Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndiyenera Kupita ku Prom?
“Kaŵirikaŵiri usiku wopita ku prom umakhalanso nthaŵi yoyamba pamene makolo anu amakuuzani kuti, ‘Wokondedwa, ukakhale ndi nthaŵi yabwino. Tidzawonana m’maŵa.’”
“Ndikumbukira kuti ndinapita kukavina kusukulu kumene kunali operekeza aŵiri chabe, ndipo iwo sanali kupereka chisamaliro chirichonse kwa achichepere.”
ANZANU a m’kalasi akhala akulankhula za iyo kwa miyezi yambiri. Ndiiko komwe, proma ya omaliza maphunziroa sukulu yasekondale imachitika kamodzi m’moyo wa munthu. Ndipo popeza kuti mudzakhala mukusazika anzanu a m’kalasi amene mwawadziŵa kwa zaka zambiri, inu mwachibadwa mungafune kukapezekako. “Chiyambire kuloŵa mbali yoyamba ya sukulu yasekondale,” akutero msungwana wina wazaka 18 zakubadwa, “ndakhala wofunitsitsa kupita ku prom.”
M’maiko ena prom ya omaliza maphunziro a sukulu yasekondale—kuvina kwamwambo kochitidwa maphunziro a sukulu yapamwamba (sekondale) asanamalizidwe—kuli kofunika kwambiri kwa achichepere. Koposa ndi kukhala phwando wamba la anthu onse, prom iri dzoma lolemekezeka loloŵera muuchikulire. Magazini a Seventeen akuti: “Kaŵirikaŵiri usiku wopita ku prom umakhalanso nthaŵi yoyamba pamene makolo anu amakuuzani kuti, ‘Wokondedwa, ukakhale ndi nthaŵi yabwino. Tidzawonana m’maŵa.’ Kukaseŵera usiku wonse sikuli chabe kololedwa—kulinso kanthu kamene munthu ayenera kuchita.”
Sizikutanthauza kuti achichepere onse amakonzekera usiku wonse wa khalidwe lokaikitsa. Mmalo mwake, ambiri amangoyembekezera kukhala ndi nthaŵi yabwino kwambiri—mwaŵi wa kulemekezedwa kapena kukopa! “Ziri ngati maloto,” akutero Darcey wa zaka 19 zakubadwa. “Iwo amatsika m’galimoto zokongola zochita kulipirira, amajambulitsa zithunzithunzi, nadziwonetsera pamaso pa mabwenzi awo. Imakhala nthaŵi yawo yokopa chidwi cha ena.”
Kochititsa chidwi pang’ono, komanso kotchuka, ndiko kuvina kwa pasukulu. “Nthaŵi ndi nthaŵi, mumafunikira mayanjano ocheza kokha kuti mukhale ndi nthaŵi yabwino,” akutero Jamey wazaka 15 zakubadwa. Koma mosasamala kanthu kuti kaya chimene chimawakopa ndicho kuvina, kukadya chakudya chamadzulo, kapena kuvala zovala zabwino, achichepere ambiri amawona kuti kupita ku zochitika zamtundu umenewu kuli thayo lalikulu. Iwo amangoda nkhaŵa za amene adzapita naye, zimene adzavala, ndi mmene adzapezera ndalama zolipirira chochitika cha madzulowo. Koma pali zinthu zina zimene mungafunikire kupenda.
Kuyang’ana Patali Koposa Chikondwererocho
Yesu Kristu iyemwini anali munthu amene anapita ku mapwando olemekezeka. (Yerekezerani ndi Luka 5:29; Yohane 2:1, 2.) Koma ‘michezo,’ kapena “mapwando osalamulirika,” amatsutsidwa m’Baibulo. (Agalatiya 5:21; Byington) M’zaka za zana loyamba, mapwando osalamulirika kumene akunja anachita poyera “zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka,” anali ofala. Chotero Akristu anachenjezedwa kupeŵa kupita kuzochitika zosalamulirika zimenezi.—1 Peter 4:3, 4.
Bwanji za maprom ndi kuvina kwa pa sukulu? Ena amalinganizidwa ndi kuyang’aniridwa bwino lomwe, chotero amakhala zochitika zolamulirika bwinopo. Khalidwe loipa lingatsutsidwe ndi kuthetsedwa mwamsanga ngati libuka. Koma kumbuyo kwa chikondwerero ndi nsangala ya maprom ambiri—ngati sionse—kaŵirikaŵiri kumakhala mzimu wa mchezo.b “Pamakhala chisembwere ndi kumwa kwambiri,” wachichepere wina anauza mtola nkhani wa Galamukani! Zakumwa zoledzeretsa zingaletsedwe mwalamulo. Koma kumwa kwambiri kungachitikire m’zimbudzi, m’makwerero, ndi m’malo oika galimoto.
