Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/01 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 11/01 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu November: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe mabuku ameneŵa, mungagaŵire mabuku aŵa, Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kapena Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. January: Buku lililonse la masamba 192 limene mpingo uli nalo, lofalitsidwa chaka cha 1987 chisanafike. February: Buku lililonse lakale la masamba 192 limene mpingo uli nalo.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wamusankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa December 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detili. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mukatha kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Mipingo iyambe kuoda buku la 2002 Yearbook of Jehovah’s Witnesses pamodzi ndi oda yawo yamabuku ya November. Mabuku a Yearbook adzakhalako mu Chingelezi ndi Chifalansa. Ma Yearbook adzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo kufikira pamene adzakhalapo ndi kutumizidwa. Mabuku a 2002 Yearbook ndi zinthu za oda yapadera, kutanthauza kuti mpingo ndiwo uyenera kuoda mabuku ameneŵa ngati pali anthu amene akuwafuna; mtumiki wa mabuku sangaodere mpingo mulu wa mabuku ameneŵa abale ndi alongo asananene kuti akuwafuna. Chotero afunika kusunga mosamala zimene wofalitsa aliyense waitanitsa. Mitu ya mabanja ingaone kuti buku limodzi pabanja lililonse n’lokwanira.

◼ Ofesi ya nthambi siimalembera wofalitsa oda ya mabuku amene akufuna. Woyang’anira wotsogolera azilengeza mwezi uliwonse asanatumize kunthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo kuti onse amene akufuna mabuku auze mbale wosamalira mabuku. Chonde, kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera.

◼ Mipingo iyenera kuitanitsa timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso cha chaka chamaŵa pa fomu yotsatira Yofunsira Mabuku (S-14). Alipo mu Chicheŵa, Chifalansa, Chingelezi ndi Chitumbuka. Itanitsani timapepalati m’magulu a timapepala 100 pa chinenero chilichonse. Chonde itanitsani mapepalaŵa mwanzeru popeza anapangira anthu achidwi okha, osati kuti azigaŵidwa wambawamba.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena