Kuulula Machimo—Kodi Pali Cholakwika?
“KUULULA ndiko kudziyeretsa kwauzimu, njira ya kuyambiranso, njira yakuchotsa chidetso. Ndimakonda kupita Kukaulula, ndikumuuza wansembe machimo anga, iye akundikhululukira ndi kumva bwino kumene kumatsatira.” Akutero Mkatolika wina wokangalika.—Bless Me, Father, for I Have Sinned.
Mogwirizana ndi New Catholic Encyclopedia, “nkwa wansembe yekha kumene Kristu anaperekako kapena kupatsa mphamvu ya kumanga ndi kumasula, ya kukhululukira ndi kubwezera” machimo. Bukhu lazilozero limodzimodzilo limati kuulula kwa nthaŵi zonse kuli ncholinga cha “kubwezeretsa chiyero cha moyo wodetsedwa ndi tchimo lalikulu ndi . . . kuyeretsa chikumbumtima cha munthu.” Komabe, makhalidwe a anthu m’maiko ambiri amasonyeza kuti kuulula kwa nthaŵi zonse sikumapangitsa ambiri amene amakuchita ‘kufutuka pazoipa, ndikuchita zabwino.’ (Salmo 34:14) Chotero kodi pali cholakwika?
Kodi ndi Dzoma Chabe?
Kuulula kungayambe monga dzoma wamba. Mu Ireland, kuulula koyamba kumachitidwa mwamsanga Misa yoyamba isanachitike. Ndipo kodi nzodabwitsa kuti msungwana wazaka zisanu ndi ziŵiri zakubadwa akalingalira kwambiri za chovala chaching’ono cha mkwatibwi, chokongola chimene adzavala kuposa za ‘kubwezeretsa chiyero cha moyo wodetsedwa ndi tchimo lalikulu’?
“Chinthu chimene chinandisangalatsa koposa chinali chovalacho, pambali pa kulandira ndalama kuchokera kwa achibale anga,” akuvomereza motero Ramona, yemwe anachita kuulula kwake koyamba pamene anali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. “Pakati pa asungwana onse omwe ndinadziŵa,” iye akupitiriza motero, “panalibe malingaliro auzimu. Panalibe aliyense wa ife amene analingalirapo za Mulungu panthaŵiyo.”
Kwenikweni, kupatsa ana achichepere thayo la kuulula machimo kwanthaŵi zonse kungatsogolere ku kachitidwe ka kubwerezabwereza mawu kosalingalira. “Ndinkagwiritsira ntchito mawu amodzimodziwo mobwerezabwereza,” akutero Michael, yemwe nayenso anayamba kachitidwe ka kuulula pamene anali wazaka zisanu ndi ziŵiri zakubadwa.
Ndemanga za Akatolika ena zogwidwa mawu m’bukhu lakuti Bless Me, Father, for I Have Sinned zimasonyeza kuti kuulula kunalibe phindu lauzimu lenileni kwa iwo ngakhale pamene anakula. “Kuulula kumakuphunzitsani kunama, chifukwa chakuti pali zinthu zina zimene sungathe kuziulula kwa wansembe,” anavomereza motero munthu wina. Kusiyana kwa kachitidwe ka ansembe kungagwiritsiridwe ntchito kupeza chilango chochepa. Ena anafunafuna woululitsa “wabwino” kuti apeze uphungu umene anafuna kuumva. Mkazi wachichepere wina ananena kuti: “Nditafunafuna kwa miyezi itatu, ndinadzipezera wondiululitsa wanga. Ndimawonana naye mwezi uliwonse, maso ndi maso m’chipinda choyanjanitsira, ndipo iye ngwabwinodi.” Mkatolika wina anati: “Mutachita mwaŵi, mungapeze wansembe yemwe ndi gonthi ndi wosatha kulankhula Chingelezi kusiyapo mawu ‘atatu [akuti] Tikuwoneni Mariya.’”
Pamenepa, mwachiwonekere pali chinachake cholakwika m’kuulula mwa njira yochitidwa ndi anthu ambiri. Koma Baibulo limasonyeza kuti kuulula machimo nkofunika, popeza limati: “Palibe amene abisa machimo ake amene adzapambana, yense woulula machimo ndi kuwataya adzapeza chifundo.”—Miyambo 28:13, The New Jerusalem Bible.
Kodi izi zimatanthauza kuti Mkristu ayenera kuulula machimo ake onse? Ngati nditero, kwa yani? Nkhani yotsatira idzasanthula mafunsoŵa.