Kumaliyang’ana Dziko
Kuŵerenga Baibulo Kutsika mu Sweden
Kuŵerenga Baibulo kwacheperako mokulira mu Sweden, kulingana ndi ripoti lokhala ndi mutu wakuti Anthu a ku Sweden ndi Baibulo. Mkonzi, Thorleif Pettersson, profesala wothandizira wa Swedish Bible Society, wadziŵitsa kuti kokha maperesenti 36 a chiŵerengero cha m’dzikomo amadzinenera kukhala aŵerengi a Baibulo, 3 peresenti ya iwo amati amaliŵerenga ilo tsiku ndi tsiku. 64 peresenti yotsala silimaliŵerenga nkomwe. Mosiyanako, mu 1949, panali 66 peresenti omwe anaŵerenga Baibulo ndi 34 peresenti omwe sanatero. Mu ripoti lake, Pettersson wadziŵitsa kuti 11 peresenti ya chiŵerengero cha dziko alibiretu Baibulo ndipo imasonyeza icho kukhala chowona kwa 25 peresenti ya aja omwe ali pansi pa zaka 30 za kubadwa. Atafunsidwa ngati anthu achichepere “angadzaŵerenge Baibulo atakula,” iye anayankha kuti, “Ayi, iwo sadzaliŵerenga nkomwe Baibulo. Kuŵerenga Baibulo kudzachepa mwapang’onopang’ono ngati kachitidwe kamakonoka kapitirizabe ndipo ngati mphepo zauzimu sizidzayamba kukuntha.”
Kubwezera Choipa pa Choipa
Wodziŵa za mbiri yakale wa ku Egypt, Ahmed Behgat, wafalitsa bukhu lomwe lapereka mlandu wakuti “mnthaŵi ya Kutuluka Aisrayeli akale anaba golide kutuluka naye kupita ku Igupto ndipo anamugwiritsira ntchito kupanga mwana wa ng’ombe wa golide.” Kufufuza kwa Mr. Behgat kolowa m’malo osungira zinthu zakale a ku Igupto kwamtsogolera iye kumaliza kuti Israel afunikira kulipira Igupto $40 biliyoni (U.S.) koma popanda chiwongola dzanja, kulingana ndi lamulo la Chisilamu. Komabe, pamene kupeza kwake kunafalitsidwa, kulingana ndi nsonga zopezeka mu World Press Review, “Liwu la Wailesi ya ku Israel inafuna zobwezeretsedwa kaamba ka ntchito ya ukapolo imene Farao anaika pa Israyeli.”
Chikumbumtima cha Sirapu
Maple sirapu ya ku Canada yodziŵika kwambiri padziko iri pangozi yokulira ya kudzangokhala kokha zokumbukiridwa ngati kuyambukira kwa kuipitsidwa kwampweya sikunachotsedwepo mwamsanga mwanjira ina yake, yatero nkhani ina mu nyuzipepala ya m’dzikolo The Globle and Mail. “Chiyambire 1978, Quebec yotulutsa maple-sirapu yakhala ikuchitira ripoti kuti mitengo ya misinkhu iriyonse inali kufa popanda chifukwa chenicheni. Kulongosola kokha kumene asayansi akhala akubwera nako kuli kuipitsidwa kwampweya, kuphatikizapo mvula yaululu ndi mankhwala olingana nazo,” iyo inatero. Kufufuza mu mbali zovulazidwazo kumasonyeza kukula kodabwitsa chiyambire 1983: kuchokera pa maperesenti 29 amitengo yoyambukiridwa moipa kufika ku maperesenti 80. Mkuyesayesa kwa kufuna kupulumutsa mitengoyo ndi indasitiri ya maple-sirapu, ofufuza akuitanira kaamba ka kulekeka kwa kuipitsa mpweya kochitidwa ndi kugwiritsira ntchito kwa mankhwala onga ngati sulfur ndi nitrogen oxides.
Kukambitsirana kwa UN
Majagi omwera madzi unali mutu wa kukambitsirana kwaukali kwa maora atatu pa Mitundu Yogwirizana, ndipo mofanana ndi nkhani zina zomwe anakambitsirana, panali kugwirizana kochepa. Nkhaniyo inauka pamene majagi omwera madzi ndi magalasi operekedwa kwa nthumwi imodzi ndi imodzi mu zipinda za mabungwe 13 zinachotsedwapo monga njira yochepetsako zotaika za $100,000 pachaka. Chomwe chinafunsidwa chinali chifukwa chimene tcheyamani wa bungwe ndi aja okhala pafupi naye anapitirizabe kukhala ndi zotengera madzi. (Chinali chifukwa chakuti sangakhoze kutuluka ndi kupita ku akasupe amadzi.) Funso lina linali ponena za mmene UN inakhozera kugwira ntchito ndi zowonongedwa zazikulu zoterozo kokha kungofuna kuperekera madzi ku nthumwizo. (Chinali chifukwa chakuti anthu asanu ankafunika kuperekera madzi kaŵiri patsiku ndi kuphitsa magalasiwo kuti aphe tizirombo pambuyo pa kugwiritsira ntchito kumodzi ndi kumodzi.) Pamene kukambitsirana kunakulitsidwa, tcheyamani analingalira kuti nthaŵi yowonjezereka yolipiridwa kwa olonda ndi otembenuza usiku umenewo ikalingana ndi unyinji womwe ukasungidwa mwa kuleka ntchito ya madzi.
Opereka Ziwalo Amoyo?
Chiŵerengero chokulira cha adokotala akukaikira ngati ophatikizidwa mu ngozi “omwe achotsedwa ziwalo ndi asing’anga osamutsa ziwalo pambuyo pa kulengezedwa kukhala atafa koma amene mitima yawo ikali kugundabe” alidi akufa, yachitira ripoti tero The Sunday Times ya ku London. Osuliza njira ya mankhwala ya kupereka ziwalo za “mitima yopitirizabe kugunda” anena kuti kufufuza kogwiritsiridwa ntchito kudziwa imfa mu nkhani zoterezi kuli “mwalamulo kolakwika.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti, malinga ndi ripotilo, mtembo ku umene ziwalozo zimachotsedwako kaŵirikaŵiri umayankha ku mpeni wa sing’anga wotumbulayo pamene kulasa koyamba kwapangidwa. “Miyendo imaimitsidwa mu kuyankha kochinjiriza, ndipo minofu m’mimba imakungana molimba, kuyankha ku kutumbulako. . . . Mlingo wa kuyenda kwa mwazi wa woperekayo ndi mlingo wa kumenya kwa mtima zonse ziŵiri zimakwera pamene kutumbulidwa kuyambika . . . , zizindikiro zimenezi pa kutumbulidwa kwanthaŵi zonse zimasonyeza kuti . . . wodwalayo anali kumva kupweteka,” yadziŵitsa tero Times. Kulongosola kudera nkhaŵa pankhaniyo, woweruza mmodzi anadziŵitsa kuti: “Pamawonekera kwa ine kukhala kusiyana kokulira pakati pa zomwe zitchedwa kufa kwa bongo ndi imfa ya thupi. . . . Chowonadi cha nkhaniyo chiri chakuti ngati afuna ziwalo zako . . . iwo amachotsako ziwalo zina zapadera pamene usanafe mlingaliro lakuti inu ndi ine tingachimvetsetse icho.”
Kuchepetsa Kubala mu China
Kwa zaka khumi China watenga kugwira ntchito kwamphamvu kwa kuchepetsako mlingo wa obadwa a m’dzikolo. Kulingana ndi nyuzipepala ya Chifrench yatsiku ndi tsiku Le Figaro, lamulo la kubala mwana mmodzi yekha “liri lopambana koma liri ndi mbali zina zomvetsa mantha. . . . Mwamwambo, mabanja a chiChinese amafuna kukhala ndi mwana wa mwamuna. Chotero ana a akazi kaŵirikaŵiri amalandira kulonjeredwa koipa, popeza kuti okwatirana aŵiri amachipeza kukhala chovuta kulandira wolowa m’malo wamkazi.” M’maiko ambiri, maphunziro a kubadwa 1,000 adzasonyeza chiŵerengero chimodzimodzi chokulira kapena chochepera cha ana amuna ndi akazi. Mu China, ngakhale ziri tero, “pa kubadwa kolembetsedwa 1,000 [kulembetsa kumachitika milungu inayi pambuyo pa kubadwa], pali anyamata 660 kaamba ka atsikana 340.” Kodi nchiyani chimene chimachititsa kusiyana kwakukuluko pakati pa ziŵerengero ziŵirizo? Le Figaro yadziŵitsa kuti: “Chikuwonekera chotsimikizirika kuti mamiliyoni a ana achitsikana akuphedwa chaka chirichonse.”
Kusuta Kumapha
Ndudu zimapha chifupifupi chikwi zana limodzi la anthu chaka chirichonse mu United Kingdom, yalengeza tero Faculty of Community Medicine mu ripoti lawo Charter for Action. Ziŵerengero zavumbulanso kuti maperesenti 90 a imfa za kansa ya mapapo zonse mu Britain, kuphatikizapo ndi gawo lachitatu la imfa kuchokera ku mitundu ina ya kansa, zingakhale zochititsidwa ndi chizoloŵezi cha kusuta. Lamulo latsopano lalunjikitsidwa pa kuchinjiriza anthu achichepere ku matumba atsopano ochirikizidwa a fodya. Mu Britain, kugulitsa kwa zotulutsidwa za fodya kwa awo a zaka za pansi pa 16 kumafikira ku £90 miliyoni ($130 miliyoni, U.S.) pa chaka.
Kokha Chifukwa Chakukhala Kumeneko
Anthu onse aku Alaska—amuna, akazi, ndi ana—analandira cheki ya $556.26 pa kutha kwa chaka chatha. Uko kunali kugawana kwawo kwa $296 miliyoni imene inagawidwa pakati pa nzika zokhala ku Alaska 531,911. Ndalamazo zinachokera ku mapindu a mafuta kuchokera ku kutukuka kwa minda ya boma. Peresenti imodzi imaikidwa mu thumba, lomwe tsopano liri ndi $7 biliyoni, kotero kuti Alaska idzamwazikana pamene mafuta atha. Theka la ndalama zopezedwa zaperekedwa kwa anthu a ku Alaska chaka chirichonse chiyambire pamene inayamba mu 1982.
Chikepe Chachikulu Koposa cha Bwato
Dipartimenti ya ntchito ya madzi ya ku Belgian tsopano ikumanga chikepe chachikulu koposa cha bwato m’dziko. Pa Canal du Centre pakati pa Mons ndi La Louvière (mizinda iŵiri ya ku Belgian), pali kusiyana kwa mapazi 223 (68 m) mu mlingo wa madzi. Kufikira tsopano, zikepe zinayi zakale za hydraulic, za mapazi 56 chimodzi ndi chimodzi (17 m) mu utali, zakhala zokhoza kunyamula mabwato amatani 300. Koma chikepe chatsopano chomwe chikumangidwa chidzakhala cha mapazi 380 (116 m) mu msinkhu, mapazi 427 (130 m) mu utali, ndipo chidzakhala chokhoza kutenga unyinji wa matani 2,000. Icho chidzakhala ndi matanki aŵiri a mapazi 368 (112 m) mu utali ndi mapazi 40 (12 m) mu lifupi. Monga mmene nyuzipepala ya Chifrench Le Monde inalongosolera, “chikepe cha Strepy-Thieu chiri chitsimikiziro chakuti anthu a ku Belgian akukhulupirirabe mu maulendo a pamadzi.”
Zizindikiro Zotsutsana
Chomwe chinayamba monga njira zochinjiriza kwenikweni chatembenukira tsopano kukhala zinthu zokometsera. Poyambirira, zinthu za mainchi asanu (13 cm), zizindikiro zopangidwa monga miyala yonyezimira, zomamatizidwa ku galasi la zenera la kumbuyo la galimoto ndi chomamatizira, zinalinganizidwa kuchenjeza onyendetsa galimoto ena kuti wachichepere anali mkatimo kotero kuti angakhale osamalitsa kwenikweni. Ndipo mu zaka ziŵiri zapita, zizindikiro mamiliyoni ambiri zomwe zimati “Khanda liri Paulendo!” kapena “Mwana ali Paulendo!” zagulitsidwa kwa makolo odera nkhaŵa mu United States. Lerolino, ngakhale ziri tero, mamiliyoni ambiri a zoseketsa akusonyezedwa, zomwe zimanena zinthu zonga ngati “Khanda Likuyendetsa Galimoto!” “Palibe Aliyense Paulendo!” ndi “Apongozi Mkati mwa Choikamo Zinthu cha Galimoto.” Nduna zochinjiriza ngozi za pa msewu zikufuna kuti zizindikiro zonsezi zichotsedwe, zikumalongosola kuti zimachinjiriza kuwona kwa woyendetsa galimoto ndipo ziri zochititsa za ngozi.