Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 30, 2006. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya September 4 mpaka October 30, 2006. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. N’chifukwa chiyani kudekha n’kofunika polankhula, ndipo tingachepetse motani nkhawa? [be-CN tsa. 135 ndime 5–tsa. 137 ndime 2, mabokosi]
2. Pamene tafunsidwa za zikhulupiriro zathu, n’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito Baibulo poyankha? [be-CN tsa. 143 ndime 1-3]
3. Kodi tingatani kuti tikhale ndi luso logwiritsa ntchito Baibulo? [be-CN tsa. 144, bokosi]
4. N’chifukwa chiyani m’pofunika kugwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki, ndipo tingalimbikitse bwanji omvera kuti aziligwiritsa ntchito pa misonkhano ya mpingo? [be-CN mas. 145-6, mabokosi]
5. Kodi ndi zolinga ziwiri ziti zimene tiyenera kukhala nazo potchula mawu owerengera lemba? [be-CN tsa. 147 ndime 2]
NKHANI NA. 1
6. Kodi oyang’anira ayenera kukhala ndi mtima wotani akamasamalira maudindo awo mumpingo? [od-CN tsa. 27 ndime 2–tsa. 28 ndime 3]
7. Kodi n’chiyani chingachititse kuti anthu ena mumpingo akhale omasuka kuuza woyang’anira zakukhosi kwawo ndi kufunsira uphungu ndiponso malangizo pa nkhani zosiyanasiyana zimene iwo akukumana nazo zokhudza moyo wa m’banja? [od-CN tsa. 31 ndime 2–tsa. 33 ndime 2]
8. Kodi woyang’anira wa mpingo amene ali woyenerera kuphunzitsa ndi wotani? [od-CN tsa. 34 ndime 1–tsa. 35 ndime 1.]
9. Kodi Miyambo 2:1-5 amatanthauzanji pamene akutilimbikitsa kupitiriza kufunafuna nzeru, kudziwa, ndi kuzindikira “ngati siliva” ndiponso “chuma chobisika”? [be-CN tsa. 38 ndime 4]
10. Kodi anthu amayembekezera zotani kwa amuna amene akwaniritsa miyezo yachikristu yakukhala oyang’anira? [od-CN tsa. 35 ndime 2–tsa. 36 ndime 2]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi Davide ‘analinganiza ndi kutontholetsa moyo wake ngati mwana wom’letsa kuyamwa amake’ motani, ndipo ife tingam’tsanzire motani? (Sal. 131:1-3)
12. Kodi ndi chitonthozo chotani chimene chingapezeke pa mawu ouziridwa a pa Salmo 139:7-12?
13. Kodi ndi zitsanzo ziti za ukulu wa Yehova, zomwe zingatichititse kum’tamanda m’mapemphero athu ndi mu utumiki wa kumunda? (Sal. 145:3)
14. Ndi motani mmene kuopa Yehova kulili “chiyambi cha kudziwa” ndi “chiyambi cha nzeru”? (Miy. 1:7; 9:10)
15. Kodi n’chiyani chimaphatikizidwa pa “mawu anga” ndi “malamulo anga” zotchulidwa pa Miyambo 7:1, 2?