Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira June 26, 2006. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya May 1 mpaka June 26, 2006. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi kusinthasintha mawu n’kutani, ndipo n’chifukwa chiyani kuli kofunika? [be-CN 111, mabokosi]
2. Kodi tingamasinthesinthe bwanji liwiro lathu pamene tikukamba nkhani? [be-CN tsa. 112 ndime 3 mpaka tsa. 113 ndime 1, bokosi]
3. Kodi tingatani kuti tizikamba nkhani yathu mwaumoyo, ndipo n’chifukwa chiyani luso limeneli lili lofunika? [be-CN tsa. 115 ndime 1 mpaka tsa. 116 ndime 2, mabokosi]
4. Pamene tikuphunzitsa ena, n’chifukwa chiyani kulankhula ndi mzimu waubwenzi kuli kofunika, ndipo n’chiyani chingatithandize kusonyeza luso limeneli? [be-CN tsa. 118 ndime 3 mpaka tsa. 119 ndime 5]
5. Fotokozani kufunika kogwiritsa ntchito manja ndi nkhope polankhula. (Mat. 12:48, 49) [be-CN tsa. 121, mabokosi]
NKHANI NA. 1
6. Kodi anthu mu mpingo amasonyeza motani kuti amagonjera Kristu monga mutu wa mpingo? [od-CN tsa. 19 ndime 1 mpaka tsa. 21 ndime 1]
7. Kodi mipingo imavomereza ndiponso kugwirizana motani ndi makonzedwe operekedwa ndi gulu? [od-CN tsa. 25 ndime 1 mpaka tsa. 27 ndime 1]
8. Kodi munthu wochenjera wotchulidwa pa Miyambo 13:16 ndi kamberembere? Fotokozani. [w04-CN 7/15 tsa. 28 ndime 3-4]
9. Kodi mzimu woyera umatumikira monga mthandizi m’njira zotani ndipo zimenezi ziyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani? (Yoh. 14:25, 25) [be-CN tsa. 19 ndime 2-3]
10. Kodi Yesu akubwera mu lingaliro lotani, ndipo ndi ‘kudza’ kotani kumene Yesu ananena pa Mateyu 16:28? [w04-CN 3/1 tsa. 16, bokosi]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi timaphunzira chiyani pa zimene Yobu anayankha Yehova, zolembedwa pa Yobu 42:1-6?
12. Kodi n’zinthu “zopanda pake” zotani zimene anthu amitundu akhala akulingalira? (Sal. 2:1, 2)
13. Kodi ndi maziko ati amene akupasuka? (Sal. 11:3)
14. Kodi ndi motani mmene Yehova ‘amabwezera zochuluka’ munthu wodzitama? (Sal. 31:23)
15. Kodi ndi mawu otonthoza otani opezeka mu Salmo 40, amene angatithandize kulimbana ndi kupanda ungwiro kwa thupi lathu lochimwa ndiponso mavuto a m’moyo uno? (Sal. 40:1, 2, 5, 12)