Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi paulendo wobwereza, mungawalembetsere magazini. Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji n’cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba. June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha amasamba 32 aŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndiponso “Taonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Mabulosha a Buku la Anthu Onse, ndiponso Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, mungawagaŵire pamene kuli koyenera kutero.
◼ Kuyambira mwezi wa April uno, mabaji a msonkhano wachigawo wa 2001 a Chicheŵa, Chingelezi ndi Chitumbuka adzatumizidwa pamodzi ndi mabuku. Simufunika kuoda mabajiwa. Mabaji adzaikidwa m’mipukutu ya mabaji 25, malinga ndi kukula kwa mpingo uliwonse. Ngati mipingo ikufuna mabaji ena, iyenera kuoda pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). N’kofunika kuoda mapulasitiki oikamo mabaji ngati pali amene akuwafuna mu mpingomo.
◼ Pa “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2001” nkhani Na. 3 ndi Na. 4 zatengedwa m’buku la Kukambitsirana pamasamba ndiponso ndime zimene asonyezazo. Poŵerenga ndime m’bukuli, muziŵerenga zimene zayambira mkati zokha.
◼ N’koyenera Sosaite kusunga maadiresi ndi manambala afoni amene akugwira ntchito a oyang’anira otsogolera ndi alembi onse. Nthaŵi iliyonse zimenezi zikasintha, mlembi azitumiza msanga ku Sosaite fomu ya Kusintha Keyala ya Woyang’anira Wotsogoza/Mlembi (S-29).
◼ Alembi a mipingo ayenera kusunga mafomu okwanira a Chofunsirapo Utumiki Waupainiya Wokhazikika (S-205) ndi Chofunsirapo Utumiki Wothandiza (S-205b). Angaode zimenezi pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Sungani zokwanira chaka chimodzi. Pendani mafomu a ofunsira upainiya wokhazikika kuti mutsimikizire kuti alembedwa bwino. Ngati wofunsirayo sakukumbukira tsiku limene anabatizidwa, ayenera kungoyerekeza tsikulo ndiyeno asunge limenelo.
◼ Tikusindikiza buku la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 1 la zilembo zikuluzikulu kuti tithandize anthu amene ali ndi vuto la maso. Buku langati magazinili lidzakhala lachikuto chofeŵa chapepala, lamasamba 512, lopanda zithunzi ndi la zilembo zazikulu ngati za mu Nsanja ya Olonda ya nkhani ziŵiri zophunzira. Pakalipano tikupanga la Chingelezi basi. Tidzalengeza tikayamba kupanga m’zinenero zina. Izi zingaphatikizidwe pa fomu yofunsira mabuku mwa kulemba kuti Isaiah’s Prophesy 1—Large Print.
◼ Kuyambira mlungu wa July 30, 2001, tiziphunzira buku la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 1 pa Phunziro la Buku la Mpingo.
◼ Ngati mukukonza zopita kudziko lina ndipo mukufuna kukapezeka pamisonkhano ya mpingo, msonkhano wadera, kapena msonkhano wachigawo, funsani zokhudza masiku, nthaŵi, ndi malo ake ku ofesi ya nthambi imene imayang’anira ntchito m’dziko limenelo. Maadiresi a maofesi a nthambi ali patsamba lomaliza la Yearbook yatsopano.
◼ Posachedwa mipingo ilandira mafomu awo apachaka. Chaka chino mafomu a S-48 ndi S-89 titumizira pamodzi. Tachita zimenezi chifukwa taona kuti mipingo yonse sigwiritsa ntchito mafomuwa kaŵirikaŵiri. Choncho, tikukhulupirira kuti chaka chino popeza mipingo yonse ilandira mafomuwa, iyamba kuwagwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri. Ngati muli ndi mafunso a mmene mungawagwiritsire ntchito, funsani woyang’anira dera. Komabe, dziŵani kuti mafomuwa tingotumiza chaka chino chokha. M’tsogolomu, mipingo iyenera kuitanitsa mafomuwa pa Fomu Yofunsira Mabuku ya S-14. Mukhoza kuitanitsa mafomuwa nthaŵi ina iliyonse imene mukuwafuna. Tikulimbikitsa onse kuti aziona mafomu awo kaŵirikaŵiri kuti azidziŵa ngati akufunika kuwonjezera ena. Ayenera kuitanitsa mafomu awo asanatheretu.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:
Mipingo iyenera kuyamba kuoda mabaundi voluyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a chaka cha 2000. Mabaundi voliyumuwa adzakhalamo m’Chingelezi. Mpaka pamene adzakhalapo ndi kutumizidwa, adzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo.
(Zapitirizidwa pa tsa. 7, danga 1 )
Zilengezo (Zachokera pa tsa. 2 )