Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/05 tsamba 7
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 10/05 tsamba 7

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 31, 2005. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya September 5 mpaka October 31, 2005. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]

LUSO LA KULANKHULA

1. Kodi tingatani kuti tikamaphunzitsa anthu Mawu a Mulungu tiziwafika pamtima? (Mat. 13:19) [be-CN tsa. 258 ndime 1-2, bokosi]

2. Kodi n’chiyani chomwe tingachite kuti munthu winayo alankhule zakukhosi kwake, koma kodi n’chiyani chomwe tiyenera kusamala? [be-CN tsa. 259 ndime 1-2]

3. Tikamaphunzitsa, n’chifukwa chiyani kuli kofunika kugogomeza makhalidwe abwino a Yehova? [be-CN tsa. 260 ndime 1]

4. Kodi tingathandize bwanji ophunzira Baibulo athu kuzindikira zinthu zimene ayenera kusintha pamoyo wawo? [be-CN tsa. 260 ndime 4-5]

5. Kodi tingatani kuti tithandize ophunzira Baibulo kapena omvera athu kuyang’anitsitsa zolinga zawo pochita zinthu? [be-CN tsa. 261 ndime 5–tsa. 262 ndime 1]

NKHANI NA. 1

6. Kodi ‘kufuna’ Yehova mwakhama kumatanthauzanji, ndipo tingasonyeze bwanji kuti tikuchita zimenezi? (Aheb. 11:⁠6) [w03-CN 8/15 tsa. 25 ndime 2; tsa. 26 ndime 2-3; tsa. 27 ndime 2]

7. Kodi “chitsanzo cha mawu a moyo” n’chiyani, ndipo kodi akulu angasonyeze bwanji kuti amatsatira chitsanzo chimenechi? (2 Tim. 1:​13, 14) [w03-CN 1/1 tsa. 29 ndime 3–tsa. 30 ndime 1]

8. Kodi Yesu asanafotokoze za mkate wakumwamba panachitika zotani? [gt-CN mutu 54]

KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

9. Mogwirizana ndi lemba la 2 Mafumu 19:​32, 33, kodi n’chiyani chinachititsa kuti mfumu ya Asuri isalowe mu Yerusalemu? [w88-CN 2/15 tsa. 28]

10. Kodi n’chifukwa chiyani nkhani yopezeka pa 1 Mbiri 14:​8-17 inali yofunika kuiganizira mofatsa panthawi ya Yesaya, ndipo n’chifukwa chiyani Matchalitchi Achikristu masiku ano ayeneranso kuiganizira mofatsa? (Yes. 28:21) [w91-CN 6/1 tsa. 21 ndime 2-3]

11. Kodi lemba la 2 Mafumu 13:21 limalimbikitsa kulambira zinthu zopatulika?

12. Kodi Hezekiya anachita mgwirizano ndi Igupto? (2 Maf. 18:​19-21, 25)

13. Ngakhale kuti zolembedwa za chaka ndi chaka za moyo wa Aasuri sizichita kutchuliratu momwe Yehova anagonjetsera Sanakeribu modabwitsa, kodi n’chiyani chomwe chili chochititsa chidwi pa zomwe zinalembedwazo? (2 Maf. 19:​35, 36)

14. Kodi ndani anali atate wa Sealitiyeli? (1 Mbiri 3:​16-18)

15. M’masiku a Mfumu Sauli, kodi ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi limodzi la magawo awiri a fuko la Manase, anapereka chitsanzo chabwino chotani kwa atumiki onse a Mulungu masiku ano? (1 Mbiri 5:​18-22)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena