Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 December tsamba 6
  • December 24-30

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December 24-30
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 December tsamba 6

December 24-30

MACHITIDWE 17-18

  • Nyimbo Na. 78 ndi Pemphero

  • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • “Muzitsanzira Mtumwi Paulo pa Nkhani Yolalikira Komanso Kuphunzitsa”: (10 min.)

    • Mac. 17:2, 3​—Paulo ankagwiritsa ntchito Malemba komanso mabuku ena akamaphunzitsa (“anakambirana” “kusonyeza umboni wolembedwa” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 17:2, 3, nwtsty)

    • Mac. 17:17​—Paulo ankalalikira kulikonse kumene ankapeza anthu (“pamsika” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 17:17, nwtsty)

    • Mac. 17:22, 23​—Paulo ankachita chidwi ndi anthu ndipo ankayamba kucheza nawo pogwiritsa ntchito zinthu zimene anthuwo ankakhulupirira (“Kwa Mulungu Wosadziwika” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 17:22, 23, nwtsty)

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

    • Mac. 18:18​—Kodi tinganene chiyani pa nkhani ya lonjezo la Paulo? (w08 5/15 32 ¶5)

    • Mac. 18:21​—Kodi tingatsanzire bwanji Paulo tikamayesetsa kukwaniritsa zolinga zathu zauzimu? (“Yehova akalola” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 18:21, nwtsty)

    • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

    • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mac. 17:1-15

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri. Musonyezeni ndi kukambirana mfundo za m’vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? (koma musaonetse vidiyoyi).

  • Ulendo Wobwereza Wachitatu: (Osapitirira 3 min.) Sankhani lemba lililonse ndipo gawirani buku kapena kabuku kamene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu.

  • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) jl mutu 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 70

  • Muziphunzitsa Komanso Kulalikira Uthenga Wabwino Mokwanira: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kulambira kwa Pabanja: Paulo Analalikira Mokwanira Uthenga Wabwino. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi banja lomwe lasonyezedwa m’vidiyoyi linazindikira bwanji mbali zimene linkafunika kusintha pa nkhani yolalikira? Kodi banjali linaphunzira zinthu ziti kuchokera pa utumiki wa Paulo? Nanga anapeza madalitso otani atatsatira zimene anaphunzirazo? Kodi ndi njira zina ziti zimene inuyo mungagwiritse ntchito pa kulambira kwa pabanja kuti muzilalikira mokwanira?

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 19 ¶1-9

  • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

  • Nyimbo Na. 72 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena