mtundu wa kugonana kumene munthu amachita. “Timayesa kuphatikiza zikhalidwe pamadansi ameneŵa,” akutero mwini sitolo yomwe amagulitsamo nyimbo zapamadansi. “Cholinga ndicho umodzi,” akuwonjezera motero, “ndipo kuvinira pamodzi ndiyo njira yothandiza kwambiri yochitira zimenezo.”

Polingalira za zolinga zimenezi zooneka ngati zabwino, mungafunse kuti, ‘Chingakhale cholakwika nchiyani ndi rave?’ Koma pali zinanso zokhudza madansi a rave zimene muyenera kulingalira.

Kuipa kwa Madansi a Rave

Ena amati pa rave sikaŵirikaŵiri kumwa zoledzeretsa. Komabe, mankhwala osokoneza bongo amakhalapo ambiri. “Nzodabwitsa ngati anthu ambiri akadaikonda rave ngati pakadakhala palibe mankhwala osokoneza bongo,” akuvomereza motero wovina rave wotchedwa Brian. “Ndithudi,” iye akuwonjezera motero, “ena ambiri amadabwa kuti madansi a rave akadakhalako bwanji popanda mankhwala ameneŵa.”

Ngakhale kuti chamba ndi LSD nazonso zimapezeka pa madansi a rave ena, mankhwala omwe ovina rave amakonda kwambiri amaoneka ngati ndi MDMA, amene ambiri amawadziŵa ndi dzina lakuti Ecstasy. Omwe amamwawo amati Ecstasy aliko bwino. Iwo amaumirira kuti amangowapatsa chabe mphamvu kuti avine usiku wonse ndi kuti amathandiza kuti asangalale. Koma pansi pa mutu wakuti “Mankhwala Ofala Akhoza Kuwononga Bongo,” The New York Times inanena kuti Ecstasy “angathe kusokoneza kwa nthaŵi yaitali chilakolako chakudya, tulo, mkhalidwe wanu, kufatsa kwanu, ndi ntchito zina za maganizo anu.” Koma si zokhazo. “Ena afapo naye Ecstasy,” akutero Dr. Howard McKinney, “ndipo pali ambiri omwe anamwa motsatira malangizo koma mtima wawo ndi chiŵindi zinaleka kugwira ntchito kapena anakomoka.” Ndi zifukwa zabwino Dr. Sylvain de Miranda anati: “Ovina rave omwe amamwa Ecstasy amavina ndi imfa.”

Ngakhale mankhwala azitsamba—Herbal Acid, Acceleration, Ecstasy wazitsamba, kapena Rush—akhoza kuvulaza. Mwachitsanzo, zikumveka kuti zikayenda mwina, mankhwala azitsamba monga acceleration amapangitsa mtima kuleka kugwira ntchito ndipo mwina imfa.

Aja amene akuumirira kuti mankhwala osokoneza bongo omwe amagwiritsira ntchito pa madansi a rave ndi osavulaza ayeneranso kulingalira kanthu kena. Wapolisi wa ku Canada ditekitivi Ian Briggs anati 90 peresenti ya mankhwala omwe amagulitsidwa monga Ecstasy sakhaladi Ecstasy. “Ambiri a iwo amakhala PCP kapena mankhwala ena oopsa,” iye akutero. “Anthu omwe amagulitsa mankhwalaŵa si okhulupirika. Sakhalapo pamene mankhwalawo ayamba kugwira ntchito.”a

Zikhoza kutheka kuti pa madansi a rave ena mwina sipakhala mankhwala osokoneza bongo. Komabe, ngakhale ovina rave amavomera kuti kaŵirikaŵiri sizidziŵika kuti kaya wina, kaya angapo, kaya ambiri zedi mwa amene abwera padansi ya rave amwa mankhwala oletsedwawo.

Kodi Muyeneradi Kuvina Dansi ya Rave?

Palibe cholakwa kwenikweni kuimba ndi kuvina, komanso si kulakwa kusangalalako nthaŵi zina. Ndipo Baibulo limanena kuti pali “nthaŵi yachisangalalo” ndi “nthaŵi yakuvina.” (Mlaliki 3:4, Today’s English Version) Limalimbikitsanso kuti: “Kondwera ndi unyamata wako.” (Mlaliki 11:9) Motero Mlengi amafuna kuti muzisangalala! Komabe, muyenera kukumbukira kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Motero, siziyenera kutidabwitsa kuti zosangulutsa zomwe dziko limakonda zimaphatikizapo zinthu zina zoipa.

Mwachitsanzo, talingalirani za amene amakavina dansi ya rave. Kodi amatsatira chenjezo la Baibulo lakuti ‘aleke chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu’? (2 Akorinto 7:1) Nzoonadi kuti ovina rave angamakonde mtendere, chikondi, ndi umodzi. Koma ‘nzeru yotsika kumwamba’ si “mtendere” chabe; ndi “yoyera.” (Yakobo 3:15, 17) Dzifunseni kuti, ‘Kodi khalidwe la okonda kuvina madansi a rave limagwirizana ndi malamulo opezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo? Kodi ndikufunadi kuchezera usiku wonse ndi “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu”?’—2 Timoteo 3:4; 1 Akorinto 6:9, 10; yerekezerani ndi Yesaya 5:11, 12.

Awa ndi mafunso ofunika kwambiri kuwalingalira, chifukwa Paulo analemba kuti “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Kugwirizana ndi amene samvera malamulo a Mulungu potsirizira pake kudzatiloŵetsa m’mavuto, popeza Baibulo limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.”—Miyambo 13:20.

Kwenikweni, madansi ambiri a rave amakhala chabe mapwando a mankhwala osokoneza bongo ndipo amene amapitako akhoza kupeza mavuto. Mwachitsanzo, madansi ena a rave apolisi amawaukira ndi kuwathetsa, nthaŵi zina chifukwa chakuti akuchitidwa mosaloledwa ndi lamulo kapena chifukwa pali mankhwala osokoneza bongo. Kodi inu mukufuna kudziŵika monga mmodzi wa osamvera malamulo? (Aroma 13:1, 2) Ngakhale ngati sipanaphwanyidwe lamulo, kodi mungakhale pa madansi ameneŵa komabe “wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi?” (Yakobo 1:27) Popeza michezo, kapena “mapwando aphokoso” (Byington), zimaletsedwa m’Baibulo, kodi kupita kwanu ku dansi ya rave kudzakupangitsani kukhalabe ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu ndi anthu?—Agalatiya 5:21; 2 Akorinto 4:1, 2; 1 Timoteo 1:18, 19.

Ndithudi, Akristu ayenera kuchenjera ndi madansi a rave. Koma musataye mtima. Pali zosangalatsa zambiri zimene mungachite. Mwachitsanzo, mabanja ambiri a Mboni za Yehova amakhala ndi macheza oyenera.b Mwa kukonzekera ndi kuwayang’anira, ameneŵa amasiya onse opezekapo ali olimbikitsidwa mwauzimu ndi otsitsimulidwa kuthupi. Koposa apo, mayanjano omwe ali olimbikitsa amakondweretsa Yehova, “Mulungu wolemekezeka [“wachimwemwe,” NW],” amene amafuna kuti anthu ake azisangalala.—1 Timoteo 1:11; Mlaliki 8:15.

[Mawu a M’munsi]

a PCP (phencyclidine) ndi mankhwala oletsa munthu kumva kuŵaŵa pochita opaleshoni omwe nthaŵi zina amagwiritsidwa ntchito mosaloledwa ndi lamulo kuchititsa munthu kuona zideruderu.

b Ngati mufuna kumva zowonjezereka, onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1992, masamba 15-20, ndi Galamukani! ya June 8, 1997, masamba 22-4.

[Bokosi patsamba 24]

Kodi Techno Nchiyani?

Kunena mwachidule, techno ndi nyimbo zapadansi zoimbidwa pa zoimbira zamagetsi. Ndi zamaimbidwe osiyanasiyana. Anthu ambiri akhoza kunena kuti techno ndi za zing’wenyeng’wenye, chifukwa zimakhala ndi mabiti 115 kufika 160 pamphindi imodzi.

Nyuzipepala ya The European ikuti: “Kwa amene sanazoloŵere, techno imamveka ngati phokoso limene umamva kwa dokotala wa mano pamene akuboola dzino, kuphatikizapo phokoso limene mungayerekeze kuti linachitika mu Sodomu ndi Gomora tsiku limene zinawonongedwa.” Komabe, omvetsera ena, amatengeka ndi maliridwe osalekeza a techno. “Kwa ine,” akutero Christine wazaka 18, “nyimbo zimenezi zimandipangitsa kudzimva waufulu kwambiri ndiponso wodzidalira.” Nayenso ­Sonja amamva chimodzimodzi. “Poyamba,” iye akuvomereza, “sindinali kuzikonda nyimbo za techno. Koma pamene umazimvetsera kaŵirikaŵiri, mpamene umayamba kuzikonda. Ngati uzitsegula kwambiri, sunganyalanyaze maliridwe ake oguguda. Umangopezeka kuti ukuvina. Ngati susamala, nyimbozo zimakuloŵerera.” Shirley, wazaka 19, amaona kanthu kena pa nyimbo za techno. “Si nyimbo chabe,” iye akutero. “Zimakhudza moyo wako wonse ndipo zimaonekera pa kavalidwe ndi kalankhulidwe.”

Akristu ‘amayesa chokondweretsa Ambuye nchiyani.’ (Aefeso 5:10) Motero, ayenera kukhala osamala ndi techno monga mmene amachitira ndi nyimbo zina. Ngati muona kuti mukutengeka ndi techno, dzifunseni kuti: ‘Kodi nyimbo izi zimandikhudza motani? Kodi zimandipangitsa kukhala wosangalala, wabata, ndi wamtendere? Kapena zimandipangitsa kukhala wokwiya, mwina kundipangitsa kulingalira zoipa? Kodi kukonda kwanga nyimbo za mtundu uwu kudzandipangitsa kukhala ndi khalidwe limene zimanena? Kodi zidzandipangitsa kulakalaka kupita ku dansi ya rave kuti ndikamvere nyimbo zimenezi kapena kuvinako?’

Kwenikweni, mfundo yaikulu njakuti: Kaya mukonde nyimbo zotani, osazilola kuti zikhale chopinga pakati pa inu ndi Atate wanu wakumwamba.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena