Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Lemba la Yesaya 24:15 limanena kuti: “M’zilumba zakunyanja adzalemekeza dzina la Yehova.” Mogwirizana ndi mawu amenewa, chaka chatha, pa msonkhano wapadera umene unachitikira pa chilumba cha Chizumulu panasonkhana anthu okwana 50 ndipo anthu awiri anabatizidwa. Pachilumbachi pali mpingo umodzi wokha womwe uli ndi ofalitsa 20 ndipo ulinso ndi apainiya apadera amene akuthandiza kwambiri mpingowu.