Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu April ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Tidzayesetse mwapadera kupita kwa anthu amene angoyamba kumene kusonyeza chidwi, amene anafika pa Chikumbutso ndiponso pa nkhani yapadera, koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zambiri. Cholinga cha maulendowa chidzakhale kuyambitsa phunziro la Baibulo ndi anthu amene sanayambebe kuphunzira. June: Gawirani buku la Lambirani Mulungu Woona Yekha. July ndi August: Mungagwiritse ntchito kabuku kalikonse mwa timabuku tamasamba 32 iti: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndi What Happens to Us When We Die?
◼ Kuyambira mu April, tizitumiza mabaji a msonkhano wachigawo wa 2008 tikamatumiza mabuku. Simukufunika kuitanitsa mabajiwa. Ngati mpingo ukufuna mabaji owonjezera, itanitsani pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Muitanitse mapulasitiki oikamo baji a aliyense amene alibe mu mpingo wanu kapena amene yake inatayika.
◼ Alembi a mipingo azisunga mafomu okwanira a Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wokhazikika (S-205) ndi Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wothandiza (S-205b). Mungaitanitse mafomuwa pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Muzikhala ndi mafomu oti angakwanire chaka chimodzi. Musanatumize ku nthambi mafomu a anthu amene afunsira upainiya wokhazikika, onetsetsani kuti mafunso onse ayankhidwa.
◼ Ofesi ya nthambi imayenera kukhala ndi maadiresi ndi manambala a foni amene akugwira ntchito panopo a oyang’anira otsogolera ndi alembi onse. Zimenezi zikangosintha nthawi ina iliyonse, Komiti ya Utumiki ya Mpingo izilemba ndi kusaina fomu ya Kusintha Adiresi ya Woyang’anira Wotsogolera/Mlembi (S-29) ndi kuitumiza mwamsanga ku ofesi ya nthambi. Zimenezi zikuphatikizapo kusintha kulikonse kwa manambala a foni.
◼ Ngati mukukonza zopita ku dziko lina ndipo mukufuna kukapezeka pa misonkhano ya mpingo, msonkhano wadera, kapena msonkhano wachigawo, funsani masiku, nthawi, ndi malo a misonkhanoyo ku ofesi ya nthambi imene imayang’anira ntchito m’dziko limene mukupitalo. Maadiresi a maofesi a nthambi ali pa tsamba lomaliza la Yearbook yatsopano.
◼ Atumiki a Mabuku Adziwe Izi: Tikufuna kufotokoza zimene mawu amene amakhala pa mpambo wolongedzera akuti “Zoyembekezeredwa” amatanthauza. Ngati panthawiyo zinthu zimene mwaitanitsa palibe, pampambowo pamakhala mawu akuti “Zoyembekezeredwa.” Palibe chifukwa choitanitsiranso zinthuzo. Zinthuzo zikayamba kupezekanso, tidzakutumizirani. Dziwani kuti pangatenge nthawi yaitali ndithu kuti tikutumizireni zinthu zochokera ku nthambi za kutsidya la nyanja, monga ma CD-ROM, ma DVD ndi zinthu za zinenero za ku mayiko ena.
◼ Popeza kuti Utumiki Wathu wa Ufumu sukukhalanso ndi mbali yobwerezera mfundo za pamisonkhano yadera ndiponso masiku a msonkhano wapadera, ngati akulu akufuna kuti azibwereza mfundo za pamisonkhanoyi mu Msonkhano wa Utumiki ndi kukambirana malangizo amene akuona kuti angawagwiritse ntchito kwawoko, angachite zimenezi pa “Zosowa za pampingo.”
◼ Ma Compact Disc a MP3 Atsopano Amene Alipo:
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo (mpmy)—Chingelezi
Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja (mpfy)—Chingelezi
Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? (mpbh)—Chingelezi
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? (mprq)—Chingelezi
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako (mpgt)—Chingelezi
Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira (mpwe)—Chingelezi
Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso (mplr)—Chingelezi
Yandikirani kwa Yehova (mpcl)—Chingelezi
◼ Ma Compact Disc Atsopano Amene Alipo:
Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja (cdfy)—Chingelezi
Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira (cdwe)—Chingelezi
(Zapitirizidwa patsamba 7)
Zilengezo (Zachokera patsamba 5)