Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira December 29, 2003. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya November 3 mpaka December 29, 2003. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi n’chifukwa chiyani kuŵerenga Baibulo kuli kofunika kwambiri mu utumiki wa kumunda? [be-CN tsa. 145 ndime 2, bokosi]
2. Kodi zochitika za m’lemba zingakhudze bwanji njira yotchulira lembalo? [be-CN tsa. 149]
3. Kodi n’chifukwa chiyani kuli kofunika kutsindika mawu oyenerera poŵerenga lemba m’Baibulo, ndipo zimenezi zingachitidwe bwanji? [be-CN tsa. 151 ndime 2, bokosi]
4. Kodi tingatsatire motani uphungu wa Paulo ‘wolunjika nawo bwino mawu a choonadi’ pophunzitsa ena, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? (2 Tim. 2:15) [be-CN tsa. 153 ndime 2, bokosi]
5. Kodi Paulo anachita chiyani polingalira nawo omvera kuchokera m’Malemba? (Mac. 17:2, 3) [be-CN tsa. 155 ndime 5–tsa. 156 ndime 1]
NKHANI NA. 1
6. Pogwiritsa ntchito Baibulo monga chida chathu chachikulu chofufuzira, n’chifukwa chiyani zimathandiza (1) kupenda mbali zosiyanasiyana za lembalo, (2) kuŵerenga malemba owonjezera, ndi (3) kufufuza mwa kugwiritsa ntchito namlozera mawu wa Baibulo? [be-CN tsa. 34 ndime 3–tsa. 35 ndime 2]
7. Kodi kukhulupirika kwenikweni kumasonyezedwa motani ndipo kwa ndani? [w01-CN 10/1 mas. 22-3]
8. Kodi Mulungu wapereka chiyani kuti chititsogolere chomwe tingachifanizire ndi kompyuta youlutsira ndege zamakono zonyamula anthu? [w01-CN 11/1 mas. 3-4]
9. Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kukumbukira posankha mfundo zimene tigwiritse ntchito m’nkhani yathu pambuyo pofufuza? [be-CN tsa. 38]
10. N’chifukwa chiyani mawu a Yesu onena za “masiku a Nowa” akufanana kwambiri ndi mmene zinthu zilili masiku athu ano? (Mat. 24:37) [w01-CN 11/15 tsa. 31 ndime 3-4]
KUŴERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi kalata ya Paulo kwa Filemoni ikusonyeza bwanji kuti ntchito ya Akristu ndi kuthandiza anthu kukhala Akristu, osati kulimbikitsa kuti zinthu zisinthe m’dziko? (Filem. 12)
12. Kodi kusiyana kwake kwa ‘kutengeka,’ ‘kulekana,’ ndi ‘kugwa” n’kotani? (Aheb. 2:1; 3:12; 6:6) [w99-CN 7/15 tsa. 19 ndime 12; w86-CN 11/15 tsa. 14 ndime 16-17; w80 12/1 tsa. 23 ndime 8]
13. Kodi tingapeŵe bwanji kusukulutsa mawu akuti “akalola Mulungu”? (Yak. 4:15) [cj tsa. 171 ndime 1-2]
14. Kodi ‘kuyembekezera ndi kukumbukira nthaŵi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova’ kumatanthauza chiyani, ndipo tingachite motani zimenezi? (2 Pet. 3:12, NW) [w97-CN 9/1 mas. 19-20]
15. Kodi ndi uphungu wotani wofunika kwa Akristu masiku ano umene ukupezeka m’mauthenga opita ku mipingo isanu ndi iŵiri yotchulidwa m’Chivumbulutso chaputala 2 ndi 3? (Chiv. 2:4, 5, 10, 14, 20; 3:3, 10, 11, 17, 19)