JUNE 15-21, 2026
NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika
Muziona Mavuto Moyenera
“Ngakhale kuti ndinakumana ndi zowawa komanso mavuto, ndinapitirizabe kukonda malamulo anu.”—SAL. 119:143.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiphunzira mmene kuona mavuto moyenera kungatithandizire kuti tithe kulimbana nawo.
1-2. Kodi timafunika kuchita chiyani kuti tikwanitse kulimbana ndi mavuto? (Onaninso chithunzi.)
KODI panopa mukukumana ndi zinthu zopanda chilungamo, anthu a m’banja lanu akukutsutsani, kapena mukuzunzidwa chifukwa cha zimene mumakhulupirira? Kodi mukuvutika ndi matenda enaake kapena mavuto obwera chifukwa cha uchikulire? Kapena kodi mwakumana ndi vuto lina lake lalikulu, mwachitsanzo imfa ya munthu amene mumamukonda? Mofanana ndi nkhosa zina zonse za Yehova zomwe ndi zamtengo wapatali, moyo wanu ukhoza kukhala “wodzaza ndi mavuto komanso chisoni.”—Sal. 90:10.
2 Kuti tikwanitse kulimbana ndi mavuto athu tiyenera kumawaona moyenera. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingayerekezere mavuto amene timakumana nawo ndi zinthu zoopsa zimene dalaivala angakumane nazo pamsewu. Potengera zimene wakumana nazo, akhoza kukhotera kumanzere kapena kumanja, kuchepetsa liwiro kapena kungoimiratu. Kuti dalaivala adziwe zoyenera kuchita, ayenera kuona kaye bwinobwino zinthu zoopsazo. Koma ngati mawindo ake ndi akuda chifukwa cha matope sangathe kuona bwinobwino. Mofanana ndi zimenezi, kuti tikwanitse kulimbana ndi mavuto athu tiyenera kumawaona mmene Yehova amawaonera. Munkhaniyi tikambirana (1) zimene tingachite kuti tiziona mavuto athu moyenera, (2) zimene zingachitike ngati sitikuona mavuto moyenera, ndiponso (3) zimene tingachite kuti tipitirize kuona zinthu moyenera tikakumana ndi mavuto.
Tiyenera kumaona mavuto athu moyenera kuti tithe kulimbana nawo (Onani ndime 2)
KUONA MAVUTO ATHU MOYENERA
3. M’dziko loipa limene tikukhalamoli, kodi ndi mfundo iti imene tiyenera kuivomereza?
3 N’zosatheka kupeweratu mavuto m’dziko loipali. Tonsefe timakumana ndi mavuto chifukwa choti tikukhala m’dziko lolamulidwa ndi Satana komanso si ife angwiro. Pamene mapeto akuyandikira tizikumana ndi mavuto ambiri kaya a m’chilengedwe kapena oyambitsidwa ndi anthu, kapenanso obwera chifukwa cha zoipa zimene anthu ena achita. (Mat. 24:8; 2 Tim. 3:13) Ngati Yehova atathetsa mavuto onsewa panopa, zingaoneke ngati akuthandiza Satana kulamulira dzikoli. Choncho m’dziko loipali palibe chimene tingachite kuti tisakumane ndi “tsoka.”—Mlal. 9:12.
4. Kodi Akhristu amakumana ndi mavuto enanso ati?
4 Akhristu amakumananso ndi mavuto ena. Nthawi zambiri Yesu ankauza ophunzira ake kuti adzazunzidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira. (Mat. 24:9; Yoh. 16:2) Choncho sitidabwa tikamazunzidwa ndipo chikhulupiriro chathu chimakhalabe cholimba. (1 Ates. 3:3, 4) Tikamapirira mayesero chifukwa choti tili ndi chikhulupiriro cholimba sitikayikira kuti tikupitiriza kuyenda pamsewu wopita ku moyo wosatha. Kuwonjezera pamenepa timasonyeza mbali imene tili pa nkhani yaikulu yokhudza Yehova ndi Satana. Pofuna kudetsa dzina la Mulungu, Satana amanena kuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. Iye amakonda kulimbana kwambiri ndi atumiki a Yehova pofuna kusonyeza kuti zimene amanenazo ndi zoona. (Yobu 1:9-11) Koma Yehova amasangalala kwambiri tikamapirira chifukwa chomukonda.—Miy. 27:11.
5. Kodi tikuphunzira chiyani pa Mlaliki 7:13, 14? (Onaninso zithunzi.)
5 Yehova amalola kuti tizikumana ndi mavuto. Yehova sachita zinthu zoipa kapena kutiyesa ndi zinthu zoipa. (Yak. 1:13) Komabe Mfumu Solomo inalemba kuti ‘Mulungu woona anapanga’ “tsiku la tsoka.” (Werengani Mlaliki 7:13, 14.) Nthawi zambiri Baibulo likamanena kuti Yehova wachita chinachake limangotathauza kuti wachilola kuti chichitike. Solomo anapereka malangizo abwino otithandiza kuti tiziona moyenera mavuto athu. Choyamba, tizivomereza kuti m’dziko la Satanali masiku ena zinthu zizitiyendera bwino koma masiku ena tizikumana ndi mavuto. Tikakhala ndi tsiku labwino, tiziyamikira Mulungu chifukwa cha ubwino wake ndipo tiziona kuti tsikulo ndi mphatso imene iye watipatsa. Chachiwiri, Solomo akutikumbutsa kuti ‘sitidziwa chilichonse chimene chingatichitikire’ pa tsiku, kaya chabwino kapena choipa. Mavuto osayembekezereka amagwera anthu olungama ndi osalungama omwe.
Tizivomereza kuti m’dziko la Satanali masiku ena zinthu zizitiyendera bwino koma masiku ena tizikumana ndi mavuto (Onani ndime 5)
6. N’chifukwa chiyani Yehova angalole kuti tikumane ndi mavuto? (Aheberi 12:7, 11)
6 Tikamaona mavuto athu moyenera, timazindikira kuti Yehova akutiphunzitsa kuti tisamadzidalire koma tizidalira iyeyo. Nthawi zonse Yehova amaona mavuto amene tikukumana nawo, amakhudzika ndipo amatithandiza. Ngakhale pamene walola kuti tiyende “mʼchigwa chamdima wandiweyani,” amapitiriza kutitsogolera, kutitsimikizira kuti amatikonda komanso kutipatsa mphamvu kuti tipirire. (Sal. 23:4) Mavuto angatithandizenso kuzindikira makhalidwe amene tikufunika kukhala nawo ndipo Yehova angatithandize kukhala ndi makhalidwewo. (Werengani Aheberi 12:7, 11.) Mwachitsanzo, Yobu ankafunika kuyesetsa kuti akhale wodzichepetsa. Yehova sanachititse mavuto a Yobu, koma anangowalola ndipo anagwiritsa ntchito mavutowo pomuthandiza kuphunzira zinthu zofunika. (Yobu 42:1-6) Kaya takumana ndi mavuto otani, timadziwa kuti Yehova sangalole kuti tikumane ndi mavuto amene angatiwononge mpaka kalekale. Tikamapirira mavuto athu mokhulupirika ‘timagonjetsa zinthu zonse.’—Aroma 8:35-39.
7. N’chifukwa chiyani timakhalabe osangalala ngakhale pamene tikuzunzidwa chifukwa cha zimene timakhulupirira?
7 Tikhoza kumasangalala tikamazunzidwa. Ngati mukuzunzidwa chifukwa cha zimene mumakhulupirira, musamaganize kuti Yehova wasiya kukudalitsani. M’malomwake, kuzunzidwako ndi umboni wakuti akusangalala nanu. (Mat. 5:10-12) Tikamaona kuzunzidwa m’njira imeneyi, tikhoza kumasangalala ngati mmene atumwi ankachitira. (Mac. 5:40-42) Kuwonjezera pamenepa mukhoza kuthandiza anthu omwe si a Mboni kuphunzira choonadi ‘n’kumatamanda Mulungu.’ (1 Pet. 2:12) Mofanana ndi Yosefe, zinthu zikhoza kumakuyenderani bwino pamene mukukumana ndi mavuto osati pa nthawi yokhayo imene mavutowo atha.—Gen. 39:3, 23.
8. N’chiyani chingatithandizenso kupirira mavuto?
8 Mavuto athu adzatha. Zimene zinachitikira Yobu zimatikumbutsa kuti mavuto athu adzatha. Ndipotu “Yehova anadalitsa kwambiri mapeto a Yobu kuposa chiyambi chake.” (Yobu 42:12) Mofanana ndi zimenezi, Yehova adzatidalitsa kwambiri m’dziko latsopano. Panopa moyo wathu ndi wodzaza ndi mavuto komanso waufupi tikauyerekezera ndi moyo wosatha umene tidzasangalale nawo mtsogolo. Chimenechitu ndi chifukwa chomveka chothandiza aliyense wa ife kupirira mpaka pamapeto.—Mat. 24:13.
MAVUTO AMENE TINGAKUMANE NAWO CHIFUKWA CHOSAONA ZINTHU MOYENERA
9. Kodi chingachitike n’chiyani ngati sitikuona mavuto athu moyenera?
9 Kaya tikukumana ndi mavuto otani, tiyenera kumawaona moyenera kuti tisawonjezerenso mavuto ena. Mwachitsanzo, mwina tikhoza kumaganiza kuti Yehova ndi amene wachititsa kuti tikumane ndi mavuto. Kwa kanthawi, Yobu ankaona kuti Yehova ndi amene anayambitsa mavuto ake ndipo maganizo olakwikawa anamuchititsa kuti ‘azidziikira kumbuyo kuti iye ndi wolungama, osati Mulungu.’ (Yobu 32:2) Nayenso Naomi poyamba ankaimba mlandu Yehova chifukwa cha mavuto amene ankakumana nawo. (Rute 1:13, 20, 21) Yobu ndi Naomi akanapitiriza kukhala ndi maganizo olakwikawa akanawononga ubwenzi wawo ndi Yehova. (Miy. 19:3) Komabe Yehova anawathandiza kuti ayambirenso kuona mavuto awo moyenera ndipo anawadalitsa chifukwa chokhala okhulupirika.
10. Kodi tingayambe kukayikira za chiyani tikakumana ndi mavuto?
10 Ngakhale pamene tikudziwa kuti Yehova sachititsa kuti tikumane ndi mavuto, tingayambe kukayikira ngati akukhudzika ndi zimene zikutichitikira. Maganizo olakwikawa angachititse kuti tifooke. (Miy. 24:10) Mfumu Davide ndiponso mneneri Habakuku anakumana ndi mavuto ambiri ndipo nthawi zina ankakayikira ngati Yehova ankamvetsera mapemphero awo. (Sal. 10:1; Hab. 1:2) Komabe iwo sanasiye kupemphera. Yehova anayankha mapemphero awo n’kupitiriza kuwathandiza ndipo n’zimenenso adzachitire inuyo.—Sal. 10:17.
11. Kodi chingatichitikire n’chiyani ngati sitikuona mavuto athu moyenera?
11 Tikamalephera kuona mavuto athu moyenera, tikhoza kumadabwa tikakumana ndi mavutowo mwinanso kumaona kuti samayenera kutichitikira. (1 Pet. 4:12) Ophunzira a Yesu ankavutika kumvetsa mfundo yoti iye adzazunzidwa kwambiri. (Luka 18:33, 34) Ngakhale kuti Yesu anafotokoza momveka bwino za mavuto amene adzakumane nawo, Petulo ankaganiza kuti Mulungu sakanalola zimenezo. Yesu ankadziwa kuti maganizo amenewa akanamulepheretsa kuchita zimene Yehova amafuna, choncho anamudzudzula. (Maliko 8:31-33) Ndipotu ngakhale pambuyo pa imfa ya Yesu, ophunzira ake ankavutikabe kumvetsa chifukwa chake iye anaphedwa. Komabe Yesu sanasiye kuwathandiza. Pamene ankalankhula nawo ataukitsidwa, iye anawathandiza kuti ayambe kuona moyenera mavuto amene ankakumana nawo ‘powafotokozera Malemba momveka bwino.’ (Luka 24:25-27, 32, 44-48) Kuganizira zimene Yesu anawaphunzitsa kukanawathandiza kuti akozekere kutsutsidwa monga ophunzira ake. Ifenso kuganizira mfundo za m’Malemba kungtithandize kukonzekera mavuto.
12. Kodi kuona mavuto athu molakwika kugatikhudze bwanji?
12 Ngati tikuona mavuto athu molakwika tikhoza kumaganiza kuti ndi aakulu kwambiri kuposa mmene alili. Yesu anasonyeza mmene zimenezi zingachitikire mufanizo lake la ogwira ntchito m’munda wa mpesa. Antchito ena anakhumudwa chifukwa ankaganiza kuti sanalandire malipiro oyenera, koma mwini mundawo anauza m’modzi mwa iwo kuti: “Bwanawe, sindinakulakwire.” (Mat. 20:10-13) Ogwira ntchitowo anadandaula osati chifukwa choti panachitika zinthu zopanda chilungamo koma chifukwa chakuti zimene ankayembekezera sizinachitike. Masiku anonso a Mboni ena amafunika kulimbana ndi maganizo amenewa, ngati sanapatsidwe utumiki umene amaufuna kapena apemphedwa kuti asiye utumiki umene amaukonda. Ndiye kodi tingatani kuti tiziona mavuto athu moyenera?
ZIMENE TINGACHITE TIKAKUMANA NDI MAVUTO
13. Kodi n’chiyani chingachitike tikakumana ndi mavuto?
13 Muyenera kuti mumadziwa zimene Baibulo limanena zokhudza mavuto. Mwinanso munawerengerapo ena mavesi owathandiza kupirira. Komabe, inuyo mukakumana ndi mavuto mukhoza kuvutika kuti muziona zinthu moyenera. Mwachitsanzo, mungamaganize kuti Yehova akukulangani kapena sakumvetsera mapemphero anu. Ndiye kodi mungatani kuti mupitirize kuona zinthu moyenera?
14. Kodi mungamupemphe chiyani Yehova mukakumana ndi mavuto? (Afilipi 4:13)
14 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Muzimuuza vuto limene mwakumana nalo komanso mmene lakukhudzirani. Mungamuuzenso zenizeni zimene mukufuna kuti akuchitireni. Mungamupemphe mzimu wake woyera kuti ukupatseni mphamvu komanso nzeru zokuthandizani kupirira. Komabe muzikumbukira kuti Yehova akhoza kuyankha mapemphero anu m’njira imene simukuyembekezera. (Aef. 3:20) Iye angagwiritsenso ntchito angelo kapena abale ndi alongo kuti akuthandizeni. (Sal. 34:7) Choncho muzivomereza njira iliyonse imene wagwiritsa ntchito pokuthandizani. Yehova amapereka mzimu wake mowolowa manja ndipo mzimuwo ungakuthandizeni kupirira vuto lilionse.—Werengani Afilipi 4:13.
15. N’chiyani chingakuthandizeni kupirira mavuto? (Onaninso chithunzi.)
15 Musasiye kuchita zinthu zauzimu. Muzichita zimene mungathe panopa ngakhale kuti sizingafanane ndi mmene munkachitira poyamba. Pamene mukukumana ndi “zowawa komanso mavuto,” muziyesetsa kuwerenga kapena kumvetsera zinthu zimene zingakuthandizeni kuganizira kwambiri za Yehova komanso zimene amanena. (Sal. 119:143) Pitirizani kumawerenga Baibulo nthawi zonse, kuliphunzira, ndiponso kuganizira mfundo zake. Muzichita zonse zimene mungathe pa ntchito yolalikira, kusonkhana komanso kutengapo mbali. Muzichita zinthu ndi abale ndi alongo anu. Musamadzipatule ngakhale pamene mukumva kuti mukufunika kukhala panokha.—Miy. 18:1.
Muzichita zonse zomwe mungathe kuti mupitirize kuchita zinthu zauzimu (Onani ndime 15)
16. Kodi mungamakayikire chiyani mukakumana ndi mavuto, nanga mungathetse bwanji maganizowa? (2 Akorinto 10:4, 5)
16 Muzisintha mmene mukuonera zinthu. Mukakumana ndi mavuto mungafunike kugwetsa “zinthu zozikika molimba,” zomwe zikuphatikizapo maganizo odzikayikira komanso kukayikira Yehova. (Werengani 2 Akorinto 10:4, 5.) Mungakwanitse kulimbana ndi maganizo okayikirawa pogwiritsira ntchito zimene ‘mukudziwa zokhudza Mulungu’ zomwe zimapezeka m’Baibulo komanso m’mabuku athu. Mwachitsanzo, kodi mumakayikira kuti Yehova amakukondanibe? Ngati ndi choncho mungaphunzire zokhudza mtumwi Paulo. Pa utumiki wake anakumana ndi mavuto akuluakulu, komabe mavutowa anangomutsimikizira kuti anali mtumiki wovomerezeka wa Khristu. (2 Akor. 11:23-27) Kodi mumakayikira ngati Yehova anakukhululukirani machimo amene munachita m’mbuyomu? Ngati ndi choncho, mungasonkhanitse malemba amene amasonyeza kuti Yehova amakhululuka. (Yes. 43:25) Kenako muwerenge mavesiwo n’kumawaganizira mozama. (Sal. 119:97) Kodi mwakumana ndi vuto lalikulu lomwe lachititsa kuti muyambe kukayikira ngati Mulungu angakwaniritse lonjezo lake loti adzateteza atumiki ake okhulupirika? Muzifufuza nkhani zofotokoza chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika komanso mmene amatitetezera mwauzimu posatengera zimene takumana nazo. (Sal. 91:9-12) Muziwerenganso zokhudza abale ndi alongo omwe anakwanitsa kupirira mavuto akulu.a
17. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikakumana ndi vuto linalake lalikulu?
17 Kodi panopa mukusangalala ndi tsiku labwino, kapena kuti simukukumana ndi mavuto aakulu? Muzithokoza Yehova n’kumamutamanda chifukwa cha zabwino zimene wakupatsani. (Mlal. 7:14) Koma mukakumana ndi mavuto musasiye kuona zinthu moyenera ndipo muzipitiriza kudalira kwambiri Yehova. Mukamachita zimenezi, Yehova “adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.” (1 Akor. 10:13) Koma nanga bwanji za abale ndi alongo athu? Kodi tingawathandize bwanji akakukamana ndi mavuto? Tikambirana zimenezi munkhani yotsatira.
NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke
a Mwachitsanzo, nkhani yakuti “Banja Losangalala Linakumana ndi Zokhumudwitsa, Kenako Linayambiranso Kusangalalala” yomwe ili pa jw.org, ikufotokoza zimene M’bale David Maza ndi banja lake anachita kuti apirire imfa ya mwana wawo.