Baibulo limachenjeza: ‘Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa.’ (Miyambo 20:1) Tsopano wonjezanipo nyimbo zina zaphokoso kapena zodzutsa nyere, kuvina kosalamulirika, magetsi oŵala pang’ono, ndi gulu la achichepere omwe angakhale osalemekeza kwambiri malamulo a Baibulo, ndipo mudzakhala ndi zosonkhezera mchezo. Kodi mungadalire operekeza kulamulira zinthu? Osati nthaŵi zonse. Wachichepere wotchedwa Charles molunjika akuti: “Operekezawo samachita kalikonse.” Ndibodza? Osati malinga ndi kunena kwa Darcey wachichepere, amene akuti: “Ndikukumbukira kuti ndinapita kukavina kusukulu kumene kunali operekeza aŵiri chabe, ndipo iwo sanali kupereka chisamaliro chirichonse kwa achichepere.”
Tiyenera kuvomereza kuti ngakhale woperekeza wosamalitsa angakuwone kukhala pafupifupi kosatheka m’chipinda chovinira kapena m’holo yochita kamdima kulamulira gulu la achichepere amene ali otsimikiza kukhala ndi ‘nthaŵi yabwino.’ Chotero, chiyembekezo cha kukhala ndi madzulo osangalatsa chingasinthe mwamsanga kukhala chosakondweretsa. “Kumachitika ndewu zochuluka,” akutero msungwana wina.
Mikhalidwe Yochititsa Kugonja
Zowona, simaprom onse kapena kuvina konse kwa pa kusukulu kumene kumabukapo chiwawa. Chikhalirechobe, pali ngozi yaikulu yakuti mungaloŵetsedwe mumkhalidwe wowopsa wa kugonja. Msungwana wina akukumbukira kuti: “Mukamavina nkhope yanu itayandikana kwambiri ndi ya anyamata, manja awo amapapasa mbali zosiyanasiyana za thupi lanu. Amayembekezera kuti muvomereze zimenezo!” Kodi simungapeŵe vuto longa limeneli mwa kungodzipatula kwa ena? Mwinamwake. Koma kaŵirikaŵiri zimenezo nzosavuta kunena koposa kuchita.
Tinene kuti mwapita popanda woperekeza kapena mwapita ndi kagulu ka mabwenzi. Msungwana wina akutikumbutsa kuti: “Anyamata ena amakhala opanda mnzawo, ndipo amayesa kulondola asungwana ambiri monga momwe angathere.” Ndiponso kumeneko kungakhale asungwana angapo aukali. Wachichepere yemwe amapita yekha mosavuta angakope oterowo mosayembekezera.
Kumbali ina, kukhala ndi wokhulupirira mnzanu monga wopita naye kungachititsenso mavuto ena. Ndiiko komwe, kupalana ubwenzi kumatengedwa mwamphamvu ndi Mboni za Yehova lerolino.c Ndipo ngakhale ngati muli wotsimikizira kuti mtima wa yemwe mudzapita naye suuli wokopeka ndi inu, kodi iye angakhaledi wokutetezerani kufikira pati? Lora wazaka 19 zakubadwa akuti: “Kodi nchiyani chimene chidzaletsa ena kusinthana wovina naye—kapena kukupemphani kupita nawo kokacheza? Pamenepo nchiyani chingachitike?” Mkhalidwe woipa, wosakondweretsa ungabuke mosavuta.
Ndiponso, chosafunikira kunyalanyazidwa ndicho upandu wa kululuza miyezo yanu yachikhalidwe ndi kudziloŵetsa mumzimu wa chochitikacho. Ndithudi mayanjano oipa “aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Nick wazaka 18 zakubadwa akuvomereza kuti: “Ngakhale ngati aŵiri a Mboni za Yehova angapitire limodzi, iwo mosavuta angasonkhezeredwe kuchita zimene wina aliyense akuchita.”
