‘Iye Amadziŵa Mayankho Onse a Baibulo’
Nthaŵi ina yapitayo mkazi wokhala mu New York State anatumizira yemwe kale anali mnzake wa m’kalasi, amene ankalera banja, kope la bukhu la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Patapita nthaŵi ina mkaziyo analandira kalata kuchokera kwa mnzakeyo mu imene analemba za mwana wake wamkazi Elizabeth:
“Iye amalikonda bukhulo—ndilo lokha limene amafuna kuŵerengeredwa popita kogona. Iye amalandira nkhani zisanu (chifukwa chakuti ali ndi zaka zisanu) usiku umodzi, ndipo mlungu watha mphunzitsi wake wa Sande sukulu anandiuza kuti angadalire pa Elizabeth kudziŵa mayankho onse ku mafunso Abaibulo. Chotero liyenera kukhala linalembedwa ndi winawake amene amamvetsetsadi chimene ana amakonda.”
Mkazi wa ku New York ameneyo akulongosola motere ponena za bwenzi lakelo: “Chimenechi chiyenera kukhala chivomerezo chake chowona mtima, popeza kuti iye ngomasuka ndipo sakanatamanda bukhulo ngati sakadalikonda.”
Tikulingalira kuti nanunso mudzawona bukhu lokhala ndi zithunzi zokongolali, lazilembo zazikulu kukhala lamtengo koposa. Nkhani zake 116 za Baibulo zimapatsa woŵerenga lingaliro la chimene Baibulo likunena. Nkhanizi zimawoneka m’ndandanda ya mmene zochitikazo zinachitikira m’mbiri. Mudzapeza zimenezi kukhala zothandizadi pophunzira pamene zinthu zinachitika m’mbiri, mogwirizana ndi zochitika zina. Landirani bukhu lofunika koposa limeneli lamasamba 256 mwakudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 4.)