Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu August: Tidzagwira ntchito yapadera yogawira kapepala kodziwitsa anthu za webusaiti yathu ya jw.org/ny. September ndi October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! November ndi December: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?
◼ Ofesi ya nthambi imasunga mafomu a anthu amene afunsira utumiki wa pa Beteli kwa chaka chimodzi. Ofalitsa obatizidwa amene ali ndi zaka za pakati pa 19 ndi 35 ndipo anatumiza fomu yofunsira utumikiwu, ayenera kutumizanso fomu ina chaka chilichonse ngati sanaitanidwe.