Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 1/8 tsamba 32
  • “M’Kamwa mwa Makanda”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “M’Kamwa mwa Makanda”
  • Galamukani!—1996
Galamukani!—1996
g96 1/8 tsamba 32

“M’Kamwa mwa Makanda”

Mkazi wina wa ku Ballito, Natal, South Africa, anayamikira kwambiri buku lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndi kulemba kuti:

“Ndili ndi mphwanga, Rudi Naidoo, amene ali kokha ndi chaka chimodzi ndi theka, ndipo amatchula pafupifupi dzina la munthu aliyense wa m’bukumo mwa kungoyang’ana zithunzi zawo. Amakuuzaninso ngakhale zimene ena a anthu a m’Baibulowo akuchita pazithunzipo. Mwachitsanzo, nkhani 11 imasonyeza Nowa akupereka nsembe. Rudi amatiuza kuti, ‘Nowa—pemphera Yehova.’

“Atafunsidwa zimene Yoswa akuchita m’nkhani 49, Rudi amaima ngati Yoswa pachithunzipo akumanena kuti ‘Dzuŵa ima!’ Sangathe kutchula mawuwo bwinobwino koma amazinena m’njira yake yokondweretsa ndi yabwino.

“Kachiŵirinso, ndikufuna kukuyamikani kaamba ka chofalitsidwa chabwino kwambiri chimenechi. Ana aang’ono amatha kufotokoza zimene akulu ena samadziŵa. Mawu a Yesu pa Mateyu 21:16 ngoonadi: ‘M’kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza.’”

Ngati mungakonde kulandira buku la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kapena ngati mungafune wina kubwera panyumba panu kudzakambitsirana nanu za kufunika kwa kuphunzira Baibulo, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yapafupi nanu yondandalikidwa patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena