Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu July: Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe kapena lililonse la mabrosha otsatirawa a masamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” August ndi September: Mkupiti wapadera wa buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi pamitengo yotsika. (K18.00 ofalitsa a mpingo ndi onse, K12.00 apainiya pa lalikulu; K9.00 ofalitsa a mpingo ndi onse, K6.00 apainiya pa laling’ono.) October: Masabusikripishoni a Galamukani! kapena Nsanja ya Olonda. Pangani kuyesayesa kwamphamvu kuti mugaŵire makope a magazini ameneŵa. Masabusikripishoni angagaŵiridwe pamaulendo obwereza. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene sinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambazo iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Request (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi.
◼ Sosaite ikupanga mabaundi voliyumu ACHINGELEZI a Nsanja ya Olonda a zaka za 1951 mpaka 1959. Ofalitsa atsopano alionse kapena mipingo yatsopano imene ikufuna zofalitsa zimenezi ingaziode kupyolera mumpingo. Zinthu zimenezi sizidzakhaliratu m’sitoko ya Sosaite. Mabaundi voliyumu ali zinthu zoodedwa mwapadera ndipo mipingo siiyenera kuwasunga m’sitoko.
◼ Mkupiti Wapadera wa July: Mipingo inauzidwa m’kalata kuti m’mwezi wa July tidzakhala pamkupiti wapadera wogaŵira buku lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Pangani makonzedwe tsopano a kukhala ndi phande lokwanira m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba mkati mwa mkupitiwo. Mipingo yonse iyenera kufola gawo lawo monga momwe angakhozere ndi chothandiza kuphunzira Baibulo chapadera chimenechi. Khalani wachisangalalo pogaŵira bukulo. Popeza kuti uwu udzakhala mkupiti wapadera, perekani chisamaliro choyamba pa chogaŵira chake m’malo mwa zinazo. Pamene sichilandiridwa, yesani kugaŵira mabrosha ena. Mitengo yotsika ya K4.50 apainiya ndi K6.00 mpingo ndi onse ingakhalenso yosonkhezera kwa ofalitsa ndi ena onse. Konzekerani bwino lomwe mkupitiwo ndipo tsimikizani mtima za kudzakhala ndi phande lokwanira m’kugaŵira buku la Moyo wa Banja ndi kuthandiza ambiri kukhala ndi moyo wa banja wabwinopo.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe—Chicheŵa, Chingelezi
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi (lalikulu)—Chicheŵa, Chingelezi
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi (laling’ono)—Chicheŵa, Chingelezi