Bokosi la Mafunso
◼ Mwa Malemba, kodi Mkristu wodzipereka ayenera kuwaona motani mabungwe a anthu ogwira ntchito, ndipo kodi angatenge nawo mbali m’zochitika za mabungwewo?
Malemba amalangiza Akristu ‘kuganizira zinthu zaulemu pamaso pa anthu onse.’ Amatinso “ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.” Mfundo za mawu amenewa zingakhudzenso nkhani ya mabungwe a anthu ogwira antchito, chifukwa kuti munthu awalabadire angafunikire kukhala membala wa bungwe la anthu ogwira ntchito. Tiyeni tiyerekeze maudindo a munthu monga membala wa bungwe la anthu ogwira ntchito ndi maudindo ake monga nzika ya dziko. Munthuyo amapindula ndi mautumiki osiyanasiyana a boma chifukwa cha misonkho imene amapereka; mofananamo, kungakhale koyenera kuti iye azipereka msonkho ku bungwe la anthu ogwira ntchito, ndipo zimenezi zimapereka chitetezo ku ntchito yake. Choncho, palibe choletsa kuti Mkristu akhale membala wa bungwe la anthu ogwira ntchito, kupereka msonkho ku bungwelo, ndi kulabadira malangizo ake akuti anthu asapite kuntchito pa sitalaka.—Aroma 12:17; 1 Tim. 5:8.
Komabe, Mkristu sayenera kulowerera kwambiri m’zochitika za mabungwewo moti mpaka kupatsidwa malo audindo. Ngakhale panthawi ya sitalaka, sayenera kuchita nawo zionetsero kapena kuchita zinthu zina zosokoneza pofuna kukwaniritsa cholinga cha sitalakayo. Komanso, sayenera m’pang’ono pomwe kuchita nawo ziwawa za mikangano ya mabungwe a anthu ogwira ntchito, chifukwa “kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu.” “Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” Monga mmene Mkristu sakhalira mbali iliyonse m’nkhani zandale ndi m’nkhondo za m’dziko mwake, n’chimodzimodzinso Mkristu yemwe ndi membala wa bungwe la anthu ogwira ntchito. Satenga nawo mbali pa ntchito zoyendetsa bungwelo kapena pamikangano yokhudza za ndalama. Sayenera kukhalira mbali iliyonse.—2 Tim. 2:24; Aroma 12:18.