Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 9/8 tsamba 5-8
  • Dziko Lophunzitsidwa Kudana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lophunzitsidwa Kudana
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyamba ndi Ana
  • Kodi Chipembedzo Chimaphunzitsanji?
  • Mantha, Mkwiyo, Kapena Kuopa Kuvulala
  • Kodi Udani Udzatha Konse?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Njira Yokhayo Yothetsera Chidani
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2005
  • N’chifukwa Chiyani Chidani Sichikutha?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 9/8 tsamba 5-8

Dziko Lophunzitsidwa Kudana

MWACHIBADWA anthu ngodzikonda. Ndipo kudzikonda, ngati sakulamulira, kungakule kukhala chidani. Anthu amaphunzitsana kudzikonda monga ngati kudzikondako si koipa kwambiri!

Inde, kunena mwachisawawa za anthu ena sikumakhala kanthu nthaŵi zina, komabe, mzimu wina umakhala wofala kwambiri koti sitingangounyalanyaza kuti ndimo mmene aliyense amachitira. Kodi andale samafunitsitsa kupambana chisankho kuposa kuthandiza anthu m’chigawo chawo? Kodi amalonda samafunitsitsa kupanga ndalama, mwaukatangale nthaŵi zina, koposa kuletsa katundu wangozi kufika pamsika? Kodi atsogoleri achipembedzo samafunitsitsa kutchuka kapena kupeza ndalama koposa kutsogolera nkhosa zawo panjira ya makhalidwe abwino ndi chikondi?

Kuyamba ndi Ana

Pamene ana awalera molekerera, kwenikweni amakhala akuwaphunzitsa kudzikonda, pakuti amanyalanyaza kulingalira ena ndi kusadzikonda natsata zikhumbo zawo zachibwana. Kusukulu ndi kukoleji, ophunzira amawaphunzitsa kukhala nambala wani, osati chabe pamaphunziro komanso pamaseŵera. Mwambi wawo ngwakuti, “Kukhala wachiŵiri sikusiyana nkukhala womaliza!”

Maseŵera apavidiyo amene amasonyeza chiwawa amaphunzitsa achinyamata kuthetsa mavuto mwanjira yodzikonda—kungomkonza mdani wako! Umenewo ndi mzimu wosalimbikitsa chikondi ngakhale pang’ono! Zaka zoposa khumi zapitazo, dokotala wamkulu wa ku United States anachenjeza kuti maseŵera apavidiyo akhoza kuwononga achinyamata. Iye anati: “Amangosonyeza mophulitsira mdani wako. M’maseŵera amenewo mulibe chothandiza chilichonse.” Kalata yolembedwa kwa a The New York Times inatero kuti maseŵera ambiri apavidiyo “amalimbikitsa munthu kukhala ndi makhalidwe onyansa koposa” ndipo inawonjeza kuti: “Amatulutsa mbadwo wa achinyamata osimbwa ndi ankhanza.” Wokonda maseŵera apavidiyo wa ku Germany moona mtima anavomereza kuti mawu omalizawa ngoona pamene anati: “Powaseŵera, ndinaloŵa m’dziko lamaloto landekha mmene mwambo wake unali wakuti: ‘Ipha mnzako ngati sapha iwe.’”

Chidani chitakumana ndi ufuko, ndiye chimakuliratu. Ndiye chifukwa chake Ajeremani mwachionekere akuda nkhaŵa ndi mavidiyo opangidwa ndi anthu osafuna kusintha amene amalimbikitsa chiwawa kwa akunja, makamaka Aturki. Ndipo ayeneradi kuda nkhaŵa, poti kuyambira January 1, 1994, Aturki anakwana 27.9 peresenti ya alendo 6,878,100 m’Germany.

Mzimu wa ufuko umalimbikitsa zimene utundu umaphunzitsa ana kuyambira ukhanda, ndiko kuti, kuda adani a dziko lako sikulakwa ayi. George M. Taber, wolemba nkhani m’danga la magazini ya Time, anapereka ndemanga yakuti: “Paziphunzitso zonse za ndale m’mbiri, mwinamwake utundu ndiwo [chiphunzitso] champhamvu koposa.” Anapitiriza kufotokoza kuti: “Mwazi wambiri wakhetsedwa m’dzina lake koposa m’dzina la china chilichonse kusiyapo chipembedzo. Pazaka zambiri atsogoleri olonjeza zosatheka asonkhezera magulu achiwawa mwa kunena kuti ochititsa mavuto awo onse ndiwo afuko lina lapafupi.”

Kudana ndi mafuko kapena mitundu ina kwa nthaŵi yaitali ndiko kwachititsa mavuto ambiri m’dziko lerolino. Ndiponso xenophobia, kuopa alendo kapena ochokera dziko lina, kukuwonjezeka. Zodabwitsa nzakuti kagulu ka ku Germany kofufuza za kakhalidwe ka anthu kanapeza kuti kumene amaopa alendo kwambiri ndi kuja komwe kuli alendo oŵerengeka. Zimenezi zikuchita ngati zikutsimikiza kuti kuopa alendo kaŵirikaŵiri kumakhalapo chifukwa cha malingaliro olakwika osati kuti pali zimene zinamchitikira munthuyo. “Amene makamaka amalimbikitsa achinyamata kukhala ndi tsankhu ndiwo mabwenzi awo ndi achibale,” nzimene anapeza ofufuza za kakhalidwe ka anthu. Inde, 77 peresenti ya amene anafunsidwa, ngakhale kuti anatchula za tsankhu, sanakumanepo ndi alendo, kapena anakumanapo ndi oŵerengeka okha.

Kuphunzitsa wina kudzikonda si nkhani yapatali ayi, pakuti tonsefe tinalandira mlingo wina wake wa kudzikonda kuchokera kwa makolo opanda ungwiro. Koma kodi chipembedzo chimachita ntchito yanji pamkangano womwe ulipowu wa chikondi ndi chidani?

Kodi Chipembedzo Chimaphunzitsanji?

Anthu ambiri amaganiza kuti chipembedzo chimalimbikitsa chikondi. Koma ngati chimatero, nchifukwa ninji kusamvana kwa zipembedzo kwachititsa mikangano ku Northern Ireland, Middle East, ndi India, kungotchula zitsanzo zitatu chabe? Zoona, anthu ena amati kusamvana pazandale ndiko kwachititsa chipwirikiti, osati zipembedzo ayi. Mfundo imeneyo njochititsa mkangano. Kaya zikhale motani, nkwachionekere kuti chipembedzo chokhazikika chalephera kukhomereza mwa anthu chikondi cholimba chokhoza kugonjetsa tsankhu la ndale ndi mafuko. Okhulupirira ambiri, Akatolika ndi Aorthodox limodzinso ndi a zipembedzo zina, kwenikweni amalekerera tsankhu, limene limayambitsa chiwawa.

Palibe cholakwa ndi kuyesa kutsutsa ziphunzitso ndi miyambo ya chipembedzo zimene munthu aganiza kuti nzolakwika. Koma kodi zimenezo zimampatsa ufulu wogwiritsira ntchito chiwawa polimbana ndi chipembedzocho kapena polimbana ndi anthu ake? The Encyclopedia of Religion inavomereza mosabisa kuti: “Atsogoleri a zipembedzo asonkhezera chiwawa mobwerezabwereza pa zipembedzo zina m’mbiri ya Near East ndi Ulaya.”

Insaikulopediya imeneyi ikuvumbula kuti chiwawa ndiwo mwambo wa chipembedzo, ikumati: “Ochirikiza chiphunzitso cha Darwin sali okha povomereza kuti kulimbana kumafunika kuti kakhalidwe ka anthu katukuke ndi kuti atseguke maso. Chipembedzo chayambitsa mikangano, chiwawa, ndiye mwanjira imeneyo, chayambitsa chitukuko.”

Sitinganene kuti chiwawa chili bwino pachifukwa chabe chakuti nchofunika kuti pakhale chitukuko, pakuti zimenezi zikuwombana ndi pulinsipulo lodziŵika kwambiri limene Yesu Kristu anakhazikitsa pamene mtumwi Petro anayesa kumtetezera. Koma pamene Petro “anatansa dzanja lake, nasolola lupanga lake, nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.”—Mateyu 26:51, 52; Yohane 18:10, 11.

Kuchita anthu ena chiwawa—kaya ali abwino kapena oipa—si njira ya chikondi. Ndiye chifukwa chake anthu amene amachita chiwawa amakhala akudzinamiza ponena kuti akutsanza chikondi cha Mulungu. Wolemba Amos Oz posachedwapa anati: “Ndi mmene zimakhalira kwa oyaluka ndi chipembedzo . . . kuti ‘malamulo’ omwe amalandira kwa Mulungu nthaŵi zonse ndi lamulo limodzi kwenikweni lakuti: Uzipha. Mulungu wa oyaluka ndi chipembedzo onse achita ngati ndi mdyerekezi.”

Baibulo limanena zofanana ndi zimenezo: “Mmenemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: yense wosachita chilungamo saali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziŵa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye. Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona. Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.”—1 Yohane 3:10, 15; 4:20, 21.

Chipembedzo choona chiyenera kutsatira njira ya chikondi, imene imaphatikizapo kukonda ngakhale adani. Za Yehova timaŵerenga kuti: “Amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:44, 45: onaninso 1 Yohane 4:7-10.) Wasiyana kwambiri ndi Satana, mulungu wa chidani! Satanayo amanyengerera ndi kukopa anthu kukhala ndi moyo wosadzisunga, waupandu, ndi wodzikonda, mwa kutero amadzaza moyo wawo ndi zopweteka ndi chisoni, uku akudziŵa bwino kuti moyo woluluzika umenewo udzawawonongetsa pomaliza pake. Kodi ameneyo ndiye mulungu woyenera kumtumikira, amene sangathe—ndipo mwachionekere safuna—kuteteza otsatira ake?

Mantha, Mkwiyo, Kapena Kuopa Kuvulala

Pali umboni wochuluka wakuti zinthu zimenezi zimayambitsa chidani. Lipoti la mu Time linati: “Makamaka kuyambira m’ma 1930 mpamene zipani zambirimbiri zokonda mwambo za ku Ulaya zadyerera mikhalidwe yooneka ngati mwaŵi. . . . Poopera ntchito zawo, anthu akukwiya ndi maboma ololera ndipo akunamizira alendo okhala pakati pawo.” Jörg Schindler, mu Rheinischer Merkur/Christ und Welt, anatchula za othaŵa kwawo zikwi makumi ambiri amene aloŵa m’Germany pazaka makumi aŵiri zapitazo. The German Tribune ikuchenjeza kuti: “Kuda anthu a fuko lina kukuwonjezeka mu Ulaya yense.” Kubwera kwa alendo ochuluka odzakhala m’dziko kukubutsa mzimu wa chidani. Anthu amveka akudandaula kuti: ‘Amatitayitsa ndalama, akutilanda ntchito zathu, ali angozi kwa ana athu aakazi.’ Theodore Zeldin, membala wa St. Antony’s College, Oxford, anatero kuti anthu “amachita chiwawa chifukwa cha mantha kapena manyazi. Zimene zimawakwiyitsa nzimene zifunikira kusamalira.”

Mtolankhani wa pawailesi yakanema ya ku Britain, Joan Bakewell, akugwiritsira ntchito mawu oyenera pofotokoza dziko lathu, limene limaphunzitsa anthu ake kudana. Akulemba kuti: “Sindine Mkristu wa chipembedzo chilichonse, koma nditha kuona choonadi chosakanika m’chiphunzitso cha Yesu: kuipa ndiko kusoŵeratu chikondi. . . . Ndikudziŵa kuti tikukhala m’dziko limene silimalola kwenikweni chiphunzitso cha chikondi. Inde, dziko lachimakono kwambiri moti limaona chiphunzitso ngati chimenecho kukhala chakale, maloto, chosatheka, limene limanyodola munthu wokonda kusamala ena ndi wosadzikonda amene sakonda phindu ndi zake zokha. ‘Tinenetu zoona,’ limatero pamene lipeza malonda atsopano, kunama pa zimene liyenera kuchita ndi kupeputsa umboni umene umalisonyeza kuti nlolakwa. Dziko ngati limenelo limakhala la anthu olephera, odzikonda, osatha kupeza zomwe anthu amaona kukhala zinthu zofunika, ndiko kuti kupambana, kulemekezeka ndi mabanja achimwemwe.”

Inde, mulungu wa dzikoli, Satana, akuphunzitsa anthu kudana. Koma monga munthu payekha, tingaphunzire kukonda ena. Nkhani yotsatira idzasonyeza kuti zimenezo nzotheka.

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi maseŵera apavidiyo angakhale akuphunzitsa ana anu kuda anzawo?

[Chithunzi patsamba 8]

Chiwawa cha nkhondo ndicho chizindikiro cha umbuli ndi chidani

[Mawu a Chithunzi]

Pascal Beaudenon/Sipa Press

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena