Mawu a M'munsi
a Tsiku lachiyuda linkayamba madzulo. Malinga ndi kalenda yathu, Nisani 14 ameneyo anayamba madzulo pa Lachinayi, March 31, kufikira pakuloŵa kwa dzuŵa Lachisanu madzulo, April 1. Chikumbutso chinayambitsidwa pa Lachinayi madzulo, ndipo imfa ya Yesu inachitika pa Lachisanu masana a tsiku lachiyuda lomwelo. Anauka patsiku lachitatu, Sande mmamaŵa.