Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/01 tsamba 1
  • Dalirani Yehova Kuti Akupatseni Mphamvu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dalirani Yehova Kuti Akupatseni Mphamvu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amapereka Mphamvu kwa Wotopa
    Nsanja ya Olonda—2000
  • “Funani Yehova, ndi Mphamvu Yake”
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Yehova “Adzakulimbitsani”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Yehova Amatipatsa Mphamvu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 11/01 tsamba 1

Dalirani Yehova Kuti Akupatseni Mphamvu

1 Pali zifukwa zambiri zodalirira Yehova. Kulalikira uthenga wabwino “padziko lonse lapansi” si ntchito yamaseŵera. (Mat. 24:14) Nthaŵi zonse, timalimbana ndi thupi lathu lopanda ungwiroli. (Aroma 7:21-23) Komanso, ‘tili nako kulimbana ndi olamulira [amphamvu zoposa za anthu] a dziko la mdima lino.’ (Aef. 6:11, 12) Indedi, tifunika thandizo. Kodi tingapeze motani mphamvu kwa Yehova?

2 Mwa Kupemphera: Yehova amapereka mosaumira mzimu wake woyera wamphamvu kwa atumiki ake amene amam’pempha. (Luka 11:13) Kodi mumaganiza kuti simungathe kulalikira kunyumba ndi nyumba, mumsewu, kapena patelefoni? Kodi mumaopa kulalikira mwamwayi? Kodi kupanda chidwi kwa anthu a m’gawo lanu kwachepetsa changu chanu? Bwanji ngati mukukakamizidwa kusiya chikhulupiriro chanu kapena kukhulupirika kwanu? Dalirani Yehova. Pemphani mphamvu.—Afil. 4:13.

3 Mwa Phunziro Laumwini: Monga momwe timapezera mphamvu mwa kudya chakudya, momwemonso timalimbikitsidwa mwauzimu mwa kudya Mawu a Mulungu ndi zofalitsa za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” nthaŵi zonse. (Mat. 4:4; 24:45) Stanley Jones atafunsidwa komwe anapeza mphamvu kuti apirire zaka zimene anakhala m’ndende ya yekha ku China wopanda Baibulo, anati: “Tingalimbe m’chikhulupiriro. Inde, n’zoona kuti tiyenera kuphunzira kaye. Popanda kuphunzira sitingakhale ndi maganizo a mphamvu.”

4 Mwa Kupezeka Pamisonkhano: Yuda ndi Sila pamisonkhano yachikristu m’zaka za zana loyamba, “anasangalatsa abale ndi mawu ambiri, nawalimbikitsa.” (Mac. 15:32) Chimodzimodzinso lerolino, zimene timamva pamisonkhano zimawonjezera kuyamikira kwathu Yehova, zimalimbikitsa chikhulupiriro chathu ndi kutisonkhezera mu utumiki. Misonkhano imatipangitsa kuti nthaŵi zonse tizipezeka pamodzi ndi ‘antchito anzathu a mu Ufumu wa Mulungu,’ omwe ndi ‘chotonthoza mtima’ wathu.—Akol. 4:11.

5 Tifunika thandizo ‘m’nthaŵi zoŵaŵitsa’ zino. (2 Tim. 3:1) Amene amapeza mphamvu kwa Yehova, ndi otsimikiza kuti: “Adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.”—Yes. 40:31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena