Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira JUNE 30, 2003. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya MAY 5 mpaka JUNE 30, 2003. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
Luso la Kulankhula
1. Kodi n’chifukwa chiyani kusinthasintha mawu kuli kofunika mukamakamba nkhani, ndipo kodi ndi motani mmene mungachitire zimenezo? [be-CN tsa. 111 bokosi; tsa. 112 bokosi]
2. Kodi zimatheka bwanji kuti munthu wokonda Yehova amenenso amakhulupirira zimene akunena akhale wopola m’kalankhulidwe? [be-CN tsa. 115 ndime 3-4; tsa. 116 ndime 1]
3. Kodi n’chiyani chimene chingathandize wokamba nkhani kusonyeza mzimu waubwenzi ndiponso mmene akumvera, nanga n’chifukwa chiyani izi zili zofunika? [be-CN tsa. 119 ndime 1-4]
4. Kodi kulankhula mwaumoyo, mzimu waubwenzi ndi mitundu ina ya makhalidwe okhudza mtima imene mumasonyeza m’mawu anu imadalira kwambiri pa chiyani? [be-CN tsa. 120 ndime 2-5]
5. Zoona kapena Zabodza: Kugwiritsa ntchito manja ndi nkhope n’kofunika kokha pamene omvera anu akukuyang’anani. Fotokozani. [be-CN tsa. 121 ndime 3]
Nkhani Na. 1
6. Kodi n’chiyani chinamuthandiza Yosiya kusankha njira yabwino ngakhale kuti paubwana wake anakumana ndi zinthu zoipa zambiri? (2 Mbiri 34:1, 2) [w01-CN 4/15 tsa. 26 ndime 5 mpaka tsa. 27 ndime 5; tsa. 28 ndime 4]
7. Kodi Miyambo 9:7, 8a imatanthauza chiyani, ndipo zimenezi tingazigwiritse ntchito bwanji mu utumiki wakumunda? [w01-CN 5/15 tsa. 29 ndime 4-5]
8. Kodi Yehova anatanthauzanji pamene anauza Aisrayeli kuti, ‘Musamaiŵale,’ ndipo kodi tingapeŵe bwanji kuiŵala? (Deut. 4:9; 8:11) [be-CN tsa. 20 ndime 1-3]
9. Kodi ndi motani mmene mawu ochokera pansi pamtima a Davide amene ali pa Salmo 32:1, 5 ndi pa Salmo 51:10, 15 amasonyezera kuti munthu sayenera kudzimva ngati wopanda pake akachita tchimo lalikulu koma kenaka n’kulapa? [w01-CN 6/1 tsa. 30 ndime 1-3]
10. Kodi pa malangizo amene analemba Paulo pa 1 Timoteo 5:3-16 tingaphunzirepo chiyani chokhudza kusamalira osoŵa? [w01-CN 6/15 tsa. 11 ndime 1]
Kuŵerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu
11. Kodi Yesu amafotokoza za chiyani pamene anatchula mawu oti “kubadwanso” olembedwa pa Yohane 3:3? [w95-CN 7/1 mas. 9-10 ndime 4-5]
12. Kodi Yesu anagwiritsira ntchito maphunziro ake m’njira yotani, ndipo kodi ndi phunziro lofunika lotani limene tikutengapo pamenepa? (Yohane 7:15-18) [w96-CN 2/1 mas. 9-10 ndime 4-7]
13. Kodi n’chifukwa chiyani mawu a pa Yohane 7:53–8:11 anaikidwa padera m’malo mowaika limodzi ndi mawu a mavesi ena onse m’mabaibulo ena kuphatikizapo New World Translation?
14. Kodi Yesu ‘anadza momwemo’ monga mmene anapitira kumwamba m’njira yotani? (Machitidwe 1:11) [w90-CN 6/1 tsa. 11 ndime 5]
15. Kodi n’chifukwa chiyani “palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana [ndi ophunzirawo],” monga mmene amanenera Machitidwe 5:13?