Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/13 tsamba 4
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 4/13 tsamba 4

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu March ndi April: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamachita maulendo obwereza sonyezani munthuyo buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ngati mukuona kuti n’koyenera, mungamugawire kabuku kakuti Mverani Mulungu kapena kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha ndipo yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. May ndi June: Ofalitsa angagawire timapepala iti: Sangalalani ndi Moyo Wabanja, Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko? Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Baibulo, kapena kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Ngati mwapeza anthu achidwi, asonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena timabuku takuti Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. July: Gawirani kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu kapena timabuku iti: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira kapena kakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!

◼ Tikulimbikitsa mipingo yonse kuti iyenera kumatumiza lipoti la utumiki wakumunda pogwiritsa ntchito njira ya SMS pa foni ya m’manja. Ngati simungathe kutumiza lipoti la utumiki wakumunda pogwiritsira ntchito Intaneti pa Webusaiti yathu ya www.jw.org kapena polemba SMS pa foni, mungapitirize kutumiza malipotiwa kudzera pa fomu ya S-1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena