Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/04 tsamba 7
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 6/04 tsamba 7

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira June 28, 2004. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya May 3 mpaka June 28, 2004. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]

LUSO LA KULANKHULA

1. Kodi pokamba nkhani papulatifomu ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kulankhula mwa njira imene timalankhulira ndi anthu? [be-CN tsa. 179 ndime 4]

2. Kodi n’chifukwa chiyani kukonza mawu anu kuti azimveka bwino si nkhani yongokhudza kupuma bwino ndiponso kumasula minofu yokungika? [be-CN tsa. 181 ndime 2]

3. Tikamauza anthu ena choonadi cha m’Baibulo, kodi ndi mfundo ziti zothandiza zimene tingatsatire kuti ‘tikhale zonse kwa anthu onse’? (1 Akor. 9:20-23) [be-CN tsa. 186 ndime 2-4]

4. Kodi kumvetsera mosamalitsa tikakhala mu utumiki kumaphatikizapo chiyani? [be-CN tsa. 186 ndime 5 mpaka tsa. 187 ndime 4]

5. Kodi n’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti aliyense amene timakumana naye mu utumiki tizim’patsa ulemu? [be-CN tsa. 190]

NKHANI NA. 1

6. Kodi cholinga cha anthu amene amaphunzitsa anthu malangizo ochokera kwa Mulungu n’chiyani, ndipo kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tikwanitse cholinga chimenechi? (Mat. 5:16; Yoh. 7:16-18) [be-CN tsa. 56 ndime 3 mpaka tsa. 57 ndime 2]

7. Kodi n’chifukwa chiyani kusiyanitsa zinthu kuli kothandiza pophunzitsa, ndipo kodi Yesu anagwiritsira ntchito njira yophunzitsa imeneyi motani? [be-CN tsa. 57 ndime 3; tsa 58 ndime 2]

8. Kodi zinkatheka bwanji kuti zimene Yesu ankaphunzitsa ziwafike anthu pamtima kusiyana ndi zimene Afarisi anali kuphunzitsa? [be-CN tsa. 59 ndime 2 ndi 3]

9. Kodi tingathandize bwanji anthu amene timawaphunzitsa kuti azisankha zochita mosachita kuwasankhira? [be-CN tsa. 60 ndime 1-3]

10. Kodi mafunso okhudza nkhani zofunika kuti munthu asankhe yekha zochita omwe anthu ena amafunsa tiyenera kuwayankha bwanji? [be-CN tsa. 69 ndime 4-5]

KUŴERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

11. N’chifukwa chiyani Mose anafunika kutsatira kamangidwe ka “chifaniziro cha kachisi, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse”? (Eks. 25:9) [it-2 tsa. 1058 ndime 7]

12. Kodi tingaphunzire chiyani malinga ndi mmene Aroni anayankhira Mose pankhani yokhudza mwana wa ng’ombe wa golide? (Eks. 32:24)

13. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Aisrayeli anachita zosonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro pomvera lamulo la Yehova limene lili pa Eksodo 34:23, 24?

14. Kodi cholinga cha nsembe yoyamika chinali chiyani? (Lev. 3:1)

15. Kodi dongosolo loika munthu paudindo limene Aroni anamuchitira, limenenso linalembedwa pa Levitiko 8:23 limaimira Yesu motani? [it-2 tsa. 1113 ndime 4; w68 tsa. 399 ndime 24]

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena