Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano Za m’Buku la 1 Timoteyo 1 TIMOTEYO ZA M’BUKULI 1 Mau oyamba (1, 2) Cenjezo lokhudza aphunzitsi abodza (3-11) Cisomo cimene Paulo anacitilidwa (12-16) Mfumu yamuyaya (17) “Kumenya nkhondo yabwino” (18-20) 2 Kupemphelela anthu osiyana-siyana (1-7) Mulungu mmodzi komanso mkhalapakati mmodzi (5) Dipo la anthu onse lokwanila ndendende (6) Malangizo kwa amuna ndi akazi (8-15) Kubvala mwaulemu (9, 10) 3 Ziyenelezo kuti munthu akhale woyang’anila (1-7) Ziyenelezo za atumiki othandiza (8-13) Cinsinsi copatulika ca kudzipeleka kwa Mulungu (14-16) 4 Cenjezo lokhudza ziphunzitso za ziwanda (1-5) Mmene munthu angakhalile mtumiki wabwino wa Khristu (6-10) Masewela olimbitsa thupi komanso kudzipeleka kwa Mulungu (8) Uzisamala ndi zimene umaphunzitsa (11-16) 5 Mocitila ndi acikulile komanso acinyamata (1, 2) Thandizo kwa akazi amasiye (3-16) Kusamalila banja (8) Kucitila ulemu akulu ogwila nchito mwakhama (17-25) “Uzimwako vinyo pang’ono, cifukwa ca bvuto lako la m’mimba” (23) 6 Akapolo azilemekeza ambuye ao (1, 2) Aphunzitsi onyenga komanso anthu okonda ndalama (3-10) Malangizo kwa munthu wa Mulungu (11-16) Kulemela pa nchito zabwino (17-19) Teteza zimene unalandila (20, 21)