Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 10/8 tsamba 26-27
  • Kumanani ndi Kasenye Kakang’ono Koposa m’Dziko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumanani ndi Kasenye Kakang’ono Koposa m’Dziko
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwopsyedwa kwa Wopulumuka Wang’ono
  • Zilumba za Faeroe Zinalumikizana Mochititsa Chidwi
    Galamukani!—2010
  • “Anthu Okhala Ngati Mfuko”
    Galamukani!—1991
Galamukani!—1987
g87 10/8 tsamba 26-27

Kumanani ndi Kasenye Kakang’ono Koposa m’Dziko

CHAKA chinali 1935. Mlimi wa ku Chile ankalima nthaka yake mu mbali zokongola za mapiri a Curicó. Mwadzidzidzi, anamva agalu akupitikitsa chomwe anaganizira kukhala kalulu. Tangolingalirani kudabwitsidwa kwake pamene nyama yonga mbulu mu kapangidwe, yowoneka monga mbuzi, inathaŵa kuchokera mu ngozi ndi kupeza chipulumutso pakati pa miyendo yake. Akuyang’ana pansi pa cholengedwa chonjenjemeracho, mlimiyo anachizindikira (kwawoko) kukhala kapudu, kasenye kakang’ono koposa m’dziko.

Kasenye kochepetsetsa kosavulazaka sikawoneka kaŵirikaŵiri, popeza kamakhala m’mbali zakutali za mapiri. Kamangobwera kunja kokha kudzadya zipatso, masamba, ndi zomera zina koma kamathaŵa mwamsanga kukabisala pamene nzeru zake za kumva ndi kununkhiza zakachenjeza ponena za ngozi. Kapudu kamakonda mbali za nkhalango za mdima bii, popeza kuti kudzivumbula mwachindunji ku dzuŵa lowala kwa nthaŵi yochepera chabe monga maora atatu kungapangitse imfa yake.

Panali kudziŵika kochepera ponena za chilengedwe cha manthachi kotero kuti kokha chifupifupi pothera pa zaka zana m’pamene odziŵa za nyama anazindikira kuti simbuzi kapena nkhosa. Iwo anakadziŵa kukhala kasenye, popeza kuti kakamuna kamataya mainchi 2.5 kufika ku mainchi 3.5 (6 kufika ku 9 cm) a zisonga zake, kapena nyanga, kamodzi pachaka. Pali, mchenicheni, mitundu iŵiri ya apudu. Mtundu womwe panthaŵi imodzi unali wambiri chakumadzulo kwa Chile ndi Argentina unali ndi ubweya wa mtundu wofiira. Tafuko lake chakumadzulo mu nkhalango za ku Colombia, Peru, ndi Ecuador tiri tamtundu wodera pang’ono. Kotalika chifupifupi mainchi 16 (40 cm) ndipo kotanimpha kuchokera pa mainchi 28 kufika ku 31 (70 kufika ku 80 cm), kapudu kamalemera chifupifupi mapaundi 22 (10 kg) katatha kukula. Kanyamako kali ndi kawonekedwe kapadera ka kukhota, popeza kuti miyendo yake ya kutsogolo iri yaifupi pang’ono kuposa miyendo yake ya kumbuyo.

Kuwopsyedwa kwa Wopulumuka Wang’ono

Ngakhale kuti kapudu kali kamanyazi mopambanitsa, iko mwachiwonekere kamakonda anthu ndipo kangawakhulupilire. Apudu ambiri amatsatira nkhosa kapena ng’ombe pochoka kukadya, kokha kukapitikitsidwa ndi agalu a mlimi. Kaŵirikaŵiri, ofufuza omwe amapeza chipambano cha kudaliridwa ndi pudu amadzafupidwa mwa kunyambitidwa kwa manja kapena nkhope yawo ndi bwenzi lawo latsopano. Wofufuza matenda anyama wina anapanga chibwenzi ndi pudu wamkazi yemwe analumphira panchafu pake, kunyambita nkhope yake, ndiyeno kumukankha iye ndi mutu wake kuloza kuchisa chake, mwachiwonekere kumusonyeza iye mwana wake wobadwa chatsopano.

Pamene kuli kwakuti pudu ali ndi adani achibadwa oterowo onga ngati nkhandwe, puma, bvumbwe, ndi kadzidzi, m’dani wake wamkulu ndi munthu. M’nthaŵi za kumbuyo, kasenye kakang’ono kankayendayenda mwaufulu kwambiri, kakumagwiritsira ntchito liwiro lake ndi nzeru kuthawa adani. Kapudu kadziŵika kukhala kakuthawa kubwerera mu njira zake zoyendera kapena kusambira pamwamba pa madzi kufuna kunyenga nkhandwe kapena puma. Koma tsopano, kaamba ka kuwononga nkhalango kochitidwa ndi munthu, mudzi wa pudu ukuzimilirika zolimba. Chotero, pudu wasinthira kukhala mu mbuna zopangidwa mu chisamba cha mdima bii. Pokhala kanyama kaudongo, kali ndi malo apadera mu mbuna zake kaamba ka kudya, kugona, ndi kudzithandiza, ndipo sikamasiyanitsa zimenezi kupyola mu moyo wake. Kuzolowerana ndi mbuna kuli mfungulo yake ya kupulumuka. Ngakhale kuti kapudu kali kaliwiro kwambiri ndi kodziwa kusambira mofulumira ndithu, iko kali kosavuta kugwidwa mu minda yopanda kanthu. Koma izi siziri tero mkati mwa mbuna zake kumene, wofufuza mmodzi amati, “kamauluka monga chipolopolo,” kumusiya kumbuyo wopitikitsa.

Ngakhale kuti kusaka pudu kuli koletsedwa, anthu ena osatsatira lamulo aphunzira kugwira kapena kupha cholengedwa cha mtendere chaching’onochi. Osakawa amafulumizidwa ndi kulakalaka kwa ubweya wolemera wa nyamayi, nyama yokoma, kapena mtengo umene osunga nyama a m’maiko ena ali ofunitsitsa kulipira kaamba ka chizindikiro chaumoyo. Iwo aphunzitsa tiagalu tating’ono kupitikitsa kapuduka kuchoka kunja kwa mbuna ndi kuthawira komwe kulibe kanthu. Koma popeza kuti apudu angapambane agalu kusambira, iwo amathawira ku mtsinje wapafupi kumenenso anthu amayembekezera m’mabwato kuti awagwire. Nyamazo kaŵirikaŵiri zimavulazidwa, ndipo kulingana ndi wofufuza mmodzi, zoposa maperesenti 80 zimafa kokha kaamba ka mantha.

Mukhoza kuwona, kuti manyazi ali chofooka cha pudu. Katawopsyedwa, maso ake amawoneka kukhala atadzazidwa ndi misozi, kamanthunthumira, ubweya wake umaimirira, ndipo kaŵirikaŵiri kanyamako kamafa ndi nthenda ya mtima. Kaamba ka chifukwa ichi, ngakhale kuti apudu asungidwa monga zoweta ndi mabanja a m’midzi ndi mayuniversite, tiasenye timeneti sitiwoneka kuti timakhalitsa mu ukapolo. Ito kaŵirikaŵiri timafa popanda chochititsa chirichonse, timafanso kaamba ka kupsyinjika kwa ukapolo. Kapudu kamakonda ufulu.

Chinawonedwa kuti kapudu kangagwirizane mwamsanga ndi ndandanda ya mitundu ya nyama zoyamwitsa 68 zomwe zatha mu zana lino. Komabe, maphunziro a posachedwapa ochitidwa ndi wofufuza wina wogwira ntchito ku World Wildlife Foundation analingalira kuti kapudu kangakhoze kupulumuka. Motani? Mwakuphunzira kusinthira ku mikhalidwe yatsopano ndi njira zake za mu mbuna. Izi siziri tero ndi mkango wa m’mapiri a ku Chile, kapena puma, imene iri pangozi mwachiwonekere ya kusakhalako. Ziri zowona mochulukira chotani nanga kuti mu mikhalidwe yopsyinja kapena yosintha chimakhala bwino kukhala wokhoza kusintha ndi waubwenzi kuposa kukhala wowopsya ndi wa nkhalwe!

Tingoyembekeza kuti kapudu kangakhoze kupulumuka kufikira dongosolo la mtendere la kachitidwe ka zinthu katsopano, pamene zolengedwa zoterozo zidzasiya mbuna zawo zochinjirizira ndi kutulukira kunja kudzasangalala ndi ufulu popanda mantha. Kodi mudzakhalako kudzakumana ndi kasenye kakang’ono koposa m’dziko?

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

New York Zoological Society photos

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena