Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu August: Gwiritsani ntchito timabuku totsatirati: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! September: Gawirani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ngati n’kotheka, ofalitsa ayenera kuyesetsa kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo woyamba. October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Anthu amene asonyeza chidwi agawireni ndi kukambirana nawo kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? November: Gawirani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?