Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 9/8 tsamba 12-14
  • Kodi Ndiyenera Kuchita Maseŵero Apakompyuta Kapena Apavidiyo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndiyenera Kuchita Maseŵero Apakompyuta Kapena Apavidiyo?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Si Maseŵero Onse Amene Ali Ofanana!
  • Mbali Yake Yoipa
  • Kumwerekera!
  • Sankhani Mwanzeru
  • Kodi Ndizichita Masewera a Pakompyuta?
    Galamukani!—2008
  • Kodi Ndiyenera Kuchita Masewera a Pakompyuta?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Kusewera Magemu a Pazipangizo Zamakono?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 9/8 tsamba 12-14

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndiyenera Kuchita Maseŵero Apakompyuta Kapena Apavidiyo?

Akuzinga! Koma ukhozabe kuchitapo kanthu. Uombera mfuti zako za laser, ndi kumweta adani ako ngati tirigu. Vuto ndi lakuti, pamene ukuwaombera kwambiri, ndi pamenenso adani ambiri akuoneka. Chotero uli ndi njira imodzi yokha ngati ukufuna kupulumuka—kupha chilichonse chimene waona. Pamene ukuwaombera, adani ako akufa akumakha mwazi wochuluka . . .

“ZOSANGALATSA zong’amba msana, zong’amba mnofu, ndi zophulitsa mitu”! Umo ndi mmene wolemba magazini wina mochita chidwi anafotokozera mtundu watsopano wa maseŵero apakompyuta otchuka. Kwenikweni, ameneŵa ndi amodzi a mtundu watsopano wa maseŵero apakompyuta ndi apavidiyio amene amalola wowaseŵera kuchitadi zoyerekezera zochititsa nthumanzi. Maseŵero akale akuoneka ngati opereŵera powayerekezera ndi maseŵero ameneŵa odzala ndi mwazi, amene kaŵirikaŵiri ali achiwawa chankhanza kwambiri.

Ngakhale zili choncho, maseŵero achiwawa apavidiyo ndi apakompyuta ngotchuka kwambiri pakati pa achichepere lerolino. Ndipo chifukwa chakuti limodzi mwa mabanja atatu alionse mu United States lili ndi mtundu wina wake wa maseŵero a magetsi, achichepere mamiliyoni ambiri akhoza kuwaseŵera. Kwa achichepere amene m’nyumba mwawo mulibe zinthu zimenezi, zimangotenga mtunda waufupi kupita ku nyumba ya bwenzi kapena kumalo okhala ndi mavidiyo oseŵeretsa kukachita maseŵero ameneŵa.

Bwanji ponena za inu? Kodi munatengekapo mtima kuti mugule—kapena kungoyesa—ena a maseŵero atsopano ameneŵa? Chabwino, mutasanthula maumboni onse, mwinamwake mudzasintha maganizo anu ponena za kuchita motero.

Si Maseŵero Onse Amene Ali Ofanana!

Choyamba, tiyenera kudziŵa kuti si maseŵero onse apavidiyo kapena apakompyuta amene ali oipa kapena achiwawa. Maseŵero ambiri amapereka maphunziro; m’njira yosangalatsa amaphunzitsa maphunziro monga jogalafe, masamu, ndi kulemba ndi taipi. Maseŵero ena amatokosa mphamvu ya kuzindikira zinthu ndi kuchitapo kanthu msanga mwa kuyerekezera maseŵero monga basketball ndi hockey. Palinso ma puzzle a tekinoloji yapamwamba amene amatokosa maganizo.

Kunena zoona, ngakhale maseŵero abwino koposa angathe kudya nthaŵi yaikulu. Ndipo Baibulo limafulumiza Akristu ‘kuchita machaŵi,’ ndiko kuti, kugwiritsira ntchito bwino nthaŵi pa zinthu zauzimu. (Aefeso 5:16) Komabe, Baibulo silimafuna kuti tithere mphindi iliyonse pamene tili maso tikugwira ntchito kapena kuphunzira. Mosiyana ndi zimenezo, limatikumbutsa kuti pali “mphindi yakuseka . . . ndi mphindi yakuvina.” (Mlaliki 3:4) Kuseŵera kungakhale kotsitsimula ndiponso kwabwino ngati kumachitidwa mosapambanitsa.

Komabe, tiyenera kudziŵa kuti ambiri a maseŵero ameneŵa akuoneka kuti analinganizidwa kuti owaseŵera azitayirapo nthaŵi yaitali kwambiri. Pa ena a iwo, nthaŵi yochuluka imatayidwira pa kufuna kudziŵa maseŵerawo pamlingo wina wake, wowaseŵera asanadziŵe kuti milingo ina ingapo—yovutadi ndi yocholoŵana kwambiri—iyenera kukwaniritsidwa maseŵerawo asanathe! Palinso maseŵero ena amene amaoneka kuti samapindulitsa kwenikweni pambuyo pa kuyesayesa kwakukulu. Dan ndi Sam, Akristu aŵiri paubale wawo, ankaseŵera maseŵero ena mokangalika amene ankati adzawathandiza kudziŵa masamu. Komabe, mwamsanga anapeza kuti anali kuchita masamuwo mofulumira pa pepala kuposa pa kompyuta!

Choncho, ngakhale ndi maseŵero apakompyuta ndi apavidiyo amene ali bwino, kusankha nkofunika. Dan ndi Sam akuti: “Ngati mugula mosamaladi, mukhoza kupeza maseŵero abwino.” Komabe, nkwanzeru kupeŵa kuwonongera ndalama zambiri pa maseŵero amene amangochititsa munthu kusungulumwa mwamsanga. Kholo lina limalimbikitsa ana ake aamuna kumaseŵera kokha maseŵero amene adzawathandiza kudziŵa maphunziro amene amaphunzira kusukulu.

Mbali Yake Yoipa

Mwachisoni, maseŵero ena apakompyuta kapena apavidiyo ali zosangalatsa zovulaza—osati zophunzitsa. Zosangulutsa zapakompyuta zambiri lerolino zimasonyeza kwambiri zimene Baibulo limatcha “ntchito za thupi”—machitidwe oipa amene Mulungu amatsutsa. Pakati pa “ntchito” zotsutsidwa zimenezi pali “mchitidwe wa kukhulupirira mizimu.” (Agalatiya 5:19-21, NW) Zoonadi, kwa Yehova Mulungu kuchita matsenga ‘nkonyansa.’—Deuteronomo 18:10-12.

Komabe, maseŵero ambiri lerolino amaloŵetsamo kwambiri kukhulupirira mizimu ndi matsenga! M’maseŵero ena “kulodza” kuyenera kugwiritsiridwa ntchito kuti munthu apambane. Oseŵera amalangizidwa kuti: ‘Pamene wakonzekera kulodza, sinika pa mphezi imene ili pansi pa menu kulamanja, ndiyeno sinika pa chamoyo chimene ukufuna kupha.’ Kodi maseŵero ameneŵa sangakulitse chidwi choipa cha mphamvu zauchiŵanda?

Ndipo bwanji ponena za kumapenyerera chiwawa chauchinyama? U.S.News & World Report imanena za maseŵero aŵiri otchuka, amene amasonyeza “kuchotsa mtima wa mdani wako” ndi “mizimu yakutchire imene ikuboolaboola atsikana amaliseche” Pamene kuli kwakuti ena anganene kuti kukhetsa mwazi kwapakompyuta kuli zoyerekezera zosavulaza, Baibulo limachenjeza pa Salmo 11:5 kuti: “Yehova ayesa wolungama mtima: koma moyo Wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.”—Yerekezerani ndi Yesaya 2:4.

Kulinso kotheka kupenyerera pakompyuta zamaliseche zamtundu wapansi. Umaliseche ndi kugonana kosonyeza zonse zimaoneka kaŵirikaŵiri kwakuti opanga maseŵero a ku United States anapanga zizindikiro zochenjeza ogula za maseŵero oipa. Komabe, ndi amalonda oŵerengeka amene akuoneka kukhala ofunitsitsa kuleka kugulitsa zimenezi kwa ana. “Thayo lathu ndilo kupatsa makasitomala zimene akufuna kwatha,” akutero wogulitsa wina m’sitolo. Komabe dzifunseni kuti, ‘Kodi kupenyerera zithunzi zodzutsa chilakolako chakugonana kudzandithandiza kusumika maganizo anga pa zinthu zimene zili “zolungama, zoyera, zokongola, ndi zokoma mtima”?’—Afilipi 4:8.

Kumwerekera!

Zoona, pali kusiyana malingaliro pakati pa akatswiri ponena za mmene maseŵero apakompyuta amayambukiriradi achichepere. Kufufuza kwina, kumene kunatchulidwa m’magazini a New Scientist, kunanena motsimikizira kuti maseŵero ameneŵa “sindiwo muzu wa khalidwe loipa.” Ngakhale zili choncho, 97 peresenti ya achichepere amene anafunsidwa pa kufufuzako “anaganiza kuti kumwerekera ndi maseŵerowo nkotheka.” Achicheperewo ananena kuti maseŵero a m’nyumba zamaseŵero ndiwo oipa kwambiri chifukwa “amalimbikitsa oseŵera kutaya ndalama zambiri.”

Kodi maseŵerowa alidi omwerekeretsa? Mwachionekere inde, kwa owaseŵera ena. Wachichepere wina anauza Galamukani! kuti: “Zimene umangolingalira ndizo kutsiriza ndi kupambana.” Mnyamata wina akukumbukira mofananamo kuti: “Ndinatha maola ambiri ndikumafuna kudziŵa mmene ndingaphere aliyense ndi kupita pa mlingo wina wa maseŵerowo.”

Mungalingalire kuti simungamwerekere kwambiri ndi maseŵero. Koma taganizirani mmene maprogramu ndi mafilimu a pa TV amakhudzira mtima wa anthu—kuwachititsa kulira, kukwiya, kapena kukuwa mosangalala. Ndiyeno talingalirani za programu imene siili chabe ndi zochitika zosangalatsa, yokhala ndi anthu apadera, ndi zinthu zina zodabwitsa komanso imene imalola inuyo kukhala ngwazi. Kodi kungakhale kwapafupi kupeŵa kutengeka mtima kwambiri ndi maseŵerowo? Chotero, nkosadabwitsa kuti oseŵera ena amavutika kusiyanitsa zoyerekezera ndi zenizeni. Wachichepere wina akukumbukira kuti: “Chiyambukiro cha kuseŵera maseŵero achiwawa chinali choipa kwambiri kwakuti ndinkayerekezera kuti dzanja langa linali mfuti ndipo ndinkaliloza kwa anthu.”

Sankhani Mwanzeru

Ngati makolo saletsa kugwiritsira ntchito maseŵero apakompyuta kapena apavidiyo, achichepere ayenera kulingalira za uphungu wa pa Mlaliki 2:14 wakuti: “Wanzeru maso ake ali m’mutu wake.” Zimenezi zikutanthauza kuti wanzeru amayang’ana kumene akupita naona zimene zili kutsogolo. Kunena zoona, zosangulutsa zapakompyuta zili kale ndi zinthu zambiri zotsutsana ndi chidziŵitso cha Mulungu. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 10:5.) Ndipo ndani angadziŵe zotsatirapo zimene opanga maseŵerowa adzasonyeza? Choncho wachichepere aliyense asanagule, kuseŵera, kapena kubwereka maseŵero, ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndi maseŵero anji? Kodi dzina lake likukhudza zamatsenga? Kodi chithunzi chapachikuto chikusonyeza chiwawa choipitsitsa?’

Maseŵero abwino koposa apakompyuta ndi apavidiyo angapereke chisangalalo chabwino ndi maphunziro. Koma, kunena zoona, kodi kuli bwino kuti azikudyerani nthaŵi yanu yofunika yaikulu? Sam wazaka 14, wotchulidwa poyambapo, akusimba kuti: “Atate athu sananenepo molunjika kuti sitiyenera kukhala ndi maseŵero apavidiyo. Koma iwo afunsa kuti, ‘Kodi chosangalatsa nchiyani pa kusinika batani ndi kuona munthu akuthamanga kapena kulumpha pavidiyo?’” “Ndipo tsopano ndiwo malingaliro athu amenewo,” akuwonjezera motero mbale wake Dan.

Inde, musaiŵale kuti pali njira zina—mwinamwake zopindulitsa kwambiri—zimene mungasangalale nazo, monga kuŵerenga, kuchita zaumisiri, kutengamo mbali m’maseŵero abwino, kuimba, kapena kuphunzira kuliza chiŵiya china choimbira. Nkopindulitsa kwambiri kuthera nthaŵi “ukumadziphunzitsa ndi cholinga cha kupeza kudzipereka kwaumulungu.” (1 Timoteo 4:7, NW) Kuchita motero kudzakhala kopindulitsa kwambiri kuposa kuseŵera maseŵero alionse apakompyuta ndi apavidiyo.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Achichepere okwanira 97 peresenti amene anafunsidwa pa kufufuza kwina “anaganiza kuti kumwerekera ndi maseŵerowo nkotheka”

[Chithunzi patsamba 14]

Kodi kuseŵera maseŵero achiwawa apavidiyo kungakuvulazenidi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena