Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 1/8 tsamba 23
  • ‘Mtundu Woipitsitsa wa Kuipsya Mwana’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Mtundu Woipitsitsa wa Kuipsya Mwana’
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusakaza kwa Moyo Wonse
  • Osuta Paketi Imodzi pa Tsiku
  • Kodi Kusuta Kulidi Koipa Motero?
    Galamukani!—1991
  • N’kusiyiranji Kusuta?
    Galamukani!—2000
  • Kodi Iwo Akuyambukitsa Imfa?
    Galamukani!—1988
  • Fodya ndi Umoyo Wanu—Kodi Palidi Kugwirizana?
    Galamukani!—1989
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 1/8 tsamba 23

‘Mtundu Woipitsitsa wa Kuipsya Mwana’

Manja a mayiyo amangana mozungulira khosi la khandalo. Kenaka ayamba kusindikiza—akumanyonga mwanayo mwapang’onopang’ono. Mwana wopanda thandizoyo apuluputa. Kokha panthaŵi yake mkaziyo achepetsa kugwira kwakeko. Khandalo lipuma mpweya mwabefu koma lapulumuka kuwukirako. Pasanapite nthaŵi yaitali, mkaziyo agwiranso khosi laling’onolo, ndi kuyambanso kuzunzako. Kachiŵirinso aleka ndi kulola kamwanako kakupuma mpweya mwabefu . . .

ZIMENE mwangoŵerengazo zikulongosa kuvutika konga kumene mwana wosabadwa amakumana nako pamene akuipsyidwa moipa ndi mayi wosuta.

Kusakaza kwa Moyo Wonse

Ndemanga yongoyerekeza? Kutalitali. nkhani ya mu New York Times ikusimba kuti ziŵerengero zomakulakula za maphunziro asayansi zikusonyeza kuti mayi amene amasuta mokhazikika angaike zivulazo za moyo wonse zakuthupi ndi maganizo pa mwana wake. Nkhaniyo ikutero kuti, zina za zivulazo zimenezi, “zimawonekera pa nthaŵi yomweyo pamene kuli kwakuti zina zimachitika pang’onopang’ono.”

Kodi ndimwanjira yotani kusuta kwa mayi kumayambukirira mwana wosabadwa? Dr. William G. Cahan, dokotala wothandizira kutumbula pa Memorial Sloan-Kettering Cancer Center mu United States ndiponso mkozi wa nkhani ya mu Times, akulongosola kuti: “Mkati mwa mphindi zingapo kusuta kulikonse kwa ndudu kumalowetsa carbon monoxide (mpweya woipa) ndi chikonga m’mwazi wa mayiyo.” Pamene carbon monoxide ikuchepetsa mphamvu ya mwazi wonyamula oxygen (mpweya wabwino) ndipo chikonga chikuchepetsa ukulu wa mitsempha ya mwazi mu chibaliro, “mwana wosabadwayo kwa kanthaŵi amamanidwa unyinji wachibadwa wa oxygen. Ngati kumanaidwa kumeneku kubwerezedwa kaŵirikaŵiri,” akutero sing’anga wotumbula Cahan, “kungawononge kotheratu ubongo wa mluza, chiŵalo chimene chimavulazika mofulumira ndi kusoŵa kwa oxygen.”

Mwachitsanzo, kufufuza kwina kunavumbula kuti mphindi zisanu pambuyo pakuti mayi wapakati wasuta ndudu ziŵiri zokha, miluza yawo inasonyeza zisonyezero za kusoŵa chochita—kukwera kwa kugunda kwa mtima kotsatiridwa ndi kuyenda kofanana ndi kupuma kwa mpweya.

Osuta Paketi Imodzi pa Tsiku

Pamenepa, kodi nchiyani chimene chimachitika kwa mwana wosabadwa ngati mayi wake amasuta ndudu 20, kapena paketi imodzi pa tsiku? Dr. Cahan akuyerekezera kuti wosuta wamba amakoka utsi kasanu pa ndudu imodzi. Chotero, chizoloŵezi cha paketi imodzi patsiku chimafikira ku kukoka utsi kwa zana limodzi pa tsiku. Popeza kuti mimba imatenga masiku 270, mayiyo amaika mwanayo “ku kuukiridwa kwakuthupi ndi mankhwala chifupifupi 27,000.”

Ana oipsyidwa moterowo angalipire mtengo wa moyo wawo wonse chifukwa cha chizoloŵezi cha fodya cha mayi wawo. Pambali pa mavuto akuthupi, akutero Dr. Cahan, anawo angakhale ndi “mavuto a makhalidwe, kusoŵeka kwa maluso akuŵerenga, kuchita zinthu mopambanitsa ndi kupinimbira kwa maganizo.” Mosadabwitsa, iye akufunsa kuti: “Kodi ndi mkazi wathayo wotani amene angapitirize ndi chizoloŵezi chowopsyeza motero kwa wachichepere wake?”

Kuwonjezerapo, makolo osuta alinso chiwopsyezo kwa ana omakula. Chifukwa ninji? Kabukhu kakuti Facts and Figures on Smoking, kofalitsidwa ndi American Cancer Society, kakuyankha kuti: “Ana a osuta amakhala ndi matenda ochurukira a dongosolo lopumira kuposa aja a osasuta, kuphatikizapo kuwonjezeka kwa nthawi ndi nthawi kwa chifuwa cholepheretsa kupuma ndi chibayo kuchiyambiyambi m’moyo.”

Chotero Dr. Cahan akumaliza kuti “mtundu umenewu wa kuipsya mwana ungakhale woipitsitsa kuposa yonse.” Funso nlakuti, Kodi mumakupeŵa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena