Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/05 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 7/05 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu July ndi August: Gawirani lililonse la mabulosha awa: Buku la Anthu Onse, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu, Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! September: Gawirani buku la Lambirani Mulungu Woona Yekha. Mipingo imene ili ndi mabuku kapena mabulosha ambiri akale ingathe kugawira amenewo. Tikukumbutsanso mipingo kumaitanitsiratu mabuku okwanira pasadakhale kaamba ka utumiki monga mmene amasonyezera mu Utumiki Wathu wa Ufumu uliwonse. October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kwa amene aonetsa chidwi, asonyezeni bulosha la Mulungu Amafunanji.

◼ Kuyambira mwezi wa September, oyang’anira madera azidzakamba nkhani ya onse ya mutu wakuti “N’chifukwa Chiyani Kuli Kofunika Kuti Baibulo Lizititsogolera?”

◼ Zimakhala bwino kutumiza mafomu a upainiya wokhazikika ku ofesi ya nthambi kutatsala masiku osachepera 30 tsiku loyamba upainiyawo lisanafike. Mlembi wa mpingo ayenera kuonetsetsa kuti zonse pa mafomuwo n’zolembedwa bwino. Ngati amene akufunsira utumikiwo sakukumbukira deti limene anabatizidwa, angoyerekeza detilo ndi kulisunga. Mlembi ayenera kulemba deti limeneli pa Khadi la Mpingo Lolembapo Ntchito za Wofalitsa (S-21).

◼ Alembi a mipingo ayenera kuonetsetsa kuti ali ndi Kalata Yotsimikiza Kuikidwa kwa Mpainiya (S-202) ya mpainiya aliyense wokhazikika amene ali mu mpingomo. Ngati alibe, chonde dziwitsani ofesi ya nthambi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena