Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu September: Gawirani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Yesetsani mwapadera kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo wanu woyamba. Bwererani kwa aliyense amene munam’gawira bukuli n’cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo la panyumba. October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Munthu amene wasonyeza chidwi, muonetseni kabuku kakuti Dikirani! n’cholinga chokulitsa chidwi chomwe ali nacho pa zinthu za m’Baibulo. November: Tidzagawira buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Eninyumba akanena kuti alibe ana, apatseni kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? kapena kapepala kena koyenerera. December: Gawirani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mulibe buku limeneli, mungagawire Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kapena buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ngati mpingo wanu uli nawo.
◼ Mipingo iyambe kuitanitsa mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 2006 ndi Watchtower Library—2006 Edition ya pa CD-ROM potumiza oda yawo yotsatira ya mabuku. Zinthu zimenezi zili m’Chingelezi. Kumbukirani kuti Watchtower Library—2006 Edition inakonzedwera anthu obatizidwa okha ndipo mumaodetsa kudzera ku mpingo basi.
◼ Akulu akukumbutsidwa kuti atsatire malangizo amene anaperekedwa mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, masamba 21 mpaka 23, onena za anthu alionse ochotsedwa kapena odzilekanitsa amene angafune kubwezeretsedwa.
◼ Ndife osangalala kwambiri kulengeza kuti posachedwapa tidzakhala ndi sewero latsopano pakaseti m’Chichewa. Mutu wake ndi wakuti, “Anachitira Umboni Uthenga Wabwino Mokwanira.” Tikulimbikitsa onse amene ali ndi wailesi ya kaseti kuti aitanitse panopa sewero latsopanoli kudzera ku mpingo wawo. Mtumiki wa mabuku angaitanitse makaseti a sewerowa pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) pogwiritsa ntchito chizindikiro chakuti csdr04-CN.