Pamene Phwandolo Litha
Komabe, nthaŵi zambiri mavuto aakulu amabuka pambuyo pa phwandolo. “Ena amapita ku hotela kapena ku nyumba ya wina,” akutero Tanya wachichepere. Yolanda akuwonjezera kuti: “Ufunikira kukhala komweko usiku wonse. Umenewo ndimwambo.” Anamgoneka, zakumwa zoledzeretsa, ndi kugonana zingakhalenso mbali ya mwambo wa prom. Komabe, m’maŵa motsatira wachichepereyo angatsale ndi chikumbumtima chovulala, kudzilemekeza kocheperapo, ndi mantha aakulu a kutenga mimba—kapena AIDS.
Pamenepa, mwakaŵirikaŵiri kwambiri, maprom ndi kuvina kwa pa sukulu zimalephera kukwaniritsa chiyembekezo cha chisangalalo ndi nthaŵi yabwino ndipo zimakhala mapwando aphokoso, michezo. Tikukumbutsidwa kuti mneneri Yesaya m’tsiku lake anasonyeza kutsutsa kwa Mulungu mapwando ‘amene achezera usiku.’ Mapwandowo anali okwanira ndi vinyo ndi nyimbo—‘zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro.’ Inali nthaŵi yabwino kodi? Ndithudi. Koma Yesaya anati za opita ku mapwandowo: ‘Iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang’ana pa machitidwe a manja ake.’—Yesaya 5:11, 12.
Inde, kuchita mapwando ndi achichepere amene samazindikira lingaliro la Baibulo kungadzetse upandu wowopsa. Zowona, sizochitika zonse zotero zimene zimakhala michezo, ndipo mikhalidwe imasiyanasiyana pa dziko lonse. Choncho inu ndi makolo anu muyenera kusankha kaya ngati kuli koyenera kwa inu kupita. “Nkovuta,” anavomereza motero msungwana wina, “chifukwa prom imasangalatsa, ndipo imakuikadi pachiyeso. Imakhala nkhani yaikulu chaka chonse!”
Koma kukambitsirana ndi makolo anu kapena Mkristu wachikulire kungathandizire kumveketsa zinthu. Lingalirani izi: Kodi ndani amene adzapita kukuvina? Kodi ndiuyang’aniro wotani umene udzakhalako? Kodi zakumwa zoledzeretsa zidzaperekedwa? Kodi ndinyimbo zamtundu wotani zimene zidzalizidwa? Kodi panabukapo mavuto zaka zapitazo? Kodi kutenga mbali m’chochitika chotero kungawonedwe motani ndi ena—makamaka Akristu anzanu? Kodi kukapezekako kungakhale kokhumudwitsa ena?—1 Akorinto 10:23, 24, 32.
Polingalira za mavuto ogwirizanitsidwa ndi maprom ndi kuvina kwa pa sukulu, achichepere Achikristu amakambitsirana ndi makolo awo ndipo mwinamwake angasankhe kusapitako. Koma kodi kumaliza maphunziro anu sikuli chipambano chokondwera nacho? Ntheradi! Komabe, mwinamwake mungapeza njira yabwino yokondwerera, kapena mwa kugaŵana chimwemwe chanu ndi Mboni zinzanu. Mwachitsanzo, banja lanu lingasankhe kukonza kamsonkhano koyenera kapena phwando. Pamene masonkhano otero saali aakulu kwambiri ndipo ali olinganizidwa bwino, kaŵirikaŵiri sipamabuka mavuto owopsa.d
Phwando lotero lingasoŵe chikondwerero ndi nthumanzi zopezeka ku prom yamwambo ya pa sukulu. Koma lingakhalebe nthaŵi yachisangalalo—yopanda mbuna zimene prom kapena kuvina kwa pa sukulu kungadzetse. Chabwino kopambana, mudzagwirizana ndi mawu a Paulo pa 1 Akorinto 10:31: ‘Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse kuulemerero wa Mulungu.’
[Mawu a M’munsi]
a “Kuvina kwamwambo kochitidwira kalasi ya pasukulu ya sekondale kapena pakoleji kaŵirikaŵiri pamapeto kapena pafupi ndi mapeto a chaka cha maphunziro. [Chidule cha PROMENADE.]”—The American Heritage Dictionary of the English Language.
b “Mchezo” umafotokozedwa kukhala kuchita phwando kapena kusekera kwaphokoso.
c Wonani mutu 30 wa bukhu la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
d Wonani nkhani yakuti “Zosangulutsa Pocheza—Sangalalani ndi Mapinduwo, Peŵani Misampha” m’kope la Nsanja ya Olonda ya August 15, 1992.
[Chithunzi patsamba 18]
Operekeza amakuwona kukhala pafupifupi kosatheka kulamulira mkhalidwe wa opezekapo