Chimwemwe—Chatsimikiziridwa!
“ODALA ali osauka mumzimu,” anatero Yesu Kristu. (Mateyu 5:3) Mosiyana ndi nzeru wamba, Yesu anasonyeza za kukhutiritsa chosoŵa cha munthu chauzimu m’malo mwa kukhutiritsa zikhumbo za zinthu zakuthupi monga chinthu chofunika chopezera chimwemwe. Mawu a Yesu amenewo, ngati atsatiridwa, amadzetsa chitsimikizo cha chimwemwe.
Komabe, kukhala wozindikira chosoŵa cha munthuwe chauzimu, kumafuna zambiri kuposa kungozindikira kuti chilipo. Kaŵirikaŵiri, chosoŵa chosakhutiritsidwa chimakhala chinthu choyambitsa nkhawa ndi mkwiyo m’malo mwa chimwemwe. Mwambi wa Baibulo umanena zimenezi motere: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” (Miyambo 13:12) Motero, chimwemwe chimakula pamene munthu atenga masitepe a kudziŵa ndiyeno kukhutiritsa chosoŵa chake chauzimu. Kodi zimenezi zingachitidwe motani?
Apa mpamene Baibulo limafunika. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ndi ilo lokha limene lingapereke mayankho a mafunso amene anthu ambiri asinkhasinkha kwanthaŵi yaitali popanda kupeza mayankho okhutiritsa. Mwachitsanzo, kodi munayamba mwadabwapo kuti, ‘Kodi chifuno cha moyo nchotani? Kodi nchifukwa ninji munthu ali padziko lapansi? Kodi mtsogolo muli chiyani?’ Kuwonjezera pa kupereka mayankho okhutiritsa a mafunso ameneŵa ndi ena, Baibulo limaperekanso chitsogozo chokhalira moyo chimene chathandiza mamiliyoni ambiri kulimbana ndi mavuto ocholoŵana amene tonsefe timayang’anizana nawo lerolino ndi amene kaŵirikaŵiri amadodometsa kufunafuna kwathu chimwemwe. “Mawu [a Mulungu] ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Inde, Baibulo ndilo chitsogozo chotsimikizirika chimene chingakuthandizeni kupambana pa kulondola chimwemwe. Talingalirani zitsanzo ziŵiri zenizeni izi.
Kuleka Kunyansidwa ndi Kupeza Chimwemwe mu Ukwati
Ukwati ungabweretse chimwemwe kapena mavuto. Mwachisoni, kwa ambiri ndi mavuto. Komabe, uphungu wa Baibulo, pamene wagwiritsiridwa ntchito, wathandiza ambiri kupeza chimwemwe mu ukwati umene kale unali wopanda chimwemwe.
Yungk’un ndi Meihsiu anali mu mkhalidwe wotero. “Zaka zisanu ndi ziŵiri zoyambirira za ukwati wathu zinali zopanda chimwemwe,” akuulula motero Yungk’un. “Ndinathera nthaŵi yochepa kwambiri ndi mkazi wanga ndi ana aakazi aŵiri. Kunena zoona, kaŵirikaŵiri ndinkagona kuntchito.” Ngakhale kuti anali ndi zinthu zonse zakuthupi zimene anafunikira, iwo analibe chimwemwe. Mkazi wake akuwonjezera kuti: “Ngakhale kuti mwamuna wanga anatisamalira ndi zinthu zakuthupi, anangondisiyira mathayo onse a m’banja. Zinandinyansa kwambiri.” Iwo analingalira ngakhale za kulekana.
Yungk’un anali ndi mavuto ena ndi achibale akenso. Chifukwa cha zovuta zakumbuyo za m’banja, iye sanalankhulane ndi mlongo wake wamkulu kwa zaka zisanu ndi ziŵiri. Zimenezi zinali choncho ngakhale kuti anali kukhalirana pautali wa mamita osaposa zana limodzi chabe. Komabe, tsopano iye amasangalala ndi ukwati wachimwemwe ndi unansi wabwino kwambiri ndi mlongo wakeyo. Kodi nchifukwa ninji pali kusintha kwakukuluko?
“Mkazi wanga ndi ine tinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndi kufika pamisonkhano yawo ya Baibulo yamlungu ndi mlungu,” akulongosola motero Yungk’un. Mlongo wake anachita chimodzimodzi. Iwo anayamba kugwiritsira ntchito zinthu zimene anali kuphunzira ndipo anadabwa ndi zotulukapo zake. Yungk’un anapeza ntchito imene inamlola kusamalira osati zosoŵa zakuthupi za banja lake zokha komanso zosoŵa zawo zauzimu ndi zamalingaliro. Tsopano iwo ali ndi moyo wa banja wachimwemwe ndi wogwirizana.
Anapeza Chifuno cha Moyo
Awo amene amapenda chibadwa cha munthu anena kuti, kuti tikhale achimwemwe tifunikira chifukwa chokhalira moyo, chifuno cha moyo. Moyo wozikidwa pa kulondola zinthu zakuthupi kwadyera sumakhutiritsa chosoŵa chimenechi. Lini wa zaka 26 anapeza zimenezi kukhala zoona.
“Ndinali kugwira ntchito maola 12 patsiku, masiku asanu ndi aŵiri pamlungu,” akutero mkaziyo. “Chonulirapo changa chinali chakuti nditsegule saluni yaikulu yokonzeramo tsitsi.” Ngakhale kuti iyeyo anali pafupi kukwaniritsa chikhumbo chakecho, anaona kuti kanthu kena kanali kusoŵeka m’moyo wake. “Ndinali kudabwa ponena za chifuno cha moyo. Kodi chinali cha kungogwira ntchito ndi kupeza ndalama?”
Ndiyeno tsiku lina munthu wina anafika mu saluni yake ndi kumfunsa funso limodzimodzilo limene anadzifunsa. Anauzidwa kuti Baibulo lingayankhe funso limenelo. Ngakhale kuti anali asanaŵerengepo Baibulo, anavomereza kupatula ola limodzi mlungu uliwonse kuti alisanthule.
M’phunziro lake lamlungu ndi mlungulo, Lini anaphunzira kuti Baibulo linaneneratu zinthu zambiri zimene anali kuona tsiku lililonse. Anadabwa ndi mmene Baibulo linafotokozeratu molondola za mikhalidwe imene anali kuona, likumaneneratu kuti “anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” Anaphunziranso maulosi ena amene amasonyeza za mavuto omwe sanachitikepo ochititsidwa ndi nkhondo, njala, ndi masoka achilengedwe amene akuoneka padziko lonse.—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:7, 12.
Ndiyeno Lini anaphunzira za kanthu kena kamene kanampatsa chimwemwe kwambiri—kuti mikhalidwe ya dziko imeneyi imene kaŵirikaŵiri imalanda anthu chimwemwe ili chizindikiro chakuti nyengo ina yatsopano m’mbiri ya munthu ili pafupi kudza. (Mateyu 24:3-14) Iye anaŵerenganso m’Baibulo kuti Mlengi wa mtundu wa anthu akufuna kukhazikitsa dziko latsopano pompano pa dziko lapansi, mmene mudzakhala kulemera kumene munthu wopanda ungwiro sanakuonepo padziko lonse. (Salmo 72:16; Yesaya 65:17, 18, 21, 22) Chitaganya cholemera cha mtsogolo chimenechi sichidzaipitsidwa ndi umbombo, dyera, ndi kukondetsa chuma, ndi zotulukapo zake zonse zoipa. (Salmo 37:9-11, 29; 1 Akorinto 6:9, 10) Iye anakondwera pamene anaŵerenga mawu awa m’Baibulo: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:13.
Chimwemwe Chikukuyembekezerani
M’malo mwa kuthera nthaŵi yake yonse pa kulondola zonulirapo zakuthupi, Lini tsopano amathera nthaŵi yake yochuluka pa kuuza ena za zinthu zimene waphunzira. Kodi mungakonde kudziŵa zambiri ponena za malonjezo abwino ameneŵa? Kodi mungakonde kudziŵa mmene Baibulo lingakuthandizireni kupeza chimwemwe chimene Lini, Yungk’un, Meihsiu, ndi mamiliyoni ena apeza? Mboni za Yehova zidzakhala zofunitsitsa kukuthandizani.
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Mlengi wathu akufuna kukhazikitsa paradaiso wa padziko lapansi