December 4-10
ZEFANIYA 1–HAGAI 2
Nyimbo Na. 151 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Funafunani Yehova Tsiku la Mkwiyo Wake Lisanafike”: (10 min.)
[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Zefaniya.]
Zef. 2:2, 3—Bwerani kwa Yehova, yesetsani kukhala olungama, yesetsani kukhala ofatsa (w01 2/15 18-19 ¶5-7)
[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Hagai.]
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Zef. 1:8—Kodi pavesili tikupezapo chenjezo lotani? (w07 11/15 11 ¶3)
Hag. 2:9—Kodi ulemerero wa kachisi wa Zerubabele unaposa ulemerero wa kachisi wa Solomo m’njira ziti? (w07 12/1 9 ¶3)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Hag. 2:1-14
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Kukambirana “Zitsanzo za Ulaliki.” Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyo. Limbikitsani ofalitsa kuti adzayesetse kugawira magazini ambiri a Galamukani! Na. 6 2017. Popeza tikufunitsitsa kudzalankhulana ndi anthu mwachindunji, tisadzasiye magaziniwa pakhomo limene palibe anthu.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zofunika Pampingo: (5 min.)
Chilankhulo Choyera Chimatithandiza Kukhala Mwamtendere Komanso Mogwirizana (Zef. 3:9): (10 min.) Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2012, tsamba 12, ndime 4. Onetsani vidiyo yakuti Anthu Omwe Ankadana, Anakhala Mabwenzi Apamtima.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 11 ¶1-8
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 136 ndi Pemphero