Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/09 tsamba 4
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 1/09 tsamba 4

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu January: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? February: Gawirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April: Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pangani maulendo obwereza kwa anthu amene anasonyeza chidwi, kuphatikizapo amene anabwera pa Chikumbutso kapena pamisonkhano ina koma sanayambebe kugwirizana ndi mpingo. Mungawapatse buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo ndi bukulo.

◼ Nkhani ya onse yatsopano imene oyang’anira madera adzayamba kukamba ndi yakuti “Kanani Zokopa za M’dzikoli Ndipo Tsatirani Zinthu za Ufumu.” Iwo adzayamba kukamba nkhani imeneyi mlungu woyamba wa March.

◼ Mipingo iyenera kukonzekera bwinobwino kudzachita Chikumbutso cha chaka chino Lachinayi, pa April 9, dzuwa litalowa. Mpingo uliwonse uyenera kuyesetsa kuti udzakhale ndi mwambo wakewake wa Chikumbutso. Ngati m’Nyumba ya Ufumu yanu mumasonkhana mipingo ingapo, mipingo inayo ingathe kupeza malo ena ochitirako Chikumbutso. Ngati n’kotheka, mukamaliza pazidzatha mphindi zosachepera 40 mpingo wotsatira usanayambe mwambo wawo wa Chikumbutso pofuna kuti aliyense adzakhale ndi mpata wocheza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena