Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 3/8 tsamba 32
  • “Kukula Popanda Iwo Kwakhala Kovuta Kwambiri”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kukula Popanda Iwo Kwakhala Kovuta Kwambiri”
  • Galamukani!—1995
Galamukani!—1995
g95 3/8 tsamba 32

“Kukula Popanda Iwo Kwakhala Kovuta Kwambiri”

“NDIKULEMBA kalata nditaŵerenga chotulutsidwa chathu chatsopano cha msonkhano, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, kuti ndisonyeze kuthokoza kwanga kwakukulu kochokera mumtima kaamba ka brosha lolembedwa mokhudza mtima ndi lolimbitsa chikhulupiriro limeneli.

“Ndili ndi zaka 18. Atate wanga anafa pangozi ya galimoto pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi zitatu, ndipo ngakhale kuti zimenezi zinachitika zaka khumi zapitazo, ndidakali wosungulumwabe kwambiri. Kukula popanda iwo kwakhala kovuta kwambiri. Pali zinthu zambiri zimene ndinafuna kuwauza, kukambitsirana nawo, kudziŵa za iwo. Nkotonthoza kwambiri chotani nanga kukumbutsidwa za chiyembekezo cha chiukiriro chachikondi cha Yehova! Chimadzetsa misozi m’maso mwanga. Zikomo kachiŵirinso chifukwa cha kundipatsanso chiyembekezo.”—Mboni yachichepere ya ku Austria.

Makalata ambiri onga imeneyi alandiridwa ku maofesi a Watchtower Society a ku New York. Lofalitsidwa m’zinenero 18 tsopano, brosha la masamba 32 limeneli limatonthoza anthu mamiliyoni ambiri. Ngati mukulira chifukwa cha kutayikiridwa mu imfa ndi wokondedwa wanu wina, khalani womasuka kupempha kope la chofalitsidwa chimenechi mwa kulembera ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera yondandalikidwa patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena