Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 3/8 tsamba 17-19
  • Choonadi Ponena za Bodza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Choonadi Ponena za Bodza
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Bodza Loyamba
  • Zotsatirapo Zaimfa
  • Chizoloŵezi Chokhomerezeka
  • Mabodza Achipembedzo Lero
  • Kusamala Nkofunika
  • Kuimira Choonadi
  • Kodi Nchifukwa Ninji Kunama Kuli Kosavuta Choncho?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Tizilankhula Zoona Zokhazokha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Anataya Mwayi Wokhala M’Paradaiso
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Kodi Munthu Akafa Amapita Kuti?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 3/8 tsamba 17-19

Choonadi Ponena za Bodza

“WABODZA Iwe!” Kodi anakukalipiranipo ndi mawu opyoza mtima amenewo? Ngati anatero, ndiye kuti mosakayika mukudziŵa kupweteka kwake.

Monga momwe chotengera chokondeka chadothi chingaswekere chitagwera pansi, momwemonso bodza lingawononge unansi wamtengo wapatali. Zoona, pambuyo pa nthaŵi yaitali, mungakonze chowonongekacho, koma unansiwo sudzakhalanso monga woyamba uja.

“Aja amene amadziŵa kuti ananamizidwa,” likutero buku lakuti Lying—Moral Choice in Public and Private Life, “amakhala maso pazoyesayesa zatsopano zobwezeretsera mtendere. Ndipo amakumbuka zomwe ankakhulupirira ndi zochita zawo zakale ndi kuzigwirizanitsa ndi mabodza amene angowatulukirawo.” Atangotulukira chinyengo, unansi umene poyamba unali wabwino ndi wolankhulana momasuka ndi kudalirana umaduka chifukwa chokayikirana.

Chifukwa cha kukhumudwa konse kumene bodza limadzetsa, tingafunse kuti, ‘Kodi kachitidwe kopotoka kameneka kanayamba bwanji?’

Bodza Loyamba

Pamene Yehova Mulungu analenga anthu aŵiri oyamba, Adamu ndi Hava, anawapatsa mudzi wokongola wonga munda. Mudzi wawowo unalibiretu mtundu uliwonse wachinyengo. Ndithudi unali paradaiso!

Komabe, nthaŵi ina pambuyo pa kulengedwa kwa Hava, Satana Mdyerekezi anamfikira monyengerera. Anamuuza Hava kuti ngati atadya “zipatso zamtengo,” umene Mulungu analetsa, sadzafa monga momwe Mulungu ananenera kuti adzafa. M’malo mwake, ‘adzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.’ (Genesis 2:17; 3:1-5) Hava anamkhulupirira Satana. Anatenga chipatsocho nadya, ndipo anampatsako mwamuna wake. Koma m’malo mwa kukhala ngati Mulungu monga mmene Satana analonjezera, Adamu ndi Hava anakhala ochimwa osamvera, akapolo a chivundi. (2 Petro 2:19) Ndipo mwa kunena bodza loyambalo, Satana anakhala “atate wa mabodza onse.” (Yohane 8:44, Today’s English Version) Patapita nthaŵi, anthu atatu ochimwawo, anadziŵa kuti palibe angapambane ngati atanena bodza kapena kudalira bodza.

Zotsatirapo Zaimfa

Yehova anafuna kuti zolengedwa zake—kumwamba ndi padziko lapansi—zidziŵe kuti samalekerera kusamvera kwadala. Anachitapo kanthu mwamsanga mwa kuchiweruza cholengedwa chauzimu chopandukacho kuti chidzakhala kunja kwa gulu loyera la Mulungu moyo wake wonse. Ndiponso, potsirizira pake Yehova Mulungu adzatsimikiza kuti Satana wawonongedwa kotheratu. Izi zidzachitika pamene “mbewu” imene Mulungu analonjeza itswanya mutu wake.—Genesis 3:14, 15; Agalatiya 3:16.

Ponena za Adamu ndi Hava anawaingitsa m’munda wa Edene. Mulungu anamweruza Adamu kuti: “M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” Patapita nthaŵi, iyeyo ndi Hava anafa, monga mmene Mulungu anali ataneneratu.—Genesis 3:19.

Monga mbadwa za Adamu, banja lonse la anthu ‘lagulitsidwa kuuchimo.’ Anthu onse alandira choloŵa cha kupanda ungwiro chochititsa imfa. (Aroma 5:12; 6:23; 7:14, NW) Ha, zotsatirapo za bodza loyambalo zakhala zoopsa chotani nanga!—Aroma 8:22.

Chizoloŵezi Chokhomerezeka

Popeza kuti Satana ndi angelo amene anagwirizana naye kupandukira Mulungu sanawonongedwebe, sitiyenera kudabwa kuti akuuzira anthu ‘kunena mabodza.’ (1 Timoteo 4:1-3) Chotero, bodza lakhomerezeka mwa anthu. “Bodza laloŵerera mwa anthu,” inatero Los Angeles Times, “moti tsopano anthu angolizoloŵera.” Lero ambiri amagwirizanitsa bodza ndi zandale ndi anthu andale, koma kodi mumadziŵa kuti atsogoleri achipembedzo nawonso ali ndi mbiri yoipa ya bodza?

Adani achipembedzo a Yesu anafalitsa mabodza ponena za iye mu utumiki wake wapadziko lapansi. (Yohane 8:48, 54, 55) Anawatsutsa poyera, kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita.  . . Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.”—Yohane 8:44.

Kodi mukukumbukira bodza limene linafalitsidwa pamene manda a Yesu anapezedwa apululu pambuyo pa chiukiriro chake? Baibulo limati akulu ansembe ‘anapatsa asilikaliwo ndalama zambiri, nati, Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba Uja mmene ife tinali m’tulo.’ Bodza limeneli linafalitsidwa konsekonse, ndipo ambiri ananyengeka nalo. Ndiye anali oipatu atsogoleri achipembedzo amenewo!—Mateyu 28:11-15.

Mabodza Achipembedzo Lero

Kodi ndi bodza lofala liti limene atsogoleri achipembedzo akulinena lero? Nlofanana ndi limene Satana anauza Hava kuti: “Kufa simudzafai.” (Genesis 3:4) Koma Hava anafa, ndipo anabwerera kunthaka, kufumbi kumene anatengedwa.

Komabe, kodi anangooneka ngati wafa koma kwenikweni ali wamoyo wamtundu wina? Kodi imfa ndilo khomo loloŵera kumoyo wina? Baibulo silimasonyeza kuti mbali ina ya Hava inakhalabe ndi moyo. Sou yake sinapulumuke. Mwa kusamvera, anachimwira Mulungu, ndipo Baibulo limati: “Sou imene ichimwa—imeneyo ndiyo idzafa.” (Ezekieli 18:4, NW) Hava, monganso mwamuna wake, analengedwa ali sou yamoyo, ndipo moyo wake monga sou yamoyo unatha. (Genesis 2:7) Ponena za mkhalidwe wa akufa, Baibulo limati: “Koma akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Koma kodi matchalitchi amaphunzitsanji kaŵirikaŵiri?

Kaŵirikaŵiri matchalitchi amaphunzitsa kuti anthu ali ndi sou yosafa ndi kuti imfa imaimasula kuti iyambe moyo wina—wachimwemwe kapena wozunzika. Mwachitsanzo, The Catholic Encyclopedia imati: “Tchalitchi chimaphunzitsa momveka bwino za umuyaya wa zoŵaŵa za helo monga choonadi cha chikhulupiriro chimene wina sangatsutse kapena kukayikira popanda kukhala wampatuko ndithu.”—Voliyumu 7, tsamba 209, ya mu 1913.

Chiphunzitso chimenecho nchosiyana chotani nanga ndi zimene Baibulo limanena momvekera bwino! Baibulo limaphunzitsa kuti pamene munthu afa, “abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Salmo 146:4) Chotero, malinga ndi Baibulo, akufa samamva ululu uliwonse, pakuti sakudziŵa kanthu kalikonse. Nchifukwa chake Baibulo limalangiza kuti: “Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”—Mlaliki 9:10.

Kusamala Nkofunika

Monga momwe ambiri anasokeretsedwa ndi mabodza a ansembe m’tsiku la Yesu, momwemonso pali ngozi ya kusokeretsedwa ndi ziphunzitso zonyenga za atsogoleri achipembedzo alero. Anthu ameneŵa “asandutsa choonadi cha Mulungu cha bodza,” ndipo amachirikiza chiphunzitso chonyenga chakuti sou ya munthu simafa ndi lingaliro lakuti sou za anthu zidzazunzika m’moto wa helo.—Aroma 1:25.

Ndiponso, zipembedzo zalero kaŵirikaŵiri zimaphatikiza miyambo ya anthu, mafilosofi ndi choonadi cha Baibulo. (Akolose 2:8) Motero, malamulo a Mulungu onena za makhalidwe abwino—kuphatikizapo malamulo a kuona mtima ndi kugonana—amaonedwa ngati osinthika, m’malo mwa osasinthika. Zotsatirapo zake zili monga mmene magazini a Times akufotokozera kuti: “Mabodza amachuluka pamene anthu akukayikakayika, pamene anthu sakumvetsanso, kapena kumvana pa malamulo otsogoza khalidwe la wina ndi mnzake.”—Yerekezerani ndi Yesaya 59:14, 15; Yeremiya 9:5.

Kukhala m’dera limene anthu samalemekeza choonadi kumachititsa kumvera uphungu wa Mulungu wa kusalankhula bodza kukhala wovuta. Kodi nchiyani chimene chingatithandize kulankhula zoona nthaŵi zonse?

Kuimira Choonadi

Chikhumbo chathu cha kulemekeza Mlengi wathu ndicho chisonkhezero chabwino kwambiri cholankhulira choonadi. Moyenerera, Baibulo limamutcha “Mulungu wa choonadi.” (Salmo 31:5) Chotero, ngati tikhumba kukondweretsa Mlengi wathu, yemwe amadana ndi “lilime lonama,” tidzafuna kum’tsanzira. (Miyambo 6:17) Kodi tingatero motani?

Kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu kungatipatse nyonga yofunikira ya ‘kulankhula zoona yense ndi mnzake.’ (Aefeso 4:25) Komabe, kungodziŵa zimene Mulungu amafuna kwa ife sikokwanira. Ngati sitikonda kulankhula choonadi nthaŵi zonse, monga ambiri padziko lero, tifunikira kuyesayesa kutero. Tingafunikire kutsanzira chitsanzo cha mtumwi Paulo cha kudzilumira mano. “Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo,” analemba choncho Paulo.—1 Akorinto 9:27.

Thandizo lina pankhondo yakulankhula choonadi nthaŵi zonse ndilo pemphero. Mwa kupempha thandizo la Yehova, tingakhale ndi “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akorinto 4:7, NW) Ndithudi, kukhala ndi “mlomo wa ntheradi” ndi kutaya “lilime lonama” kungakhale nkhondo yeniyeni. (Miyambo 12:19) Koma ndi thandizo la Yehova zingatheke.—Afilipi 4:13.

Nthaŵi zonse kumbukirani kuti ndi Satana Mdyerekezi amene amapangitsa bodza kuoneka ngati nchinthu chabwino. Ananyenga mkazi woyambayo, Hava, nam’namiza modukidwa. Komabe, tikudziŵa bwino zotsatirapo zangozi za bodza la Satana. Banja la anthu lavutika mosaneneka chifukwa cha bodza limodzi ladyera ndi anthu atatu adyera—Adamu, Hava, ndi Satana.

Inde, choonadi ponena za bodza nchakuti nlofanana ndi mankhwala akupha. Komatu, tingachitepo kanthu. Tingasiye chizoloŵezi chonama ndi kusangalala kosatha ndi chiyanjo cha Yehova, Mulungu “wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.”— Eksodo 34:6.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Kunama kuli ngati mankhwala akupha

[Chithunzi patsamba 17]

Zotulukapo za bodza zili ngati kusweka kwa chotengera chadothi

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena