Mbiri Yateokalase
◼ Albania: Chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 1,556 amene anapereka malipoti m’January chikusonyeza kuti chaposa chiŵerengero cha avareji ya chaka chatha ndi 20 peresenti.
◼ Belau: Chiŵerengero cha December cha ofalitsa 73 chinaposa chiŵerengero cha chaka chatha ndi 20 peresenti ndipo chinaposa chiŵerengero cha m’December wa chaka china cham’buyomo ndi 22 peresenti.
◼ Canada: Pa January 1, 1999, apainiya okhazikika atsopano 460 anaikidwa.
◼ United States: Sosaite inakhazikitsa makomiti osamalira za masoka kuti apereka thandizo kumwera kwa United States kumene zinthu zinawonongeka ndi mikuntho. Izi zinaphatikizapo komwe kunasefukira madzi ku Texas ndi ku Florida Keys komwe mphepo ya Hurricane Georges inawononga zinthu. Oyandikana nawo anadabwa kwambiri ndi njira imene Sosaite inathandizira abale ndi mmene ntchito yopereka thandizoyo inachitikira.