Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira April 28, 2003. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya March 3 mpaka April 28, 2003. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingapangitse munthu kumadodomadodoma polankhula? [be-CN tsa. 93]
2. Zoona Kapena Zonama: M’pofunika kumapeŵa kupuma polankhula chifukwa chakuti kungapangitse maganizo a anthu kuyendayenda ndi kuwapatsa mwayi wotidula mawu. Fotokozani.
3. Kodi kutsindika ganizo moyenerera n’kwaphindu motani kwa wokamba nkhani kapena woŵerenga pamaso pa anthu? (Neh. 8:8) [be-CN tsa. 101]
4. Kodi munthu angapeze bwanji luso lotsindika ganizo moyenerera? [be-CN mas. 102-3]
5. Kodi ndi malingaliro ofunika kwambiri ati amene ayenera kutchulidwa motsindika poŵerenga paphunziro la Baibulo kapena pa msonkhano wa mpingo? [be-CN tsa. 105]
NKHANI NA. 1
6. Kodi makolo angachite chiyani pophunzitsa ana “kuti amve, ndi kuti aphunzire” pa misonkhano yachikristu? (Deut. 31:12) [be-CN tsa. 16]
7. Kodi paradaiso wauzimu n’chiyani? [w01-CN 3/1 mas. 8-10]
8. Kodi Miyambo 8:1-3 amasonyeza motani kuti munthu aliyense angapeze nzeru ya Mulungu ndipo mogwirizana ndi Akolose 2:3, kodi nzeru imeneyo ingapezeke kuti? [w01-CN 3/15 mas. 25, 28]
9. Kodi ena tingawadziŵitse bwanji dzina la Mulungu? (Yoh. 17:6) [be-CN mas. 273-5]
10. Kodi ndi mfundo zofunika ziti zomwe anthu afunika kuzidziŵa ponena za ‘uthenga wabwino wa Ufumu’? (Mat. 24:14) [be-CN mas. 279-80]
KUŴERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. (a) M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, kodi “chonyansa cha kupululutsa” chotchulidwa pa Marko 13:14 chinali chiyani? (b) Kodi ‘kuima kwake pomwe sichinayenera’ kunatanthauza chiyani?
12. Kodi Uthenga Wabwino wa Luka umasonyeza motani kuti Yesu anali woloŵa ufumu wa Davide mwachibadwa? (Luka 3:23-38) [w92-CN 10/1 tsa. 9 ndime 3]
13. Kodi mawu a Yesu omwe ali pa Luka 12:2 anali kutanthauza chiyani?
14. M’fanizo la Yesu la ndalama ya siliva yotayika, n’chifukwa chiyani zochita za angelo zili zochititsa chidwi? (Luka 15:10) Kodi chitsanzo chawo chiyenera kutikhudza motani?
15. Kodi Luka 22:29 akunena za mapangano aŵiri ati?