MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Musamade Nkhawa”
M’nthawi ya Aisiraeli Yehova ankathandiza anthu osauka. Kodi masiku ano iye amathandiza bwanji atumiki ake omwe ndi osauka?
Amawaphunzitsa kuti azikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ndalama.—Lu 12:15; 1Ti 6:6-8
Wawathandiza kuti azidziona moyenera. —Yob 34:19
Wawaphunzitsa kuti azigwira ntchito mwakhama komanso kupewa zizolowezi zoipa.—Miy 14:23; 20:1; 2Ak 7:1
Wawabweretsa m’banja la Akhristu omwe amasonyezana chikondi.—Yoh 13:35; 1Yo 3:17, 18
Wawapatsa chiyembekezo.—Sl 9:18; Yes 65:21-23
Sitiyenera kuda nkhawa ngakhale tikumane ndi mavuto otani. (Yes 30:15) Tikapitiriza kufunafuna Ufumu choyamba, Yehova adzatithandiza kupeza zinthu zofunika pa moyo.—Mt 6:31-33.
ONERANI VIDIYO YAKUTI CHIKONDI CHANU CHISATHE NGAKHALE KUTI . . . MUKUVUTIKA NDI UMPHAWI—CONGO, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi abale omwe amakhala pafupi ndi malo a msonkhano anasonyeza bwanji chikondi polandira abale ndi alongo amene anachokera m’madera akutali?
Kodi vidiyoyi yatiphunzitsa chiyani zokhudza chikondi cha Yehova kwa anthu osauka?
Kodi tingatsanzire bwanji Yehova ngakhale titakhala ndi zinthu zochepa?