Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tiyenera kuyesetsa kwambiri kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April ndi May: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Khalani ndi bulosha la Mulungu Amafunanji kaamba ka anthu ochita chidwi, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Ofalitsa omwe akufuna kuchita upainiya wothandiza m’April ndi m’May ayenera kuyamba kukonzekera pakalipano ndipo ayenera kupereka mafomu awo mwamsanga. Zimenezi zidzathandiza akulu kupanga makonzedwe ofunikira a utumiki wakumunda ndi kupeza magazini ndi mabuku ena okwanira. Mayina a anthu omwe avomerezedwa kukhala apainiya othandiza ayenera kulengezedwa kumpingo mwezi uliwonse.
◼ Kope lino la Utumiki Wathu wa Ufumu lili ndi ndandanda yonse ya maphunziro a buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Mukhoza kuchititsa fotokope ndandandayi ndi kuiika m’buku lanu kuti musamavutike kuona.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa March 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detilo. Mutatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo pambuyo popereka lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Chikumbutso chidzakhalako Lachitatu, pa April 19, 2000. Ngati mpingo wanu nthaŵi zonse umachita misonkhano Lachitatu, muyenera kuisinthira tsiku lina mlungu womwewo ngati Nyumba ya Ufumu idzakhale isakugwiritsidwa ntchito. Ngati zimenezi zili zosatheka ndipo Msonkhano wa Utumiki wanu wakhudzidwa, mbali zomwe zili zofunika kwambiri pampingo wanu zingaphatikizidwe mu Msonkhano wa Utumiki wotsatirawo.
◼ Omwe akugwirizana ndi mpingo ayenera kutumiza masabusikiripishoni onse atsopano ndi ofuna kulembetsanso a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kuphatikizapo masabusikiripishoni awoawo, kudzera kumpingo.
◼ Sosaite sikonzera wofalitsa aliyense payenkha oda ya mabuku. Woyang’anira wotsogolera ayenera kukonza chilengezo chimene chiyenera kuperekedwa mwezi uliwonse asanatumize ku Sosaite oda ya mabuku ampingo ya mwezi ndi mwezi kuti onse amene akufuna kukhala ndi mabuku awoawo adziŵitse mbale wosamalira mabuku. Chonde kumbukirani mabuku amene ali pa oda yapadera.
(Zapitirizidwa pa tsa. 8, danga 3)
Zilengezo(Zapitirizidwa)