Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano Za m’Buku la Aefeso AEFESO ZA M’BUKULI 1 Moni (1, 2) Madalitso auzimu (3-7) Kusonkhanitsa zinthu zonse kwa Khristu (8-14) “Dongosolo” pa nthawi yoikidwilatu (10) Kuikidwa cidindo ndi mzimu woyela monga cikole cotsimikizila (13, 14) Paulo anathokoza Mulungu kaamba ka cikhulupililo ca Aefeso ndipo anawapemphelela (15-23) 2 Anapangitsa kuti akhale amoyo mogwilizana ndi Khristu (1-10) Anagwetsa cipupa cimene cinali kuwalekanitsa (11-22) 3 Cinsinsi copatulika cinaphatikizapo anthu a mitundu ina (1-13) Anthu a mitundu ina adzalamulila pamodzi ndi Khristu (6) Colinga camuyaya ca Mulungu (11) Apemphelela Aefeso kuti akhale ozindikila (14-21) 4 Mgwilizano m’thupi la Khristu (1-16) Mphatso za amuna (8) Umunthu wakale komanso watsopano (17-32) 5 Malankhulidwe abwino komanso khalidwe loyela (1-5) Muziyenda ngati ana akuwala (6-14) Dzadzidwani ndi mzimu (15-20) Muziigwilitsa nchito bwino nthawi yanu (16) Malangizo kwa amuna ndi akazi okwatila (21-33) 6 Malangizo kwa ana ndi makolo (1-4) Malangizo kwa akapolo ndi ambuye (5-9) Bvalani zida zonse zankhondo zocokela kwa Mulungu (10-20) Moni womaliza (21-24)