Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/07 tsamba 7
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Timapezera Ndalama Zoyendetsera Ntchito za Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Yehova Amakonda Opatsa Mokondwerera
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Ndalama Zothandizira pa Ntchito Yathu Yapadziko Lonse Zimachokera Kuti?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Mmene Yehova Amapititsira Patsogolo Ntchito Yake
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 1/07 tsamba 7

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi zingakhale zoyenera kukonza zoti anthu agulitse katundu wosiyanasiyana kapena achite zinthu zina zofuna kupezera ndalama n’cholinga chothandiza mpingo?

Si zachilendo kuti zipembedzo zikonze zinthu zopezera ndalama, monga kuphika zakudya, kugulitsa malonda, kapena kukonza zionetsero. Ngakhale kuti ena angaone kuti zinthu zimenezi n’zothandiza, kwenikweni imeneyi ndi mitundu ya kupemphetsa ndalama. Mboni za Yehova sizipeza ndalama m’njira imeneyo.

Magazini yachiwiri ya Watch Tower, ya August 1879, inanena mawu otsatirawa pofotokoza chifukwa chimene timakanira kutsanzira matchalitchi pankhani ya kupemphetsa ndalama: “Tikukhulupirira kuti amene akuyendetsa magazini ya ‘Zion’s Watch Tower’ ndi YEHOVA, ndipo kwa nthawi yonse imene zimenezi zidzakhale choncho, sidzapempha kapena kuchonderera anthu kuti aipatse ndalama. Iye amene ananena kuti: ‘Golide ndi siliva yense wa m’mapiri ndi wanga’ akadzalephera kupereka ndalama zofunikira, tidzadziwa kuti nthawi yoti tisiye kulemba magaziniyi yakwana.”

Timapitirizabe kumvera mfundo ya m’Malemba yakuti: “Aliyense achite mwa kutsimikiza kwa mtima wake, osati monyinyirika kapena mokakamizika ayi, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.” (2 Akor. 9:7) Mabokosi a zopereka amaikidwa m’Nyumba ya Ufumu kuti anthu athe kupereka ndalama mwakufuna kwawo. (2 Maf. 12:9) Sitichita kupemphetsa zopereka, ndiponso siziperekedwa n’cholinga chopezapo kenakake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena